bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 9
Job 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 10 →
1
Tsono Yobe adayankha kuti,
2
“Inde, ndikudziŵa kuti zimenezi ndi zoona, koma nanga munthu angathe bwanji kukhala wolungama pamaso pa Mulungu?
3
Kodi wina aliyense angathe kutsutsana ndi Mulungu? Ai sangathe kutsutsana naye, chifukwa Mulungu ali ndi mafunso ambiri osayankhika.
4
Mulungu ndi wanzeru, ndipo ndi wamphamvu kwambiri. Palibe munthu amene angathe kulimbana naye, popanda kupwetekerapo.
5
Iyeyo amasendeza mapiri, iwo osadziŵako, amaŵagubuduza ali wokwiya.
6
Ndiye amene amagwedeza dziko lapansi ndi zivomezi, ndipo mizati yake imanjenjemera.
7
Ndiye amene angalamule dzuŵa kuti lisatuluke m'maŵa, ndi kuletsa nyenyezi kuti zisaŵale usiku.
8
Ndi Mulungu yekha amene adayala zakuthambo, ndiye amayenda pa mafunde apanyanja.
9
Ndiye amene adalenga nyenyezi za Mlalang'amba ndi Akamwiniatsatana, Nsangwe ndi Kumpotosimpita.
10
Ndiye amene amachita zazikulu zosamvetseka, ndiye amene amachita zodabwitsa zosaŵerengeka.
11
Ndithu Mulungu akapita pafupi ndi ine, sindimuwona konse. Akandidutsa, ine sindimpenya.
12
Akamalanda zinthu, ndani angathe kumletsa? Ndani angathe kumufunsa kuti, ‘Mukuchita chiyani?’
13
“Mulungu sabweza ukali wake, adaononga adani ake othandizana ndi Rahabu, chilombo choipa chija.
14
Nanga ineyo ndingathe kumuyankha bwanji? Mau okangana naye ndingaŵapeze kuti?
15
Ngakhale ndine wosachimwa, sindingathe kumuyankha Mulungu. Ndiyenera kungopempha chifundo kwa Iye amene akundizenga mlandu.
16
Ngakhale ndikadamuitana, Iye nkuvomera, sindikhulupirira kuti akadamvadi mau angawo.
17
Paja amandikantha ndi mavuto onga mphepo yamkuntho, amandipweteka ndi mabala ambiri, popanda nchifukwa chomwe.
18
Mulungu sandilola kuti ndipume, koma amandichulukitsirachulukitsira zoŵaŵa.
19
Kodi ine nkulimbana ndi Mulungu, mphamvu zonse zija? Kodi ine nkutsutsana ndi Mulungu pa bwalo la milandu? Ndani angamuzenge mlandu?
20
Ngakhale ndine wosalakwa, komabe zolankhula zanga zikhoza kunditsutsa. Ngakhale ndine wopanda cholakwa, akadandipezabe kuti ndine wolakwa.
21
Ine ndiye ndilibe mlandu, koma sindidziyenereza, moyo wanga ndimaunyoza.
22
Palibe chabwino ai. Nchifukwa chake ndikuti, Mulungu amaononga anthu oipa ndi anthu abwino omwe.
23
Pamene munthu wosachimwa afa mwadzidzidzi, Mulungu amangoseka tsoka la munthu wosachimwayo.
24
Mulungu akapereka dziko m'manja mwa anthu oipa, amaŵatseka maso anthu oweruza dzikolo. Ngati si Iyeyo wachita zimenezi, nanga nkukhala yani?
25
“Masiku anga ndi othamanga kwambiri kupambana munthu waliŵiro. Masikuwo amapita, ine osaona zabwino.
26
Amayenda ngati zombo zaliŵiro zapanyanja, ngati mphungu yogudukira nyama yoti idye.
27
Mwina ndinganene kuti, ‘Ndidzaiŵala madandaulo anga, nkhope yanga sidzakhalanso yachisoni, ndipo ndidzasangalala.’
28
Koma ndimaopabe kuti mavuto anga onse adzabwereranso pa ine, pakuti ndikudziŵa kuti Mulungu sadzavomereza kuti ine ndine wosalakwa.
29
Ngati ndine wolakwa ndithu, chabwinotu, zagwa zatha!
30
Ngakhale ndisambe thupi lonse ndi madzi oyera kwambiri, ndi kusamba m'manja ndi sopo,
31
Mulungu adzandiponyabe pa dzala, ndipo zovala zanga zomwe zidzachita nane nyansi.
32
Zoona, Mulungu si munthu ngati ine, kuti ndingakangane naye, sindingathe kutsutsana naye pa mlandu.
33
Palibe mkhalapakati woti nkutiweruza aŵirife, woti nkugamula mlandu pakati pa Mulungu ndi ine.
34
Mulungu asandilange ndi ndodo yake, kuwopa Iye kusandidetse nkhaŵa.
35
Motero ndidakatha kulankhula osamuwopa, koma monga zilirimu, sindingathe konse.”
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42