bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 16
Ezekiel 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 17 →
1
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, umuwonetse Yerusalemu makhalidwe ake onyansa.
3
Umuuze kuti, Ambuye Chauta akukuuza kuti, ‘Kanani ndi dziko la makolo ako, ndipo udabadwira kumeneko. Atate ako anali Mwamori, amai ako anali Muhiti.
4
Ndipo utabadwa adakuchita izi: sadadule ntchofu yako, sadakusambitse m'madzi kuti akuyeretse. Sadakuthire mchere monga kudayenera, ndipo sadakukulunge m'nsalu.
5
Palibe ndi mmodzi yemwe amene adakusamala kapena kukumvera chisoni chokwanira kuti akuchitire zimenezi. Koma adakutaya panja poyera, chifukwa adaanyansidwa nawe pa tsiku limene udabadwa.
6
“ ‘Ndiye Ine nditabwera, ndidakuwona ukuvimvinizika m'magazi ako. Ndidalankhula nawe uli m'magazi momwemo ndi kukuuza kuti, “Ukhale ndi moyo,
7
ndipo ukule ngati mbeu ya m'munda.” Udakuladi, ndipo udatalika nkutha msinkhu. Maŵere adayamba kumera, tsitsi lako lidayamba kutalika. Komabe unali wamaliseche ndi wausiŵa.
8
“ ‘Nditabweranso, ndidaona kuti nthaŵi yako yomanga banja idakwana. Tsono ndidakufunditsa mwinjiro wanga ndi kubisa maliseche ako. Ndidachita nawe chipangano chaukwati, ndipo udasanduka wanga. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
9
“ ‘Tsono ndidakusambitsa m'madzi ndi kukutsuka magazi ako, ndipo ndidakudzoza mafuta.
10
Ndidakuveka zovala zopetapeta ndi nsapato zachikopa. Ndidakupatsa nsalu zabafuta ndi kukuveka zovala zasilika.
11
Ndidakukongoletsa ndi zamakaka, nkukuveka zigwinjiri m'manja, ndi mkanda m'khosi mwako.
12
Ndidakuveka chipini pa mphuno. Ndidakuika nsapule ku makutu ndi chisoti chaufumu chokongola kumutu kwako.
13
Motero udavaladi zokongoletsa zagolide ndi zasiliva. Zovala zako zinali za bafuta wosalala, zasilika ndi za nsalu zopetapeta. Unkadya ufa wosalala, uchi ndi mafuta a olivi. Udakula mokongola zedi, ndipo udasanduka mfumukazi.
14
Mbiri ya kukongola kwako idawanda pa dziko lonse lapansi, chifukwa choti ulemerero umene ndidakuveka nawo udakukongoletsa kwambiri. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
15
“ ‘Koma udadzitama nako kukongola kwako ndi kutchuka kwako, ndipo udayamba kuchita zadama. Unkachita chigololo, kumangodzipereka kwa aliyense amene wabwera.
16
Udatengako zovala zako zina nukakongoletsera akachisi akoako, ndipo kumeneko unkakachitirako zigololo. Zotere sizinachitikepo, ndipo sizidzachitikanso.
17
Udatenganso zokongoletsera, zopangidwa ndi golide wanga ndi siliva wanga, zimene ndidakupatsa, ndipo udapangira mafano achimuna amene udachita nawo chigololo.
18
Mafanowo udaŵaveka zovala zako zopetapeta, ndipo udapereka mafuta anga ndi lubani wanga kwa iwo.
19
Udatenga chakudya chimene ndidakupatsa, ufa, mafuta ndi uchi zimene ndinkakudyetsa, nuzipereka kwa iwo ngati nsembe za fungo lokoma. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
20
“ ‘Udatenga ana ako aamuna ndi aakazi amene udabalira Ine, nukaŵapereka ngati nsembe kwa mafano. Kodi zigololo zakozo sizidakukwanire,
21
apa ukupha ana anga ndi kuŵapereka kwa mafano ako?
22
Chifukwa cha zigololo zako zonyansazo, udaiŵala masiku a ubwana wako, pamene unali wamaliseche, wausiŵa ndi womangovimvinizika m'magazi ako.’ ”
23
Ambuye Chauta akuti, “Uli ndi tsoka, ndithu uli ndi tsoka, chifukwa kuwonjezera pa zoipa zako zonsezo,
24
udadzimangira nsanja pamodzi ndi guwa lake pa bwalo lililonse.
