bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 38
Ezekiel 38
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 37
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 39 →
1
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, udzudzule Gogi, wa ku dziko la Magogi, kalonga wamkulu wa mzinda wa Meseki ndi wa Tubala, ndipo umuimbe mlandu.
3
Umuuze kuti Ine Ambuye Chauta, ndikuti, Ndikudana nawe, iwe Gogi, kalonga wamkulu wa ku Meseki ndi ku Tubala.
4
Ndidzakuzunguza, ndidzakukola ndi mbedza m'kamwa mwako. Ndidzakutulutsira poyera, iweyo pamodzi ndi gulu lako lonse lankhondo, akavalo ndi okwerapo ake. Onsewo adzakhala atanyamula zishango ndi malihawo, malupanga ao ali osololasolola.
5
Pamodzi ndi iwowo palinso asilikali a ku Persiya, ku Etiopiya ndi ku Puti. Onsewo ali ndi zishango ndi zisoti zankhondo.
6
Palinso Gomeri ndi magulu ake onse ankhondo, banja la Togarima ndi gulu lake lankhondo lochokera kutali kumpoto. Palidi mitundu ya anthu ambiri imene ili nawe.
7
“Konzekani, mukhale okonzeka ndithu, iweyo pamodzi ndi gulu lonse lankhondo limene lasonkhana mokuzungulira. Ndiwe amene udzaŵatsogolere pokamenya nkhondo.
8
Ndidzakuitana patapita masiku ambiri. Zaka zikubwerazi, ndidzakuloŵetsa m'dziko lopulumuka ku nkhondo. Udzaŵapeza anthu atasonkhana kuchokera ku mitundu yambiri ya anthu, atakhazikika ku mapiri a Aisraele amene adaasiyidwa nthaŵi yaitali. Aisraelewo adaŵatulutsa pakati pa mitundu ya anthu, ndipo onsewo ali pa mtendere tsopano.
9
Tsono iweyo ndi magulu ako ankhondo ndi mitundu yambiri ya anthu imene ili nawe, mudzabwera ngati mphepo yamkuntho. Mudzaphimba dziko lonse ngati mtambo.
10
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Pa tsiku limenelo mumtima mwako mudzaloŵa maganizo ofuna kukonzekera kuchita zoipa.
11
Ndipo udzanena kuti, ‘Ndikukathira nkhondo dziko la midzi yopanda malinga. Ndipita kwa anthu amene amakhala mwamtendere, amene satchinjirizidwa ndi malinga kapena zitseko kapena mipiringidzo.
12
Ndikukaŵalanda chuma chao ndi kufunkha zinthu zao. Ndikukathira nkhondo anthu okhala m'mizinda imene kale inali mabwinja. Ndidzalimbananso ndi anthu amene adasonkhana kuchokera ku maiko ambiri. Anthuwo ali ndi zoŵeta ndi katundu wochuluka, ndiponso amakhala pakatikati pa dziko lapansi.’
13
Anthu a ku Sheba ndi ku Dedani, ndiponso amalonda a ku Tarisisi ndi midzi yake yonse, adzafunsa kuti, ‘Kodi kutereku, ukudzafunkha? Kodi wasonkhanitsa gulu lako lankhondo kudzanyamula zofunkha, kudzatenga siliva ndi golide, kudzalanda ziŵeto ndi katundu, kuti zikhale zofunkha zochuluka?’
14
“Nchifukwa chake, iwe mwana wa munthu, ulalike ndipo uuze Gogi kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pa nthaŵi imene anthu anga Aisraele adzakhale mwamtendere, udzanyamuka.
15
Udzachokera kwanu ku mbali zakutali kumpoto, pamodzi ndi mitundu yambiri ya anthu, onsewo okwera pa akavalo, gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu.
16
Udzabwera kudzalimbana ndi anthu anga Aisraele, ngati namondwe woononga dziko lapansi. Masiku amenewo iwe Gogi ndidzakuyambanitsa ndi dziko langa kuti anthu a mitundu yonse adzandidziŵe, pamene ndidzaonetse kuyera kwanga pa zimene ndidzakuchite iweyo Gogi.
17
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Kodi iwe si ndiwe amene ndidalankhula za iwe masiku amakedzana, kudzera mwa atumiki anga aneneri a ku Israele? Pa zaka zambiri iwo ankalengeza kuti ndidzautsa iwe kuti udzalimbane ndi Aisraele.
18
Pa nthaŵi imeneyo, pamene Gogi adzabwera kudzalimbana ndi dziko la Israele, mkwiyo wanga udzayaka zedi. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
19
Chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanga woyakawo, ndikulumbira kuti kudzachita chivomezi chachikulu m'dziko lonse la Israele.
20
Nsomba za m'nyanja ndi mbalame zamumlengalenga, nyama zakuthengo ndi zokwaŵa zonse, pamodzi ndi anthu onse okhala pa dziko lapansi, zonsezo zidzanjenjemera ndi mantha. Mapiri adzaphwanyika, magomo adzanyenyeka, ndipo makoma onse adzagwa pansi.
21
Gogi ndidzamuutsira nkhondo kuchokera ku mapiri anga onse. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Anthu a Gogiyo adzaphana okhaokha ndi malupanga.
22
Ndidzamulanga ndi mliri ndi imfa. Ndidzagwetsa mvula yoopsa ndi matalala ndiponso sulufure ndi miyala yamoto pa iye, pa magulu ake ankhondo ndiponso pa mitundu yonse ya anthu omperekeza.
23
Umu ndimo m'mene ndidzaonetsere kuti ndine wamphamvu ndi woyera. Choncho ndidzadziŵika kwa anthu a mitundu yonse. Tsono adzadziŵadi kuti Ine ndine Chauta.”
← Chapter 37
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 39 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48