bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 19
Job 19
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 20 →
1
Tsono Yobe adayankha kuti,
2
“Kodi mudzakhala mukundizunzabe mpaka liti? Chifukwa chiyani mukundilasa ndi mau anu?
3
Mwakhala mukundinyoza kambirimbiri, Bwanji osachita manyazi kuti mukundisautsa?
4
Ngakhale zitakhala zoona kuti ndachimwa, kuchimwakotu nkwanga.
5
Ndithudi, mukuganiza kuti mukundipambana. Mukuti mavuto angaŵa akusonyeza kuchimwa kwanga.
6
Koma tsono mudziwe kuti Mulungu ndiye wandichita zimenezi, ndiye amene wanditchera msampha umenewu.
7
Ndithu, ndimafuula kuti, ‘Mayo, akundizunza ine!’ Koma palibe wondiyankha. Ndimapempha chithandizo, koma palibe wondichitira zolungama.
8
“Mulungu wanditsekera njira, kotero kuti sindingathe kubzola. Njira yangayo waiphimba ndi mdima.
9
Iye wandilanda ulemerero wanga, wandivula chisoti chaulemu.
10
Wandiphwanyaphwanya mbali zonse, ndipo ndatheratu. Wandilanda chikhulupiriro changa, monga momwe amazulira mtengo.
11
Mulungu wandikwiyira, akundiyesa ngati mdani wake.
12
Watumiza ankhondo ake ochuluka kuti adzalimbane nane. Akonzekeratu zodzandithira nkhondo pafupi ndi nyumba yanga.
13
“Mulungu waumiriza abale anga kuti andikane. Wasandutsa odziŵana nane kuti akhale achilendo kwa ine.
14
Achibale anga andithaŵa. Abwenzi anga anditaya.
15
Anthu odzacheza kunyumba kwanga andiiŵala, Antchito anga nawonso sakundilemekeza, ndasanduka ngati wakudza m'maso mwao.
16
Ndikaitana wantchito, sandiyankha, ndimachita kupemba kuti andichitire kanthu.
17
Ngakhale mkazi wanga yemwe amaipidwa nane. Ndine chinthu chonyansa kwa abale anga a mimba imodzi.
18
Ngakhale ana omwe amandinyoza, ndikamayenda amandinyodola.
19
Abwenzi anga onse apamtima amanyansidwa nane, amene ndinkaŵakonda kwambiri andiwukira.
20
“Ndangoti gwa kuwonda, moyo wanga wapulumukira pang'onong'ono.
21
Mvereni chifundo, chonde mvereni chifundo, inu abwenzi anganu, poti dzanja la Mulungu landikantha.
22
Chifukwa chiyani mukundilondola ndinu ngati Mulungu? Kodi simudandizunze kokwanira?
23
“Ha, achikhala ena adaakumbukira mau anga! Ha, achikhala mauwo adaalembedwa m'buku!
24
Achikhala mauwo adaazokotedwa pa thanthwe ndi chitsulo, ndi kuthirapo mtovu kuti akhale mpaka muyaya!
25
“Mtheradi ndikudziŵa kuti Momboli wanga alipo, ndipo pa nthaŵi yomaliza adzabwera kudzanditeteza.
26
Khungu langa litatha nkuwonongeka, m'thupi langa lomweli ndidzamuwona Mulungu.
27
Ine ndemwe ndidzamuwona, osati winanso ai. Ndidzamuwona ndi maso angaŵa. Mtima wanga ukulifunitsitsa tsikulo.
28
Koma inu mukuti, ‘Ha, tingamzunze bwanji, popeza kuti zovuta zonsezi zaoneka chifukwa cha iye yemweyo?’
29
Inu muwope chilango, chifukwa ukali wa Mulungu umalangadi mosalephera. Motero mudzadziŵa kuti chiweruzo chilipo ndithu.” Zofari
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42