25
Udamanga nsanja zakozo pa mseu uliwonse. Pamenepo udanyazitsa kukongola kwako, podzipereka kwa aliyense wodutsapo. Wakhala ukuchita zigololo kosaŵerengeka.
26
Udachita zigololo ndi Aejipito adama oyandikana nawe, ndipo udandikwiyitsa chifukwa udachulukitsa zigololo zako.
27
Ndidakukantha ndi dzanja langa ndipo ndidakuchepetserako dziko lako. Ndidakupereka kwa adani ako, Afilisti, amene ankaipidwa ndi makhalidwe ako onyansa.
28
Chifukwa cha zilakolako zako udachitanso chigololo ndi Aasiriya.
29
Pambuyo pake udapitirira kuchita chigololo ndi Ababiloni, anthu a m'dziko lokonda lamalonda. Komabe sudakhutire nazo.”
30
Ambuye Chauta akunena kuti, “Mtima wako ndi wofooka kwambiri chifukwa udachita zonsezo monga ngati mkazi wadama wopanda manyazi.
31
Udamanga nsanja ndi guwa lake pa mseu uliwonse ndiponso kachisi pa bwalo lililonse. Koma iweyo sunkachita monga amachitira adama ena, chifukwa sunkachitira malipiro.
32
Mkazi wadama iwe, unkakonda amuna achilendo kupambana mwamuna wako.
33
Amuna amapereka ndalama kwa akazi onse adama. Koma iwe zibwenzi zako zonse unkazipatsa mphatso. Potero unkazinyengerera kuti zizibwera kuchokera mbali zonse kudzagona nawe.
34
Choncho udaali wosiyana ndi akazi ena pochita zadama, chifukwa panalibe amene ankakunyengerera kuti uchite naye chigololo. Iweyo ndiye amene unkapereka ndalama, osati ena kukupatsa ndalama ai. Motero unalidi wosiyana kwambiri ndi akazi ena.”
35
“Tsono mkazi wadama iwe, imva mau a Chauta.
36
Ambuye Chautawo mau ao ndi aŵa, Udavula mopanda manyazi, udaonetsa maliseche ako pochita zadama ndi zibwenzi zako ndi mafano ako, ndipo udapereka ana ako kuti aphedwe ngati nsembe zopereka kwa mafanowo.
37
Nchifukwa chake ndidzasonkhanitsa abwenzi ako amene unkasangalala nawo, ndiponso onse amene unkaŵakonda pamodzi ndi onse amene unkadana nawo. Ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku mbali zonse, nkukuvula pamaso pao, kuti iwowo adzaone thupi lako lonse lamaliseche.
38
Ndidzakulanga monga amalangira akazi achigololo ndiponso opha anthu. Chifukwa cha nsanje yanga ndidzakhetsa magazi ako mokwiya kwambiri.
39
Ndidzakupereka m'manja mwa abwenzi ako. Adzaononga nsanja zako ndi maguwa ako ndi kugwetsa akachisi ako aja. Adzakuvula zovala zako ndi kukukolopola zodzikongoletsera zako zabwinozo. Motero adzakusiya wamaliseche ndi wausiŵa.
40
Adzatuma gulu la anthu kuti akuponye miyala ndi kukudula pafupipafupi ndi malupanga ao.
41
Adzatentha nyumba zako, ndipo adzakulanga poyera, akazi ambiri akuwona. Ndidzathetsa dama lako, ndipo sudzazilipiranso zibwenzi zako.
42
Pamenepo ndidzaleka, ukali wanga udzatha, ndipo sindidzakuchitiranso nsanje. Ndidzakhala phee, osachitanso ukali.
43
Iwe udaiŵala masiku a ubwana wako, ndipo udandikwiyitsa ndi zinthu zonse zimene udachita. Nchifukwa chake Ine ndidzakubwezera pamutu pako chilango cha zimene udachitazo. Pajatu udaonjezera zigololo pa zonyansa zako zina zonse. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
44
“Iwe Yerusalemu, akuluakulu adzakuphera mwambi uwu wakuti, ‘Mwana watengera cha make.’
