bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 38
Job 38
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 37
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 39 →
1
Apo Chauta adayankha Yobe m'kamvulumvulu kuti,
2
“Kodi ndiwe amene ukusokoneza uphungu wanga polankhula mau opanda nzeru?
3
Onetsa chamuna, ndidzakufunsa, ndipo undiyankhe.
4
“Kodi udaali kuti pamene ndinkaika maziko a dziko lapansi? Undiwuze ngati ndiwe womvetsa zinthu.
5
Nanga kodi ukudziŵa amene adalemba malire ake, amene adayesapo ndi chingwe padzikopo?
6
Kodi maziko ake adaŵakumba potani? Nanga mwala wake wapangodya adauika ndani?
7
Pa nthaŵiyo nyenyezi zakuvuma zinkaimba pamodzi, ndipo angelo onse a Mulungu ankafuula mokondwa?
8
“Kodi ndani amene adatsekera nyanja pamene inkalengedwa pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko?
9
Ndinetu amene ndidakuta nyanjayo ndi mitambo, ndidaiveka mdima ngati chovala.
10
Ndidailembera malire, ndidaiikira mipiringidzo ndi zitseko zake.
11
Tsono ndidati, ‘Ufike mpaka apo osabzolapo, mafunde ako amphamvuwo aime pomwepo.’
12
“Kodi chibadwire chako udalamulapo dzuŵa kuti lituluke m'maŵa, ndi kuti mbandakucha ukhalepo pa nthaŵi yake?
13
Kodi iweyo udalamulapo kuti kuŵala kwa mbandakuchawo kuunikire dziko lonse lapansi, kuti kuthaŵitse anthu oipa obisala pamenepo?
14
Chifukwa cha kuŵala kwa usana mapiri ndi zigwa zimaonekera bwino ngati makwinya a chovala ngati zilembo za chidindo pa mtapo.
15
Kuŵala kwa dzuŵa sikuŵafika anthu oipa, choncho sangathe kugwira ntchito zao.
16
“Kodi udakayendapo pansi penipeni pa nyanja ndi kukafika pa magwero ake?
17
Kodi adakuwonetsa iwe zipata za imfa? Kodi udaonako ku dziko la anthu akufa kumene kuli mdima wokhawokha?
18
Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziŵa? Undiwuze tsono ngati umazidziŵa zonsezi.
19
“Kodi njira yopita kumene kumakhala kuŵala ili kuti? Nanga mdima, kwao nkuti?
20
Kodi iwe ungathe kuziperekeza kwaoko zimenezi, kodi ukuidziŵa njira yopita kwaoko?
21
Makamaka ukudziŵadi ati, poti paja nthaŵi imeneyo nkuti iweyo utabadwa, ndipo zaka zako kuchuluka ati!
22
“Kodi udaloŵamo m'nyumba zosungiramo chisanu, kapena m'mene amasungira matalala?
23
Zimenezi ndazisungira nthaŵi ya mavuto, ndidzazitumiza nthaŵi yomenyana nkhondo.
24
Kodi udapitako kumene kumatulukira dzuŵa, kapena kumene kumachokera mphepo yakuvuma?
25
“Kodi ndani amene adakonza ngalande za mvula? Ndani adakonza njira zodzeramo mphezi?
26
Ndani amagwetsa mvula pa chipululu popanda anthu, ku dziko kumene sikukhala anthu.
27
Ndani amathirira dziko louma lagwaa, kotero kuti udzu umamerapo?
28
“Kodi mvula ili ndi bambo wake? Nanga madzi a mame adaŵabeleka ndani?
29
Kodi chisanu choundana adachibala ndani? Nanga adabereka chipale chochokera kumwamba ndani?
30
Ndani amasandutsa madzi kuti alimbe ngati mwala, pamene madzi apanyanja amazizira, nalimba kuti gwaa?
31
“Kodi Nsangwe iwe ungazimange maunyolo? Kodi zingwe za Akamwiniatsatana iwe ungathe kuzimasula?
32
Kodi ungathe kuwongolera nyenyezi pa nyengo yake? Kodi ungathe kutsogolera nyenyezi yaikulu ya Chimbalangondo pamodzi ndi tiana take?
33
Kodi malamulo a mlengalenga umaŵadziŵa? Nanga ulamuliro wake, kodi ungaukhazikitse pa dziko lapansi?
34
“Kodi iwe ungathe kulamula mitambo kuti igwetse mvula ya chigumula?
35
Kodi ungathe kutumiza zing'aning'ani kuti zing'anipe, ndi kugwera pa malo amene iwe ukufuna?
36
Ndani amene adayala mitambo bwino mu mlengalenga? Nanga ndani adalangiza mvula kuti igwere pakutipakuti?
37
Wanzeru ndani amene angathe kuŵerenga mitambo, nanga ndani angathe kupendeketsa mitsuko ya madzi akuthambo
38
amene amasandutsa fumbi matope, ndi kuumba zibumi?
39
“Kodi iwe ungathe kuufunira chakudya mkango? Kodi ungathe kuipatsa chakudya misona yake ija,
40
pamene ili khale m'mapanga mwake, kapena pamene ikubisala m'tchire?
41
Kodi khwangwala amampatsa chakudya chake ndani, pamene maunda ake akulirira kwa Mulungu, namadzandira chifukwa chosoŵa chakudya?”
← Chapter 37
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 39 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42