bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 37
Ezekiel 37
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 36
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 38 →
1
Mphamvu ya Chauta idandigwira, Mzimu wa Chauta udandinyamula nkukandikhazika pakati pa chigwa. Chigwacho chinali chodzaza ndi mafupa.
2
Chauta adandiyendetsa uku ndi uku pakati pa mafupawo. Mafupawo analitu ochuluka kwambiri m'chigwa chonsecho, ndipo anali ochita kuti gwaa kuuma kwake.
3
Tsono adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi mafupa ameneŵa angathe kukhalanso ndi moyo?” Ine ndidati, “Ambuye Chauta, ndi Inuyo amene mukudziŵa zimenezi.”
4
Apo adandiwuza kuti, “Alalikire mafupa ameneŵa, uŵauze mafupa oumawo kuti amve mau a Ine Chauta.
5
Unene kuti zimene Ine Ambuye Chauta ndikuŵauza mafupawo ndi izi: Ndidzauzira mpweya mwa inu, ndipo mudzakhalanso ndi moyo.
6
Ndidzakupatsani mitsempha ndi mnofu, nkukukutani ndi khungu. Ndidzauzira mpweya mwa inu, ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Tsono mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
7
Pamenepo ndidayamba kulalika monga momwe adandilamulira. Ndikulalika choncho ndidangomva kuti gogobedegogobede! Mafupa aja kuyamba kulumikizana.
8
Ine ndiyang'ane, ndidaona kuti pali mitsempha, kenaka mnofu ukuwonekanso, potsiriza nkubwera khungu pamwamba pake, koma munalibe mpweya mwa iwo.
9
Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, ulalike ndi kuuza mpweya mau a Ine Ambuye Chauta, akuti, ‘Mpweya iwe, bwera kuno, bwera kuchokera ku mphepo zinai, dzaŵauzire anthu ophedwaŵa, kuti akhalenso ndi moyo.’ ”
10
Motero ndidayamba kulalika monga adandilamulira. Tsono mpweya udaloŵa mwa iwo, ndipo akufa aja adakhala ndi moyo, naimirira. Linali gulu lalikulu kwambiri la ankhondo.
11
Kenaka Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, mafupa ameneŵa ndi Aisraele onse. Iwo amanena kuti, ‘Mafupa athu ndi ouma, chiyembekezo chathu chidataika, taonongekeratu.’
12
Nchifukwa chake uŵalalikire ndi kuŵauza kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Inu anthu anga, ndidzafukula manda anu, ndipo ndidzakutulutsanimo. Ndidzakubwezerani ku dziko la Israele.
13
Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzafukula manda anu ndi kukutulutsanimo, inu anthu anga.
14
Tsono ndidzaika mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo, pambuyo pake ndidzakukhazikani m'dziko lanu. Choncho mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndalankhula zimenezi, ndipo ndidzazichitadi. Ndikutero Ine Chauta.”
15
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
16
“Iwe mwana wa munthu, tenga ndodo, ulembepo kuti, ‘Ya Ayuda ndi Aisraele ogwirizana nawo.’ Tsono utenge ndodo ina, ulembepo kuti, ‘Ya Aefuremu, ndiye kuti fuko la Yosefe, ndi Aisraele ogwirizana nawo.’
17
Tsono utenge ndodo ziŵirizo ndi kuzilumikiza kuti zikhale ngati ndodo imodzi.
18
Anthu akwanu akakufunsa tanthauzo lake la zimenezi,
19
uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndili pafupi kutenga ndodo ya Yosefe, imene ili m'manja mwa Efuremu, pamodzi ndi Aisraele ogwirizana nawo, ndiilumikiza ndi ndodo ya Yuda kuti zikhale ndodo imodzi. Ndipo zidzakhaladi imodzi m'manja mwanga.
20
Ndodo zimene ukulembapozo zikadzakhala m'manja mwako, pamaso pa anthu onse,
21
pamenepo udzaŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndidzaŵaitana Aisraele kuchokera ku malo ao aukapolo pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku mphepo zinai ndi kuŵabwezera ku dziko lao.
22
Ndidzaŵasandutsa mtundu umodzi m'dzikomo, ku mapiri a Israele, ndipo adzakhala ndi mfumu imodzi yokha. Sadzakhalanso mitundu iŵiri ya anthu kapena kugaŵikana maufumu aŵiri.
23
Sadzadziipitsanso ndi mafano ao ndi zinthu zina zonyansa, kapena ndi zochimwa zao zina zilizonse. Ndidzaŵapulumutsa ku machimo ao onse, ndipo ndidzaŵayeretsa. Motero iwowo adzakhala anthu anga, ndipo Ineyo ndidzakhala Mulungu wao.
24
“Mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yao, motero onsewo adzakhala ndi mbusa mmodzi. Adzatsata malamulo anga, adzamvera mosamala malangizo anga.
25
Adzakhala m'dziko limene ndidapatsa mtumiki wanga Yakobe, kumene ankakhala makolo anu. Iwowo, pamodzi ndi ana ao ndi zidzukulu zao, adzakhala kumeneko mpaka muyaya. Ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mtsogoleri wao mpaka muyaya.
26
Ndidzachita nawo chipangano chamtendere. Chipangano chimenechi chidzakhala chao mpaka muyaya. Ndidzaŵakhazikitsa ndi kuŵachulukitsa, ndipo ndidzaika Nyumba yanga pakati pao mpaka muyaya.
27
Nyumba yanga idzakhala pakati pao. Ineyo ndidzakhala Mulungu wao, ndipo iwowo adzakhala anthu anga.
28
Apo anthu a mitundu ina adzadziŵa kuti Ine Chauta Aisraele ndimaŵasandutsa oyera, chifukwa chakuti Nyumba yanga ili pakati pao mpaka muyaya.”
← Chapter 36
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 38 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48