bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 14
Ezekiel 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 15 →
1
Tsiku lina akuluakulu ena a Aisraele adadza kwa ine nadzakhala pansi pamaso panga.
2
Tsono Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
3
“Iwe mwana wa munthu, anthu ameneŵa aika mtima pa mafano ao, aikanso maso ao pa zinthu zina zophunthwitsa. Kodi iwoŵa akuganiza kuti ndidzaŵayankha akadzapempha nzeru kwa Ine?
4
Tsono uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ngati Mwisraele wina aliyense aika mtima pa mafano ake, naikanso maso ake pa zinthu zina zophunthwitsa, kenaka nkupita kwa mneneri, Ineyo Chauta mwiniwakene ndidzamuyankha moyenerana ndi kuchuluka kwa mafano ake.
5
Ndidzatero kuti mwina mwake nkukopanso mitima ya Aisraele amene andisiya chifukwa cha mafano ao.
6
“Nchifukwa chake uŵauze Aisraele kuti Ineyo Ambuye Chauta ndikunena kuti, ‘Lapani, mulekane nawo mafano anu. Muzisiye zonyansa zanu zonse.’
7
Ngati munthu wina aliyense, Mwisraele kapena mlendo wongokhala nao, andikana Ine, naika mtima pa mafano ake, ndi kuika maso ake pa zinthu zina zophunthwitsa, munthu woteroyo akabwera kudzapempha nzeru kwa Ine, kudzera mwa mneneri, Ine Chauta mwiniwakene ndidzamuyankha.
8
Ndiye kuti ndidzalimbana naye munthu ameneyo. Ndidzamusandutsa chitsanzo ndi chisudzo, ndipo ndidzamchotsa pakati pa anthu anga. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
9
“Ngati mneneri anyengedwa nalosa, ndine Chauta amene ndamnyenga. Ndipo ndidzamkantha ndi dzanja langa ndi kumchotsa pakati pa anthu anga Aisraele.
10
Chilango cha mneneriyo ndi cha munthu amene adadzapempha nzeru kwa iyeyo, chidzalingana.
11
Ndidzachita zimenezi kuti Aisraele asandithaŵenso, ndipo kuti asiye machimo ao. Pamenepo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
12
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
13
“Iwe mwana wa munthu, dziko likandichimwira, posandikhulupirira Ine, ndidzalikantha ndi dzanja langa ndi kuchepetsa chakudya chake. Ndidzatumiza njala m'dzikomo, ndipo ndidzaononga anthu pamodzi ndi nyama zomwe.
14
Ngakhale anthu atatu aŵa, Nowa, Daniele ndi Yobe, akadakhala kumeneko, akadangopulumutsa moyo wao wokha chifukwa cha kukhulupirika kwao. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
15
Mwina ndikadatumiza zilombo kuti ziyende m'dzikomo ndi kuwononga anthu ake, mpaka dzikolo kusanduka chipululu chakuti munthu sangadutsemo chifukwa cha zilombo.
16
Apo ngakhale anthu atatu aja akadakhala kumeneko, ndithu pali Ine ndemwe Ambuye Chauta amoyo, iwo aja sakadatha kupulumutsa ngakhale ana ao omwe. Akadangopulumutsa moyo wao wokha, koma dzikolo likadasanduka chipululu ndithu.
17
“Mwina ndikadatumiza nkhondo ku dziko limenelo ndi kulamula kuti ipite m'dzikomo ndi kuwononga anthu ndi nyama zomwe.
18
Apo ngakhale anthu atatu aja akadakhala kumeneko, ndithu pali Ine ndemwe Ambuye Chauta amoyo, iwo aja sakadapulumutsa ngakhale ana ao, akadangodzipulumutsa iwo okha.
19
“Mwina ndikadatumiza mliri m'dziko limenelo, ndi kuwonetsa ukali wanga pokhetsa magazi ndi kuwononga anthu ndi nyama zomwe.
20
Apo ngakhale Nowa, Daniele ndi Yobe akadakhala kumeneko, ndithu pali Ine ndemwe Ambuye Chauta amoyo, iwo aja akadadzipulumutsa iwo okha chifukwa cha kulungama kwao, koma ana ao ai.
21
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Kudzakhala zoopsa kwambiri pamene ndidzagwetsa pa Yerusalemu zilango zanga zinai izi: nkhondo, njala, zilombo ndi mliri, kuti ziwononge anthu ndi nyama.
22
Koma ena adzatsalako m'dzikomo odzatulutsa ana aamuna ndi aakazi, muŵapenyetsetse akadza kwa inu, muwone m'mene akhalire ndi zimene achite. Mitima yanu idzakhazikika pansi, mukakumbukira zoipa zimene ndachita ku Yerusalemu, chilango chonse chimene ndalanga nacho mzindawo.
23
Mitima yanu idzakhaladi pansi, poona m'mene iwo akhalira ndi zimene akuchita, ndipo mudzamvetsa kuti Yerusalemu sindidamchite zimenezi popanda chifukwa. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48