bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 13
Ezekiel 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 14 →
1
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, ulose zodzudzula aneneri a ku Israele. Amene amalosa za kukhosi kwao, zongopeka okha, uŵauze kuti amve mau a Ine Chauta!
3
Ine Ambuye Chauta ndikunena kuti, Tsoka kwa aneneri opusa amene amachita kupeka zolosa zao, chonsecho sadaone chilichonse chochokera kwa Ine.
4
Inu Aisraele, aneneri anu akhala ngati nkhandwe zam'mabwinja.
5
Simudakwere khoma kuti mukakonze m'mene mudagumuka, kuti banja la Israele lidziteteze kolimba pa nkhondo, pa tsiku la Chauta.
6
Aneneriwo amalankhula zonama, ndipo amalosa zabodza. Amanena kuti, ‘Akuterotu Chauta,’ pamene Chauta sadaŵatume konse. Komabe amayembekeza kuti zimene anenazo zidzachitika.
7
Koma Ine ndikuti, Zimene inu aneneri mukuti mudaziwona m'masomphenya nzabodza. Ndipo kulosa kwanuko nkwabodza. Mumanena kuti ‘Akuterotu Chauta,’ ngakhale Ine sindidalankhule konse.”
8
“Tsono zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndikukutsutsani chifukwa choti mau anu ngachabe, ndipo zimene mukuti mudaziwona ngati kutulo nzabodza.
9
Ndidzakantha aneneri onama amene amati adaona zakutizakuti ngati kutulo, amenenso kulosa kwao nkwabodza. Sadzakhala nao m'bwalo la aphungu la anthu anga. Sadzalembedwa m'kaundula wa nzika za Israele, ndipo sadzaloŵa m'dziko la Israele. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta.
10
“Ndithudi aneneri asokeza anthu anga pomanena kuti, ‘Kudzakhala mtendere,’ pamene kulibe mtendere, ndipo chifukwa anthu akamanga khoma, aneneri amalipaka njereza.
11
Uŵauze opaka njerezawo kuti khomalo lidzagwa. Mvula idzavumba mwamphamvu, kudzagwa matalala akuluakulu, ndipo kudzaomba mphepo yamkuntho.
12
Pamenepo khomalo litagwa, nanga anthu sadzakufunsani kuti, ‘Kodi njereza imene mudapaka ija ili kuti tsopano?’
13
Nchifukwa chake zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndidzakunthitsa mphepo yolimba nditakwiya. Ndidzavumbitsa mvula yamphamvu ndili ndi ukali. Ndidzagwetsa matalala akuluakulu mwachipseramtima, mpaka khomalo litaonongeka kotheratu.
14
Ndidzagwetsa khoma limene mudalipaka njerezalo. Ndidzaligamuliratu mpaka maziko ake ataoneka. Pamene lidzagwa, inunso mudzafera momwemo. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
15
Ndimo m'mene ndidzagwiritsire ntchito mkwiyo wanga pa khomalo ndi pa amene ankalipaka njereza aja. Apo ndidzakuuzani kuti, ‘Khoma lagwa, amene ankalimata aja nawonso agwera kumodzi.
16
Agwanso aneneri a ku Israele amene ankalosa ku Yerusalemu, amene ankati adaona zamtendere m'masomphenya, pamene mtendere kunalibe.’ Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
17
“Tsono iwe mwana wa munthu, ugwepo pa nkhani ya akazi amene ali pakati pa anthu ako. Iwowo amalosa zopeka za mumtima mwao, tsono uŵadzudzule.
18
Uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Tsoka kwa akazi amene amasoka zithumwa zapamkono, amenenso amasoka nsalu zakumutu za anthu a misinkhu yosiyanasiyana, kuti azikola mitima ya anthu. Kodi mufuna kukola mitima ya anthu anga, inuyo nkupulumutsa moyo wanu?
19
Mwandichotsa ulemu pamaso pa anthu anga, chifukwa chofuna kulandira manja angapo a barele ndiponso zidutswa chabe za buledi. Mukupha anthu osayenera kufa, ndipo mukupulumutsa anthu osayenera kukhala moyo, pomanamiza anthu angaŵa amene amamva zabodza zanuzo.
20
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikunena kuti, Ndikuzikana zithumwa zanu zapamkono, zimene mumakolera mitima ya anthu ngati mukukola mbalame. Ndidzazithothola pa mikono yanu, kuti ndiŵapulumutse anthuwo amene mumaŵakola ngati mbalame.
21
Ndidzang'ambanso nsalu zanu zamankhwala zakumutu, ndipo ndidzapulumutsa anthu anga m'manja mwanu. Simudzakhalanso ndi mphamvu zoŵakolera. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
22
Ndi mabodza anu mudatayitsa mtima anthu anga abwino amene Ine sindidafune kuti ataye mtima. Mudalimbitsa mtima anthu oipa kuti asaleke machimo ao, choncho satha kupulumutsa moyo wao.
23
Nchifukwa chake zolosa zanu zabodza zimene mukuti mudaziwona ngati kutulo, simudzaziwonanso, ndipo simudzaombezanso. Ndidzapulumutsa anthu anga m'manja mwanu. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48