45
Ndiwedi mwana wa mai wako amene adadana ndi mwamuna wake ndi ana ake. Ndiwe mbale wa abale ako amene adadana ndi amuna ao ndiponso ana ao. Mai wako anali Muhiti, bambo wako anali Mwamori.
46
Mkulu wako ndi Samariya amene ankakhala cha kumpoto kwako pamodzi ndi midzi yake. Mng'ono wako amene ankakhala ndi midzi yake chakumwera kwako, ndi Sodomu.
47
Iwe sudakhutire nkutsata njira zao zoipa ndiponso kuchita zonyansa. Koma patangopita nthaŵi pang'ono chabe, unkachita zoipa kupambana iwowo.
48
Pali Ine ndemwe Chauta wamoyo, ngakhale mbale wako Sodomu ndi midzi yake sadachite monga m'mene iweyo wachitira pamodzi ndi midzi yako. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
49
Tchimo la mbale wako Sodomu linali lakuti iyeyo pamodzi ndi midzi yake ankanyadira chuma chake ndi chakudya chake chambiri, koma osalabadako zothandiza osauka ndi aumphaŵi.
50
Ankadzitukumula kwambiri namachita zonyansa zambiri pamaso panga. Nchifukwa chake ndidaŵachotsa monga m'mene waoneramu.
51
Ngakhale Samariya yemwe sadachite theka la machimo amene udachita iwe. Iweyo udachita zonyansa zambiri kupambana abale ako aŵiriwo, kotero kuti iwo amaoneka ngati osachimwa poyerekeza ndi iwe.
52
Tsopano mwiniwakewe uyenera kuchita manyazi ndi kunyozedwa, iwe amene waonetsa abale ako ngati osachimwa. Machimo ako ndi onyansa kwambiri kupitirira a abale ako, motero iwo aoneka ngati osalakwa. Iwenso tsono, amene udaonetsa abale ako ngati osachimwa, uchite manyazi ndi kunyozedwa.
53
“Koma ndidzadalitsanso Sodomu pamodzi ndi midzi yake. Ndidzachita chimodzimodzi ndi Samariya pamodzi ndi midzi yake. Pa nthaŵi yomweyo, nawenso Yerusalemu ndidzakudalitsa.
54
Choncho uchite manyazi ndi kunyozedwa, chifukwa udaonetsa abale akoŵa ngati angwiro.
55
Koma pamene mbale wako Sodomu pamodzi ndi midzi yake adzakhalanso monga momwe adaaliri kale, ndipo pamene mbale wako Samariya pamodzi ndi midzi yake adzakhalanso monga momwe adaaliri kale, nawenso ndi midzi yako udzakhalanso monga momwe udaaliri kale.
56
Kodi kale lija pamene iwe unkanyada, paja unkakonda kujeda mbale wako Sodomu,
57
kuipa kwako kusanadziŵike. Koma tsopano walingana naye posanduka chinthu chonyozeka kwa anthu a ku Edomu ndi kwa onse oyandikana nawo, ndiponso kwa Afilisti. Ndithu okuzungulira onsewo akukunyoza kwambiri.
58
Motero iwe uyenera kulangidwa chifukwa cha zigololo zako ndi makhalidwe ako onyansa. Ndikutero Ine Chauta.
59
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndidzakulanga potsata zimene udachita. Iwe udanyoza lumbiro lako pakuphwanya chipangano.
60
Komabe ndidzakumbukira chipangano chimene ndidachita nawe pa ubwana wako. Ndidzachita nawe chipangano china, chipangano chake chosatha.
61
Tsono udzakumbukira makhalidwe ako akale. Udzachita manyazi pamene udzalandiranso abale ako, wamkulu ndi wamng'ono yemwe. Ndidzaŵapereka kwa iwe kuti akhale ngati ana ako aakazi, ngakhale kuti iwowo sali nao m'chipangano changa ndi iwe.
62
Ndidzachita chipangano changa ndi iwe, ndipo udzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
63
Ndikadzakukhululukira zoipa zako zonse zimene udachita, udzazikumbukira ndipo udzachita manyazi kwambiri, kotero kuti sudzathanso nkulankhula komwe. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48