bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 24
Job 24
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 25 →
1
“Chifukwa chiyani Mphambe saikiratu nthaŵi yoti aweruze? Chifukwa chiyani amene ali olungama saŵaona masiku otero?
2
Anthu ena amasendeza malire, kuti akuze dziko lao, amalanda ziŵeto namakazidyetsa ku mabusa ao.
3
Amalanda abulu a ana amasiye, amalandanso ng'ombe za akazi amasiye, kuti zikhale chikole.
4
Amapatutsa anthu osauka m'miseu, ndipo amapirikitsa amphaŵi onse.
5
Amphaŵiwo amakafunafuna chakudya ku chipululu ngati mbidzi. Kulibe kwina koti apezere ana ao chakudya.
6
Amakolola za m'minda ya eniake, amakunkha mphesa m'minda ya anthu oipa.
7
Amagona maliseche usiku wonse, pa nthaŵi yozizira amasoŵa chofunda.
8
Amavumbwa ndi mvula yakumapiri, amakangamira ku thanthwe chifukwa chosoŵa pousa.
9
Palinso ena amene amatsomphola ana a masiye ku bele, ndipo amagwira ana a mmphaŵi kuti akhale chikole.
10
Amphaŵi amangoyenda maliseche kusoŵa chovala, amasenza mitolo ya tirigu ali ndi njala.
11
Amayenga mafuta a olivi m'minda ya anthu oipa, namapsinya mphesa, koma nkumamvabe ludzu.
12
Anthu amene alikufa akubuula mumzindamo, anthu ovulala akulirira chithandizo. Komabe Mulungu sakusamalako mapemphero ao.
13
“Pali ena amene amakana kuŵala, safuna kuyenda m'kuŵalako, ndipo sadziŵa njira zake.
14
Wopha anzake amadzuka usiku kuti aphe osauka ndi amphaŵi. Nthaŵi ya usiku ena amasanduka mbala.
15
Munthu wachigololo amadikira chisisira, namanena kuti, ‘Palibe woti angandiwone,’ ndipo amadzizimbaitsa nkhope.
16
Mbala zimathyola nyumba usiku, masana zimadzitsekera, ndiye kuti zimapewa kuŵala.
17
Onsewo kukada kwambiri, ndiye kuti kwaŵachera. Zoopsa za mdima woti goo ndiye bwenzi lao.
18
“Munthu woipa amatengedwa ndi madzi a chigumula. Minda yake njotembereredwa m'dziko lonse. Sapitako kukagwira ntchito ku minda yake yamphesa.
19
Monga momwe amasungunukira matalala nkuloŵa pansi chifukwa cha fundira, ndimo m'mene munthu wochimwa adzatsikire ku dziko la akufa.
20
Ngakhale mai wake adzamuiŵala, koma mphutsi zidzasangalala pomudya. Momwemonso woipayo adzathyoka ngati mtengo.
21
“Zidzatero chifukwa choti adaŵachita nkhanza akazi amasiye, akazi opanda ana sadaŵachite zabwino.
22
Koma Mulungu amaononga anthu amphamvu. Anthuwo ngakhale atakhazikika, moyo wao ndi wosatsimikizika.
23
Mulungu angathe kumtchinjiriza munthu woipa ndi kumpatsa mtendere, koma amakhala akupenyetsetsa njira zake.
24
Woipayo amamkweza pa kanthaŵi kochepa, koma posachedwa saonekanso. Monga ena onse nayenso amafota ngati udzu, amagwa ngati ngala za tirigu akazidula.
25
Ndani angathe kukana kuti si momwemo? Kodi wina anganditsutse kuti mau angaŵa si oona?” Bilidadi
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42