bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 26
Ezekiel 26
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 27 →
1
Pa chaka cha khumi ndi chimodzi cha ukapolo, tsiku loyamba la mwezi, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Tiro adanyodola Yerusalemu kuti, ‘Ha! Uja adaali chipata choloŵerapo mitundu ya anthuyu, waonongeka. Zipata zake zatitsekukira ife tsopano. Tilemera, poti iye tsopano wasanduka bwinja.’
3
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndikukukana iwe Tiro. Ndipo ndidzakubweretsera anthu a mitundu yambiri kuti adzalimbane nawe, monga momwe mafunde am'nyanja amaŵindukira.
4
Anthuwo adzaononga malinga a Tiro ndi kugwetsa nsanja zake. Ndidzapala dothi lake, ndi kumsandutsa thanthwe lambee.
5
Adzakhala malo oyanikapo kombe pakati pa nyanja. Mau anga ndi amenewo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Adzasanduka chofunkha cha anthu a mitundu ina.
6
Anthu a m'midzi yake yakumtunda adzaphedwa pa nkhondo. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
7
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Iwe Tiro ndidzakubweretsera Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mfumu ya mafumu, kuchokera kumpoto. Adzabwera ndi akavalo ndi magaleta, ndiponso okwera pa akavalo ndi gulu lalikulu lankhondo.
8
Anthu a m'midzi yako yakumtunda adzaŵapha pa nkhondo. Adzakuzinga ndi zithando zankhondo, ndiponso ndi ziwundo zankhondo. Adzakukwezera zishango kuti alimbane nawe.
9
Adzagwetsa malinga ako ndi makina ogumulira, ndipo adzagwetsa nsanja zako ndi nkhwangwa zake.
10
Akavalo ake ochuluka adzakukwirira ndi fumbi lao. Malinga ako adzagwedezeka ndi mdidi wa akavalo ndiponso ndi mkokomo wa mikombero ya magaleta poloŵa pa zipata zako, monga momwe zimachitikira poloŵa mu mzinda umene wagumulidwa.
11
Akavalo ake adzapondereza miseu yako yonse ndi ziboda zao. Anthu ako adzaŵapha ndi lupanga. Mizati yako yolimba adzaigwetsa.
12
Adzafunkha chuma chako ndi kulanda malonda ako. Malinga ako adzaŵagumula, ndipo nyumba zako zokongola adzazigwetsa. Miyala yako, mitengo yako ndi dothi lako lomwe adzaziponya m'nyanja.
13
Motero ndidzaletsa phokoso la nyimbo zako, ndipo kulira kwa apangwe ako sikudzamvekanso.
14
Ndidzakusandutsa thanthwe lambee. Udzasanduka malo okayanikapo kombe, ndipo sudzamangidwanso. Ine Chauta ndalankhula. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
15
“Zimene Ine Ambuye Chauta ndikukuuza iwe mzinda wa Tiro ndi izi: Nyanja idzagwedezeka pamodzi ndi zilumba, pakumva za kugwa kwako, ndiponso poona opweteka akubuula, ndipo anthu akuphedwa pakati pako.
16
Pamenepo mafumu onse akunyanja adzatsika pa mipando yao yaufumu. Mikanjo yao adzaiika pambali, ndipo adzavula zovala zao zopetapeta zija. Adzachita mantha nakhala pansi akunjenjemera kosalekeza, ndipo adzangoti pakamwa gwirire poona zimene zakugwera.
17
Apo adzayamba kuimba nyimbo yokudandaulira. Adzati, “ ‘Mzinda wotchuka iwe, nkuchita kuwonongeka chotere! Unali wamphamvu pa nyanja, iweyo ndi anthu ako. Iweyo ndi anthu ako munkaopsa anthu a m'mbali mwa nyanja.
18
Tsopano maiko a m'mbali mwa nyanja akunjenjemera chifukwa cha kugwa kwako. Nawonso okhala ku zilumba agwidwa ndi mantha chifukwa cha kutha kwako.’
19
“Mau a Ine Ambuye Chauta ndi aŵa: Ndidzakusandutsa bwinja, ngati mzinda umene munthu sangathe kukhalamo. Ndidzakuphimba ndi madzi ozama am'nyanja, madzi amphamvu oti akumize.
20
Ndidzakugwetsa pansi kuti ukhale pamodzi ndi anthu amvulazakale amene akutsikira ku manda. Ndidzakusunga kudzenjeko ngati ku bwinja losiyidwa kalekale, pamodzi ndi anthu amene adafa kale. Motero sudzakhalanso ndi anthu m'dziko la amoyo.
21
Ndidzakuthetsa mochititsa mantha, ndipo sudzakhalaponso. Ngakhale anthu adzakufunefune, sadzakupezanso. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 27 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48