bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 35
Ezekiel 35
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 34
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 36 →
1
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, yang'ana ku dziko lamapiri la ku Seiri, ndipo ulengeze mau oliimba mlandu.
3
Anthu akumeneko uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: “Inu anthu a ku mapiri a ku Seiri ndikudana nanu. Ndidzakumenyani ndi dzanja langa, ndidzasandutsa dziko lanu tsala ndi chipululu.
4
Mizinda yanu ndidzaisandutsa mabwinja, ndipo dziko lanu lidzakhala chipululu. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
5
“Munali adani a Israele nthaŵi zonse, ndipo munkalola kuti anthu ake aziphedwa pa nthaŵi ya mavuto ao, pa nthaŵi imene chilango chao chidafika pa chimake.
6
Tsono Ine Ambuye Chauta ndikuti, ‘Pali Ine ndemwe, ndidzakhetsa magazi anu, ndipo imfa idzakulondolani. Zoonadi, mudakhetsa magazi, tsono imfa idzakulondolani.
7
Phiri la Seiri ndidzalisandutsa tsala ndi chipululu. Ndidzapha onse amene amayenda kumeneko.
8
Mapiri ake ndi zigwa zake ndidzazidzaza ndi mitembo, tsono ophedwa pa nkhondo adzangoti vuu pa magomo, m'zigwa ndi m'mitsinje yanu.
9
Dziko lanu ndidzalisandutsa bwinja mpaka muyaya, ndipo m'mizinda mwanu simudzakhalanso munthu. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.’
10
“Inu mudanena kuti, ‘Mitundu iŵiri ya anthu, Yuda ndi Israele, idzakhala yathu pamodzi ndi maiko ao omwe.’ Mudatero ngakhale kuti Ine Chauta ndinali nao m'menemo.
11
Tsono Ine Ambuye Mulungu ndikuti, Pali Ine ndemwe, ndidzakuchitani zomwe mudaŵachita anthu anga poŵaonetsa mkwiyo wanu, nsanje yanu ndi chidani chanu. Mudzandidziŵadi pakati panupo, ndikadzakulangani.
12
Mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndidamva mau anu onse onyoza mapiri a ku Israele. Mudanena kuti, ‘Mapiri a ku Israele asiyidwa, ndipo atipatsa kuti tiŵaononge.’
13
Ndidamva zondinyoza zimene mudanena monyada. Ndidadzimvera ndekha zonse!
14
Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndidzakusandutsani bwinja kotheratu, kotero kuti dziko lonse lapansi lidzakondwa nako kugwa kwanu.
15
Monga momwe inu mudakondwera ndi kugwa kwa Israele, Ine ndidzakuchitaninso zomwezo. Iwe phiri la Seiri, ndi dziko lonse la Edomu, udzasanduka bwinja. Motero anthu onse adzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Mulungu.”
← Chapter 34
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 36 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48