bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 7
Job 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 8 →
1
“Moyo wa munthu pa dziko lapansi ndi wa ntchito yakalavulagaga. Masiku ake ali ngati a munthu waganyu.
2
Paja kapolo amalakalaka mthunzi, wantchito amayembekezera malipiro ake,
3
ndiye inenso ndimangovutika nthaŵi zonse. Ngakhale usiku ndimapezabe mavuto.
4
Ndikamagona ndimafunsa kuti, ‘Kodi kucha liti?’ Koma usiku ndi wautali, sindigona tulo, ndimangoti sadabusadabu mpaka mbandakucha.
5
Thupi langa ladzaza mphutsi ndi zonyansa. Khungu langa lang'ambika, ndipo likudza mafinya.
6
Masiku anga ndi othamanga kupambana makina oombera nsalu, amatha opanda chikhulupiriro chilichonse.
7
“Inu Mulungu kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mpweya. Masiku abwino sindidzaŵaonanso.
8
Amene akundiwona tsopano, sadzandiwonanso. Nthaŵi yomwe iye adzandifunafuna, ine ndidzakhala nditapita.
9
Monga mtambo umazimirira ndi kukanganuka, momwemonso munthu woloŵa ku manda sabwerako.
10
Sabweranso kunyumba kwake, ndipo onse omdziŵa amamuiŵala.
11
“Nchifukwa chake sindidzatseka pakamwa. Ndiyenera kulankhula, chifukwa kukhosi kwanga kuli nthumanzi. Ndiyenera kudandaula, chifukwa mumtima mwanga muli zoŵaŵa.
12
Kodi ine ndine nyanja, kapena chilombo cham'nyanja, kuti inu mundiikire alonda?
13
Ndikagona pansi kuti ndithuze mtima, ndi kupeza mpumulo pabedi panga,
14
inu mumandichititsa mantha ndi maloto, mumandiwopsa ndi zinthu zondiwonekera m'masomphenya.
15
Choncho ndikadasankha kudzikhweza kapena kufa kumene, kupambana kupirira zovuta zimene ndikuzimva m'thupi mwanga.
16
Ndatopa nawo moyo wanga, sindingakonde kukhala moyo nthaŵi zonse. Ingondisiyani, poti moyo wanga uli ngati mpweya chabe.
17
Inu Mulungu, kodi munthu nchiyani, kuti muzimganizira chotere, kuti muzisamala zochita zake?
18
Mumampenyetsetsa masiku onse, ndipo mumamuyesa nthaŵi zonse.
19
Kodi mudzaleka liti kumandizonda, kuti ndingopezako mpata womeza malovu?
20
Kodi ndikachimwa, ndimakuvutani bwanji, Inu Wopenyetsetsa anthu? Chifukwa chiyani mwandiika kuti ndikhale ngati choponyerapo chandamale chanu? Chifukwa chiyani ndikukhala ngati katundu wolemera kwa Inu?
21
Chifukwa chiyani simukundikhululukira machimo anga ndi kundichotsera zolakwa zanga? Nthaŵi yoti ndiloŵe m'manda ili pafupi. Inu mudzandifunafuna, koma simudzandiwonanso.” Bilidadi.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42