bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 4
Job 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 5 →
1
Tsono Elifazi wa ku Temani adati,
2
“Iwe Yobe, kodi wina atakuyankha, ndiye kuti wakulakwira? Ah, koma ine ndekha sindingathe kukhala chete.
3
Taona, iwe waphunzitsa anthu ambiri, walimbitsa mtima anthu ofooka.
4
Mau ako adathandiza munthu wofuna kugwa, adachirikiza munthu wotha mphamvu.
5
Koma tsopano mavuto akufikira iweyo, ndipo wataya mtima. Zakukhudza lero, ndipo ukuchita mantha.
6
Unkalemekeza Mulungu, tsono uyenera kumdalira Iyeyo, Unkayenda m'njira yosalakwa, tsono uyenera kukhulupirira Mulungu.
7
“Ganiza bwino tsopano: Kodi alipo munthu wosachimwa amene adaonongekapo nkale lonse? Nanga nkuti kumene udaona anthu olungama ataphedwa?
8
Monga ndaonera ine, anthu amene amabzala tchimo namafesa mavuto, amakolola zomwezo.
9
Monga momwe mphepo ya mkuntho imasakazira zinthu, Mulungu amaŵaononga ndi mkwiyo wake.
10
Anthu oipa amakhuluma ngati mkango, koma Mulungu amaŵathyola mano.
11
Iwowo amafa ngati mikango yosoŵa nyama, ndipo misona yao imamwazikana.
12
“Tsono mau adandifika monong'ona, khutu langa lidamva kunong'onako.
13
Zidandibwerera usiku m'masomphenya, nthaŵi imene anthu amagona tulo tofa nato.
14
Ndidagwidwa ndi mantha, nkuyamba kunjenjemera, thupi langa lonse lidaweyeseka.
15
Pamenepo mpweya wayaziyazi udandidutsa kumaso, ndipo ubweya wa pathupi panga udangoti njoo, kuimirira, chifukwa cha mantha.
16
Chinthucho chidangoti chilili, koma ine osaŵazindikira maonekedwe ake. Patsogolo panga panali chinthu ndithu, kudangoti zii, kenaka ndidamva mau akuti:
17
‘Kodi munthu angathe kukhala wolungama pamaso pa Mulungu? Kodi munthu angathe kukhala wangwiro pamaso pa Mlengi wake?
18
Mulungu sakhulupirira ndi atumiki ake omwe, angelo ake omwe amaŵapeza cholakwa.
19
Nanji munthu amene adachokera ku dothi, amene ali fumbi chabe, amene amathudzuka ngati kadziwotche.
20
M'maŵa ali moyo, madzulo nkufa munthuyo. Amapita ku manda, naiŵalika kotheratu.
21
Zonse zimene ali nazo zimatha, ndipo amafa osadziŵa nkanthu komwe.’ ”
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42