bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 41
Ezekiel 41
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 40
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 42 →
1
Pambuyo pake munthu uja adapita nane m'chipinda chopatulika cha Nyumba ya Mulungu, nayesa mphuthu zake. Muufupi mwake munali mamita atatu mbali iliyonse.
2
Muufupi mwake mwa khomo munali mamita asanu. Zipupa zake zam'mbali zinali za mamita aŵiri ndi theka muufupi mwake mbali iliyonse. Adayesa kutalika kwake kwa chipindacho, kunali mamita makumi aŵiri, muufupi mwake mamita khumi.
3
Kenaka adakaloŵa m'kati nakayesa mphuthu zapakhomo. Zinali za mita limodzi, ndipo khomolo linali la mamita atatu. Zipupa za m'mbali mwa khomolo zinali za mamita atatu ndi theka mbali iliyonse.
4
Pambuyo pake adayesa chipinda chenichenicho napeza kuti m'litali mwake ndi muufupi mwake munali mamita khumi. Apo adandiwuza kuti, “Chimenechi ndicho chipinda chopatulika kwambiri.”
5
Tsono munthu uja adayesa khoma la Nyumba ya Mulungu, linali la mamita atatu. Panali zipinda zina kuzungulira Nyumbayo, chilichonse muufupi mwake chinali cha mamita aŵiri.
6
Zipindazo zinali zitatu zosanjikizana, chigawo chilichonse chinali ndi zipinda makumi atatu. Pa makoma a Nyumba ya Mulunguyo panali zochirikiza zipindazo, kuti zisamatsamire pa chipupa cha Nyumba ya Mulungu.
7
Zipinda zam'mbalizo zinkapita zikukulirakulira pomakwera chipinda ndi chipinda, potsata kukulirakulira kwa zochirikiza za zipinda zija. Pambali pa Nyumba ya Mulungu panali makwerero okwerera pamwamba, kuchokera chigawo chapansi kudzera chapakati, mpaka kukafika chapamwamba.
8
Tsono ndidaona chiwundo chozungulira Nyumba ya Mulungu. Chidapanga maziko a zipindazo, ndipo chinali cha mamita atatu.
9
Khoma la kunja kwa zipindazo linali la mamita aŵiri ndi theka kuchindikira kwake. Pakati pa chiwundocho
10
ndi zipinda za Nyumba ya Mulunguyo panali bwalo la mamita khumi m'kupingasa kwake, kuzungulira Nyumba yonseyo.
11
Zipinda zam'mbalizo zinali zotsekulira ku mbali za chiwundo. Chitseko chimodzi chinkayang'ana kumpoto, china chinkayang'ana kumwera. Kukula kwa chiwundo chosamangapo kanthu kunali mamita aŵiri ndi theka kuzungulira ponseponse.
12
Chakuzambwe, kuyang'anana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu, kunali nyumba inanso ya mamita 35 muufupi mwake. Khoma lake linali la mamita aŵiri ndi theka kuchindikira kwake kuzungulira ponseponse, m'litali mwake linali la mamita 45.
13
Tsono munthu uja adayesa Nyumba ya Mulungu, m'litali mwake inali ya mamita makumi asanu. Bwalo la Nyumbayo ndi makoma ake, zonse zinali za mamita makumi asanu.
14
Kumaso kwa Nyumba ya Mulungu chakuvuma kwa bwalolo muufupi mwake munali mamita makumi asanu.
15
Kenaka adayesa kutalika kwa nyumba yoyang'anana ndi bwalolo chakuzambwe kwa Nyumba ya Mulungu, ndi njira zam'kati ku mbali iliyonse. Zonsezo zinali za mamita makumi asanu. Chipinda cha m'thunthu mwa Nyumba ya Mulungu, chipinda cham'kati ndiponso khonde lam'kati loyang'ana kunja,
16
mazenera ndi made ake, zonsezo zinali zochingidwa ndi matabwa. Pamwamba, kupenyana ndi chiwundo, Nyumba ya Mulungu idaakutidwa ndi matabwa kuyambira pansi mpaka ku mazenera, ndipo mazenerawo anali okutidwa.
17
Pamwamba pa khomo loloŵera ku chipinda cham'kati,
18
adaazokotapo zithunzi za akerubi ndi za kanjedza. Kerubi mmodzi adaakhala pakati pa kanjedza muŵiri. Kerubi aliyense anali ndi nkhope ziŵiri:
19
ina inali nkhope ya munthu, yoyang'ana kanjedza wa mbali imodzi, ina inali nkhope ya mkango yoyang'ana kanjedza wa mbali ina. Zidachingidwa choncho kuzungulira Nyumba yonse.
20
Motero kuyambira pansi mpaka pamwamba pa zitseko panali zithunzi zozokota za akerubi ndi za kanjedza.
21
Mphuthu za chipinda cham'thunthu kutalika kwake mbali zonse kunali kolingana. Kumaso kwa malo opatulika kunali chinthu chooneka ngati
22
guwa lansembe la matabwa. Msinkhu wake unali wa mita limodzi ndi hafu, m'litali mwake munali mita limodzi, muufupi mwake munalinso mita limodzi. Mphuthu zake, tsinde lake ndi makoma ake, zonse zinali zopanga ndi mtengo. Munthu uja adandiwuza kuti, “Tebulo limeneli ndilo limene limakhala pamaso pa Chauta.”
23
Chipinda cham'thunthu chija chinali ndi zitseko ziŵiri, malo oyera analinso ndi zitseko ziŵiri.
24
Pa chitseko chilichonse panali zigawo ziŵiri zopatukana.
25
Pazitsekopo adazokotapo zithunzi za akerubi ndi za kanjedza, monga pa makoma aja. Kunja kwake kunali ngati denga lamatabwa pamwamba pa khonde lam'kati.
26
Pa mbali zonse za khonde lam'katilo panali mazenera, ndipo pa zipupa zake zonse adazokotapo zithunzi za kanjedza.
← Chapter 40
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 42 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48