bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 10
Ezekiel 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 11 →
1
Ndidayang'ana ku thambo lija lili pamwamba pa mitu ya akerubi, ndipo ndidaona chinthu chooneka ngati mpando waufumu wopangidwa ndi mwala wokoma wa safiro.
2
Tsono Chauta adauza munthu wovala zabafuta uja kuti, “Pita pakati pa mikombero kunsi kwa akerubi, udzaze manja ako ndi makala oyaka amene ali pakati pa Akerubiwo. Tsono makalawo uŵawaze mu mzinda.” Ndipo ndidamuwona akupitadi.
3
Ndiye kuti akerubi adaaimirira ku dzanja lamanja la Nyumba ya Chauta pamene munthuyo ankaloŵa. Ndipo mtambo udaadzaza bwalo lam'kati.
4
Ulemerero woŵala wa Chauta udachoka pamene udaali, pamwamba pa akerubi, nukafika pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Tsono Nyumbayo idadzaza ndi mtambo uja, ndipo ulemerero woŵala uja wa Chauta udadzaza bwalo.
5
Phokoso la mapiko a akerubi lidamveka mpaka ku bwalo lakunja, monga momwe limamvekera liwu la Mulungu Mphambe akamalankhula.
6
Kenaka Mulungu adauza munthu wovala zabafuta uja kuti akapale moto pakati pa mikombero, kunsi kwa akerubi. Munthuyo adaloŵa nakaima pambali pa mkombero umodzi.
7
Pomwepo mmodzi mwa akerubiwo adatambalitsa dzanja lake mpaka pa moto umene unali pakati pao. Adapalako motowo, napatsa munthu wovala zabafuta uja. Iyeyo adalandira motowo nkutuluka.
8
Ndiye kuti kunsi kwa mapiko a akerubi kunali chinthu chooneka ngati dzanja lamunthu.
9
Pambuyo pake ndidaona mikombero inai pambali pa akerubi. Pambali pa kerubi aliyense panali mkombero umodzi. Mikomberoyo inkanyezimira ngati miyala ya krizoliti.
10
Maonekedwe a mikomberoyo anali ofanana, ndipo inali yoloŵanaloŵana.
11
Poyenda akerubiwo ankapita mbali iliyonse mwa mbali zao zinai zimene ankayang'ana, osachita kutembenuka. Kumene mutu walunjika, nkumene ankapita.
12
Matupi ao, misana yao, mapiko ao pamodzi ndi mikombero yonse inai, zonse zinali ndi maso.
13
Ndidamva phokoso la mikombero monga lomwe ndidaalimva poyamba paja pamene ndinkaona zinthu m'masomphenya.
14
Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinai. Nkhope yoyamba inali ya kerubi, yachiŵiri inali ya munthu, yachitatu inali ya mkango, yachinai inali ya chiwombankhanga.
15
Tsono akerubi aja adauluka. Akerubiwo anali zilengolengo zonzija zimene ndidaaona ku mtsinje wa Kebara.
16
Akerubi ankati akamayenda, nayonso mikombero inkayenda m'mbali mwao. Pamene akerubi ankatambasula mapiko ao ndi kuuluka, mikombero inali m'mbali mwao ndithu.
17
Zilengolengo zikaima, mikombero inkaimanso. Zikauluka, mikombero inkapita nawo ndithu, pakuti mzimu wa zilengolengozo ndiwo unkayendetsa mikomberoyo.
18
Pamenepo ulemerero woŵala wa Chauta udachokapo pa chiwundo cha Nyumba yake nukakhalanso pamwamba pa akerubi.
19
Apo Akerubi adatambasula mapiko ao nauluka. Ndidaŵaona akupita, mikombero ili pambali pao. Adakaima pa khomo lakuvuma la Nyumba ya Chauta. Ndipo ulemerero woŵala wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pao.
20
Zimenezi ndizo zilengolengo zimene ndidaaziwona ku mtsinje wa Kebara, kunsi kwa mpando waufumu wa Mulungu wa Israele. Ndidazindikira kuti zilengolengozo zinali akerubi.
21
Akerubiwo aliyense anali ndi mapiko anai ndi nkhope zinai. Analinso ndi chinthu chooneka ngati dzanja lamunthu kunsi kwa mapiko ao.
22
Nkhope zao zinali zonga zimene ndidaaziwona m'masomphenya ku mtsinje wa Kebara. Chilengolengo chilichonse chinkayenda molunjika kutsogolo.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48