bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 3
Job 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 4 →
1
Pambuyo pake Yobe adalankhula, nayamba kutemberera tsiku lake lobadwa.
2
Adati,
3
“Tsiku limene ine ndidabadwa litembereredwe, nawonso usiku umene mai wanga adatenga pathupi pa ine utembereredwe.
4
Tsiku limenelo lisanduke lamdima. Mulungu kumwambako asaliganizirenso tsiku limenelo, kuŵala kusadzaonekenso pa tsikulo.
5
Tsikulo likhale la mdima wabii, likhale lamikhwithi, mdima wake ukhale woopsa.
6
Usiku umenewo ukhale wa mdima wandiweyani. Tsiku limenelo lisakhalenso pamodzi ndi masiku a pa chaka, lisaŵerengedwerenso kumodzi ndi masiku a pa miyezi.
7
Ndithu usiku umenewo usabweretsenso chabwino chilichonse, kusamvekeponso nthungulu zachikondwerero usikuwo.
8
Odziŵa kutemberera masiku, alitemberere tsikulo, ndiye kuti odziŵa kuutsa Leviyatani, chilombo cham'nyanja chija.
9
Nyenyezi zake zambandakucha zisaŵale. Tsikulo liyembekeze kucha, koma pachabe. Lisaonenso kuŵala kwa mbandakucha.
10
Tsiku limenelo litembereredwe, chifukwa ndi limene ndidatuluka m'mimba mwa mai wanga, ndipo ndi limene lidandiwonetsa zovuta.
11
“Bwanji sindidangobadwa wofaifa! Bwanji sindidangoti badwu nkufa!
12
Chifukwa chiyani mai wanga adandifukata? Chifukwa chiyani adandiyamwitsa?
13
Ndikadafa pobadwa pomwe, bwenzi ndikukhala nditagona mwaphee, kungogona tulo, ndi kumangopumula.
14
Bwenzi ndikukhala limodzi ndi mafumu ndi aphungu a pa dziko lapansi, amene adadzimangira nyumba zikuluzikulu pa mabwinja akale.
15
Bwenzi ndikukhala limodzi ndi mafumu okhuphuka, amene adadzaza nyumba zao ndi golide ndi siliva.
16
Bwenzi sindidangokhala ngati mtayo woikidwa m'manda, ngati makanda amene sadaonepo kuŵala kwa dzuŵa.
17
Kumandako anthu oipa savutitsanso, anthu otopa akupumula kumeneko.
18
Am'ndende akupeza nawo mtendere kumeneko, sakumvanso mau ankhanza a kapitao wa ndende.
19
Anthu wamba ndi apamwamba omwe ali pamodzi kumeneko, kapolo ndi womasuka kwa mbuyake.
20
“Chifukwa chiyani dzuŵa limamuŵalira munthu wapamavuto? Chifukwa chiyani amakhalabe ndi moyo munthu wa mtima woŵaŵa?
21
Amalakalaka imfa, koma osaiwona, amaifunafuna kupambana chuma chobisika.
22
Amakondwa ndi kusangalala kwambiri akafa ndi kuikidwa m'manda.
23
Chifukwa chiyani moyo umapatsidwa kwa munthu amene njira ya moyo wake yabisika, amene Mulungu wamzinga ndi mavuto ponseponse?
24
M'malo moti ndidye, ndimalira, ndipo kubuula kwanga nkosalekeza.
25
Zimene ndinkaziwopa zachitika ndithu, zimene ndinkachita nazo mantha zandigweradi.
26
Ine sindipeza mtendere kapena bata, sindiwona mpumulo, koma mavuto okhaokha.”
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42