bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 13
Job 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 14 →
1
“Zonse mukunenazi ndidaziwona ndi maso, ndidazimva ndi makutu anga, ndipo ndidazimvetsa.
2
Zimene inu mumadziŵa, inenso ndimazidziŵa. Inu simundipambana ai.
3
Koma ine ndikadakonda kulankhula ndi Mphambe, ndikadakonda kukamba naye Mulungu za mlandu wanga pamasompamaso.
4
Inuyo ndinu okometsa zinthu ndi mabodza. Nonsenu muli ngati asing'anga apakamwa chabe.
5
Achikhala munangokhala chete, apo mukadachita zanzeru
6
Tsono mumve zimene nditi ndinene, mumvere mau anga ofotokoza za mlandu wanga.
7
Kodi chifukwa chiyani mukunama potchula Mulungu? Chifukwa chiyani mukunena mabodza m'dzina lake?
8
Kodi mukuti mukondere Mulungu? Kodi mukuti muteteze Mulungu pa mlandu wake?
9
Mulungu atayang'anitsitsa inu, kodi nkukupezani kuti ndinu osalakwa? Kodi mungathe kumnyenga monga m'mene munthu anganyengere munthu mnzake?
10
Ndithudi, adzakudzudzulani, mukamachita zokondera m'seri.
11
Kodi ulamuliro wake sungakuwopseni? Kodi mphamvu zake sizingakuchititseni mantha?
12
Miyambi yanuyi ndi yopandapake ngati phulusa. Zimene mukulankhula kuti mudzitchinjirize nazo zili ngati dothi.
13
“Mukhale chete, ineyo ndilankhule, ndipo zimene zichitike, zichitike.
14
Ndili wokonzeka kuika moyo wanga pa chiswe, kaya nkufa, ndife basi.
15
Ngakhale Mulungu andiphe, ndidzamkhulupirirabe, ndipo ndidzafotokoza mlandu wanga pamaso pake.
16
Kulimba mtima kwanga ndiye kudzandipulumutse, poti munthu woipa sangafike pamaso pa Mulungu.
17
Mumvetsere mau anga mosamala, mutchere khutu zolankhula zanga.
18
Mlandu wanga ndaukonza, ndikudziŵa kuti sadzandipeza wolakwa.
19
Kodi pali yani amene angatsutsane nane? Ngati zili choncho, ndidakangokhala chete, nkufa basi.
20
Inu Mulungu, ndikukupemphani zinthu ziŵiri zokha, sindidzayesa kukubisalirani.
21
Muleke kundilanga, kuwopa Inu kusandidetse nkhaŵa.
22
Mundiitane tsono ndipo ndidzayankha. Kapena mundilole kuti ndilankhule ndine, Inuyo mundiyankhe.
23
“Kodi zolakwa zanga nzingati, ndipo machimo anga ndangati? Mundidziŵitse kulakwa kwanga ndi kuchimwa kwanga.
24
Chifukwa chiyani mukundifulatira? Bwanji mukundiyesa mdani wanu?
25
Kodi mukufuna kuwopsa ine, tsamba louluka ndi mphepone? Kapena mukuti mundithamangitse, ine mungu woumane?
26
Inu mukundizenga zinthu zondiŵaŵa, umafukula ngakhale zolakwa za pa ubwana wanga.
27
Inu mumamanga miyendo yanga ndi matangadza, mumalonda mayendedwe anga onse, mumazonda ndi poponda mapazi anga pomwe.
28
Motero munthu amatha ngati chinthu chofumbwa, ngati chovala chodyewa ndi njenjete.”
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42