bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 30
Ezekiel 30
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 31 →
1
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, ulose ndipo ulengeze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: “ ‘Pepani, tsiku latsoka lafika!
3
Ndithudi layandikira, tsiku la Chauta lili pafupi. Tsiku lamitambo, tsiku la kutha kwa mitundu ya anthu.
4
Ku Ejipito kudzafika nkhondo, ndipo ku Etiopiya kudzagwa mavuto. Anthu ambiri adzaphedwa ku Ejipito, chuma chake chidzatengedwa, ndipo maziko ake adzagumuka.’
5
“Etiopiya, Puti, Ludi, Arabiya yense, Libiya ndiponso anthu a m'dziko logwirizana naye, adzaphedwa nao limodzi pa nkhondoyo.
6
“Zimene ndikunena Ine Chauta ndi izi: Onse othandiza Ejipito adzaphedwa. Ndipo kunyadira mphamvu zake kudzamthera. Anthu ake adzaphedwa pa nkhondo kuyambira ku Migidoli mpaka ku Siyene. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
7
Dziko la Ejipito lidzasanduka bwinja kupambana mabwinja onse opasuka. Mizinda yake idzakhala yopasuka kupambana mizinda ina yoonongeka.
8
Nditamtentha Ejipito ndi kuthyola onse omuthandiza, adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
9
“Nthaŵi imeneyo ikadzafika, amithenga adzapita mofulumira kuchokera kwa Ine kukaopsa Aetiopiya, iwowo osadziŵako kanthu. Ndipo adzada nkhaŵa pa tsiku limene Ejipito adzaonongedwa, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu.
10
“Mau a Ine Ambuye Chauta ndi aŵa: Ndidzatuma Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni kuti adzathetse chuma cha Ejipito.
11
Iyeyo ndi anthu ake, mtundu wa anthu ankhalwe kwambiri aja, adzabwera kudzaononga dzikolo. Adzasolola malupanga ao kuti amenyane ndi Aejipito, ndipo dzikolo lidzadzaza ndi mitembo.
12
Ndidzaumitsa mtsinje wa Nailo, ndipo Ejipito ndidzamgulitsa kwa anthu oipa. Dzikolo ndidzaliwononga, pamodzi ndi zonse zam'menemo, polipereka m'manja mwa anthu akudza. Ine Chauta ndatero.
13
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndidzathetsa mafano ndi kuwononga milungu yosema ya ku Memfisi. Sikudzakhalanso mfumu ku Ejipito. Ndipo ndidzaŵaopsa onse okhala m'dziko limenelo.
14
“Mzinda wa Patirosi ndidzausandutsa chipululu. Mzinda wa Zowani ndidzautentha. Mzinda wa Thebesi ndidzaulanga.
15
Mzinda wa Peluziumu, linga lolimba la Ejipito, ndidzauthira mkwiyo wanga, ndipo ndidzaononga gulu lankhondo la ku Thebesi.
16
Ejipito yense ndidzamtentha, ndipo Memfisi adzavutika kwambiri. Malinga a ku Thebesi adzagumuka, ndipo makoma ake adzaonongekeratu.
17
Anyamata a ku Oni ndi a ku Pibeseti adzaphedwa pa nkhondo, ndipo akazi adzatengedwa ukapolo.
18
Ku Tehafinehesi kudzachita mdima, pamene ndidzathyole mphamvu za Ejipito kumeneko. Motero kunyada kwake kudzatha. Mitambo idzamuphimba, ndipo okhala m'midzi yake adzatengedwa ukapolo.
19
Motero ndidzamlanga Ejipito, ndipo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
20
Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri la mwezi woyamba, chaka cha khumi ndi chimodzi cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti:
21
“Iwe mwana wa munthu, ndathyola dzanja la Farao, mfumu ya ku Ejipito. Ona, sadalimange kuti lichire, ndipo sadalilimbitse ndi nsalu kuti lithe kugwiranso lupanga.
22
Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndikudana naye Farao, mfumu ya ku Ejipito. Ndidzamthyola manja onse, lamoyo ndi lothyokalo, ndipo lupanga lake lidzamtayika.
23
Ndidzaŵamwaza Aejipito pakati pa mitundu ya anthu ndi kuŵabalalitsira ku maiko ambiri.
24
Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, ndipo m'manja mwake ndidzaikamo lupanga langa. Koma Farao ndidzamthyola manja, ndipo adzabuula ngati wolasidwa koopsa pamaso pa mfumu ya ku Babiloniyo.
25
Ndithu ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, koma manja a Farao adzafooka. Motero anthu adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzaika lupanga langa m'manja mwa mfumu ya ku Babiloni. Ndipo adzaligwiritsa ntchito pomenya nkhondo ndi dziko la Ejipito.
26
Ndidzamwaza Aejipito pakati pa mitundu ya anthu, ndi kuŵabalalitsira ku maiko ambiri. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 31 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48