bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 19
Ezekiel 19
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 20 →
1
Chauta adandiwuza kuti, “Tsono iwe, uimbe nyimbo yamadandaulo, kuimbira akalonga aŵiri aja a ku Yerusalemu. Mau ake unene kuti:
2
“ ‘Mai wako anali ngati mkango waukazi pakati pa mikango yaimuna. Ankagona pakati pa mikango yaimuna akulera ana ake.
3
Adalera mmodzi mwa ana ake, ndipo mwanayo adasanduka mkango. Udaphunzira kugwira nyama, nuyamba kudya anthu.
4
Tsono mitundu ya anthu idachenjezana za mkangowo, ndipo tsiku lina udagwa m'mbuna yao. Adaukoka ndi ngoŵe kupita nawo ku dziko la Ejipito.
5
Mai uja ataona kuti mwana ankamukhulupirirayu wagwidwa, adakuzanso wina mwa ana ake, namsandutsa mkango wamphamvu.
6
Unkayendayenda pakati pa mikango inzake, pakuti unali mkango wokhwima. Udaphunzira kugwira nyama, nuyamba kudya anthu.
7
Udagwetsa malinga ao, ndipo udaononga mizinda yao. Onse a m'dzikolo adachita mantha chifukwa cha phokoso la kubangula kwake.
8
Tsono mitundu ya anthu, makamaka a m'maiko ozungulira, adabwera kudzalimbana nawo. Adautchera ukonde, ndipo udagweradi m'mbuna yao.
9
Adaukoka ndi ngoŵe nauponya m'chitatanga. Adapita nawo kwa mfumu ya ku Babiloni, mfumuyo nkuuponya m'ndende. Choncho liwu lake silidamvekenso ku mapiri a ku Israele.
10
“ ‘Mai wako anali ngati mpesa m'munda wa mphesa wobzalidwa m'mbali mwa madzi. Udabereka bwino ndipo unali ndi nthambi zambiri, chifukwa panali madzi ambiri.
11
Unali ndi nthambi zolimba zoyenera kupangira ndodo zaufumu. Udatalika nusomphoka pakati pa zomera zina, ndipo unkaoneka bwino chifukwa cha kutalika kwake ndi kuchuluka kwa nthambi zake.
12
Koma adauzula mwaukali naugwetsa pansi. Udauma ndi mphepo yakuvuma, zipatso zake zidayoyoka, thunthu lake lidauma, mtengo wonse nkupserera ndi moto.
13
Tsono adauwokanso ku chipululu ku dziko louma, lopanda madzi.
14
Ndipo moto udayaka mumtengomo, nupsereza nthambi ndi zipatso zake. Motero ulibenso nthambi yolimba yoti nkupangira ndodo ya mfumu.’ ” Imeneyi ndi nyimbo yachisoni, ndipo yasanduka nyimbo yapamaliro.
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48