bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 42
Job 42
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 41
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
1
Tsono Yobe adayankha Chauta kuti,
2
“Ndikudziŵa kuti Inu mungathe kuchita zinthu zonse, chimene mufuna kuchita, wina sangaletse konse.
3
Munandifunsa bwino kuti, ‘Kodi ndiwe yani amene ufuna kusokoneza uphungu wanga ndi mau opanda nzeru?’ Zoonadi ndidalankhula zimene sindidazidziŵe, zinthu zodabwitsa kwa ine zimene sindidazimvetse konse.
4
Munandiwuza kuti, ‘Umvetsetse ndipo ndidzalankhula. Ndidzakufunsa, ndipo iweyo undiyankhe.’
5
Ndinkangomva za inu ndi makutu, koma tsopano ndakuwonani chamaso.
6
Nchifukwa chake ndikuchita manyazi ndi zonse zimene ndidakamba, ndikulapa podzithira fumbi ndi phulusa.” Mulungu adalitsanso Yobe.
7
Chauta atalankhula ndi Yobe mau ameneŵa, adauza Elifazi wa ku Temani kuti, “Ine ndakukwiyira kwambiri pamodzi ndi abwenzi ako aŵiri, chifukwa simudalankhule zabwino za Ine, monga m'mene walankhulira mtumiki wanga Yobe.
8
Nchifukwa chake tsopano mutenge ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri, mupite nazo kwa mtumiki wanga Yobe, mukaperekere nsembe zopsereza. Tsono mtumiki wangayo adzakupemphererani, pakuti pemphero lakelo ndidzalilandira kuti ndisakuchiteni kanthu potsata kupusa kwanu. Inu simudalankhule zabwino za Ine, monga adalankhulira Yobe mtumiki wanga.”
9
Motero Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Suki ndi Zofari wa ku Naama adapita, nakachita zimene Chauta adaŵauza. Ndipo Chauta adamveradi pemphero la Yobe.
10
Choncho Yobe ataŵapempherera abwenzi ake aja, Chauta adambwezera chuma chake. Adampatsa moŵirikiza kuposa zimene adaali nazo kale.
11
Tsono abale ake onse ndi alongo ake omwe, kuphatikizapo onse amene ankamdziŵa kale, adabwera kwa iye nkudzadya naye chakudya m'nyumba mwake. Choncho adampepesa, namuthuzitsa mtima chifukwa cha mavuto onse amene Chauta adaalola kuti amgwere. Tsono aliyense mwa iwowo adampatsa ndalama ndi mphete yagolide.
12
Motero Chauta adadalitsa Yobe pa masiku ake otsirizaŵa kupambana poyamba paja. Tsono adakhala ndi nkhosa 14,000, ngamira 6,000, ng'ombe 2,000, ndi abulu aakazi 1,000.
13
Adabalanso ana aamuna asanu ndi aŵiri ndi ana aakazi atatu.
14
Wamkulu mwa ana aakazi aja adamutcha Yemima. Wachiŵiri anali Keziya, wachitatu anali Kerehapuki.
15
M'dziko monsemo munalibe akazi okongola ngati ana a Yobe. Bambo wao adaŵapatsa choloŵa chimodzimodzi ngati alongo ao.
16
Pambuyo pake Yobe adakhala ndi moyo zaka 140. Tsono adaona ana ake ndi zidzukulu zake mpaka mbadwo wachinai.
17
Potsiriza Yobe adamwalira, ali nkhalamba ya masiku ochuluka zedi.
← Chapter 41
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42