bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 29
Job 29
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 30 →
1
Yobe adapitiriza nati,
2
“Ha, ndikadabwerera mwakale monga m'mene ndinkakhalira pa nthaŵi yamakedzana, pa masiku amene Mulungu ankandisunga bwino.
3
Nthaŵi imeneyo Mulungu anali nane, nyale yake inkandiwunikira mu mdima.
4
Masiku amenewo ndinali pabwino zedi, madalitso a Mulungu anali pabanja panga.
5
Nthaŵi imeneyo Mphambe anali nane, ana anga ali kwete m'mbalimu.
6
Nthaŵi imeneyo ng'ombe ndi mbuzi zanga zinkandipatsa mkaka wambiri, mitengo yanga ya olivi inkamera ndi m'matanthwe momwe.
7
Pamene ndinkapita ku chipata cha mzinda, pamene ndinkakonzekera zokakhala nawo pabwalopo,
8
anyamata akandiwona ankapatuka, ndipo madoda ankadzambatuka nkukhala chilili.
9
Akalonga ankakhala chete, atangoti pakamwa gwirire.
10
Atsogoleri ankangoti duu, lilime litangoti nganganga ku nkhama.
11
Aliyense womva za ine, ankanditchula kuti ndine wodala, aliyense wondiwona ankandilemekeza.
12
Zidatero chifukwa choti ndinkapulumutsa amphaŵi olira, ndinkalanditsa ana amasiye opanda woŵathandiza.
13
Anthu amene anali pa zoopsa kwambiri ankanditamanda, akazi amasiye ndinkaŵasangalatsa.
14
Nthaŵi zonse ndinkachita zoyenera, ntchito zanga zonse zinali zangwiro.
15
Ndinali ngati maso kwa anthu osapenya, ndinali ngati mapazi kwa anthu opunduka.
16
Osauka ndinali ngati bambo wao, anthu osaŵadziŵa konse ndinali mtetezi wao pa milandu.
17
Ndinkaononga mphamvu za anthu ankhalwe, ndinkalanditsa amene anali atagwidwa.
18
“Tsono mumtimamu ndinkati, ‘Ndidzafera pakati pa ana anga, masiku a moyo wanga ndidzaŵachulukitsa kwambiri ngati mchenga.
19
Ndinali ngati mtengo umene mizu yake yatambalalira ku madzi umene masamba ake ndi onyowa ndi mame.
20
Aliyense ankandilemekeza, nthaŵi zonse mphamvu zanga zinali ngati uta wolimba.’
21
“Anthu ankamvetsera zimene ndinkanena, ankadikira atakhala chete kuti amve malangizo anga.
22
Ine nditalankhula, iwowo sankalankhulanso, mau anga ankaŵagwira mtima.
23
Ankayembekeza ine monga momwe amayembekezera mvula, ankangoti kukamwa yasa ngati anthu odikira mvula yam'malimwe.
24
Ndinkaŵasekerera pamene iwowo analibenso chikhulupiriro, kukoma mtima kwanga kunkaŵalimbitsa mtima.
25
Ndinkasankhula njira yao, ndipo ndinkaŵatsogolera ngati mfumu, tsono ndidakhazikika pakati pao, ngati mfumu pakati pa ankhondo ake, ndinali ngati msangalatsi pakati pa olira.”
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 30 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42