bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 22
Job 22
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 23 →
1
Tsono Elifazi wa ku Temani adayankha kuti,
2
“Kodi munthu nkukhala waphindu kwa Mulungu? Iyai, munthu wanzeru amangodzipindulira yekha basi.
3
Kodi Mphambe angapeze bwino chifukwa cha kulungama kwako? Kodi kapena Iyeyo nkupindulapo kanthu pa makhalidwe ako angwirowo?
4
Kodi nchifukwa choti umamuwopa, kuti azikudzudzula, kuti azifuna kukukokera ku mlandu?
5
Kodi osati nchifukwa choti kuipa kwako nkwakukulu, ndipo kulakwa kwako nkopanda malire?
6
“Iwe unkaumiriza pachabe abale ako kuti apereke chikole, ndipo unkaŵalanda zovala zao, mpaka kuŵasiya ali ndi usiŵa.
7
Anthu otopa sudaŵapatse madzi akumwa, anthu anjala udaŵamana chakudya.
8
Chifukwa cha mphamvu zako udalanda dziko lalikulu, chifukwa cha kudzikonda udakhazikika m'menemo.
9
Akazi amasiye udaŵachotsa opanda kanthu, ndipo ana amasiye udaŵapondereza.
10
Nchifukwa chake misamphayi yakuzinga, ndipo wadzidzimuka ndi mantha.
11
Kuli mdima ndipo sungathe kuwona kanthu, madzi achigumula akukumiza.
12
“Kodi Mulungu sali kutalitali kumwamba? Ona nyenyezi zili m'mwamba kwambirizo, ona kutalika kwake pamene ziliripo!
13
Komabe umanena kuti, ‘Kodi Mulungu amadziŵa chiyani? Wabisika ndi mitambo, nanga angatiweruze bwanji?
14
Mitambo yakuda yamzinga, kotero kuti sangathe kuwona bwino, pamene akuyenda pamwamba pa thambopo.’
15
“Kodi iwe ukufuna kuyendabe m'njira yakale imene anthu oipa ankayendamo?
16
Iwowo adachotsedwa nthaŵi yao isanakwane, maziko ao adakokoloka ndi madzi.
17
Anthuwo ankauza Mulungu kuti, ‘Chokani pali ife pano!’ Adatinso, ‘Kodi Mphambeyo nkutichita chiyani ife?’
18
Chonsecho ndi Mulungu amene adaŵalemeretsa ndi zinthu zokoma. Nchifukwa chake ine ndekha ndiye maganizo a anthu oipa sindigwirizana nawo.
19
Anthu abwino amaona zonse ndi kukondwa, anthu osachimwa amangoseka, akamaona oipa akulangidwa.
20
Amanena kuti, ‘Ndithudi, adani athu aonongedwa, zimene adazisiya zaonongeka ndi moto.’
21
“Iwe Yobe, uziyanjana ndi Mulungu kuti ukhale pa mtendere, ukatero udzaona zabwino.
22
Uzimvera malangizo amene Iyeyo amaphunzitsa, uziikapo mtima pa mau ake.
23
Ubwerere kwa Mphambe modzichepetsa, uchotse zosalungama zonse zimene zimachitika m'nyumba mwako.
24
Golide wako yense umuyese wachabechabe, ndithu, chuma chamtengowapatali uchiwone ngati dothi,
25
Koma Mphambe ndiye akhale ngati golide wako, akhale ngati siliva wako wamtengowapatali.
26
Ukatero udzakondwa naye Mphambe, Udzaikapo mtima pa Mulungu mwamtendere.
27
Ukadzapemphera kwa Iye adzakumvera, udzapereka kwa Iye zija udalumbira kuti udzaperekazi.
28
Chimene wachitsimikiza kuti udzachite, chidzachitikadi, kuŵala kudzakuunikira pa njira zako zonse.
29
Pajatu Mulungu amagwetsa onyada, koma amapulumutsa odzichepetsa.
30
Amapulumutsa munthu wopanda mlandu, adzakupulumutsa iwenso ndi kulungama kwako.” Yobe
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42