bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 48
Ezekiel 48
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 47
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
1
“Naŵa maina a mafuko: kuyambira ku malire akumpoto kuchokera ku nyanja, kudzera ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamati, kukafika ku Hazarenoni, mzinda umene uli kumpoto kwa malire a Damasiko oyang'anana ndi Hamati, ndipo kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, nchigawo chimodzi, ndipo ncha Dani.
2
Kuchitana malire ndi Dani, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Asere.
3
Kuchitana malire ndi Asere kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Nafutali.
4
Kuchitana malire ndi Nafutali kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Manase.
5
Kuchitana malire ndi Manase kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Efuremu.
6
Kuchitana malire ndi Efuremu kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Rubeni.
7
Kuchitana malire ndi Rubeni kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Yuda.
8
Kuchitana malire ndi Yuda kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo chapadera ndithu. Muufupi mwake chikhale makilomita 12 ndi theka. M'litali mwake chikhale ngati zigawo zina, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe. Ndipo malo a Nyumba ya Chauta akhale pakati pake.”
9
“Chigawo chimene muchipatule kuti chikhale cha Chauta chikhale cha makilomita 12 ndi theka m'litali mwake, muufupi mwake chikhale cha makilomita khumi.
10
Chigawocho chigaŵidwe motere: chigawo cha Ansembe chikhale cha makilomita 12 ndi theka kumpoto. Kuzambwe chikhale cha makilomita khumi. Kuvuma chikhale cha makilomita asanu. Kumwera chikhale cha makilomita 12 ndi theka. Malo a Nyumba ya Chauta akhale pakatimpakati.
11
Chimenechi chikhale chigawo cha ansembe opatulika, ana a Zadoki, amene adamvera malamulo anga, osatsata Aisraele pamene adaasokera, monga m'mene adaachitira Alevi.
12
Chigawo chimenechi, pakati pa zigawo zonse, chidzakhale mphatso yapadera kwa ansembewo, ndipo chikhale chopatulika kwambiri. Chichitane malire ndi dziko la Alevi.”
13
“Tsono chigawo cha Alevi chikhale choyandikana ndi chigawo cha ansembe. M'litali mwake chikhale cha makilomita 12 ndi theka. Muufupi mwake chikhale cha makilomita asanu. Chigawo chonsechi m'litali mwake mukhale cha makilomita 12 ndi theka, ndipo muufupi mwake mukhale makilomita asanu.
14
Asagulitse kapena kusinthitsa mbali iliyonse ya chigawo chimenechi. Ndi chigawo chapadera ndithu ndipo asachipatse ena, pakuti ndi malo opatulikira Chauta.”
15
“Chigawo chotsala muufupi mwake chikhale cha makilomita aŵiri ndi hafu, m'litali mwake makilomita 12 ndi theka. Chikhale malo omangapo mzinda ndiponso busa. Mzinda ukhale pakatimpakati.
16
Miyeso yake ikhale iyi: Kumpoto kutalika kwake kukhale mamita 2,250. Kumwera kutalika kwake kukhale mamita 2,250. Kuvuma kutalika kwake kukhale mamita 2,250. Kuzambwe kutalika kwake kukhale mamita 2,250.
17
Dera la busa likhale motere: kumpoto kutalika kwake kukhale mamita 125. Kumwera kutalika kwake kukhale mamita 125. Kuvuma kutalika kwake kukhale mamita 125. Ndipo kuzambwe kutalika kwake kukhale mamita 125.
18
Chigawo chotsala pafupi ndi chigawo chopatulika, kutalika kwake makilomita asanu kuvuma, makilomita asanu kuzambwe. Chikhale dziko la minda ya anthu ogwira ntchito mu mzinda.
19
Anthu ogwira ntchito mu mzinda, ochokera m'fuko lililonse la Israele, ndipo azilima chigawocho.
20
Tsono chigawo chathunthu chopatulikacho chikhale cha makilomita 12 ndi theka mbali zonse, ndiye kuti chigawo chopatulikacho pamodzi ndi kadziko ka mzindawo.”
21
“Tsono chigawo chotsala pa mbali zonse ziŵiri za chigawo chopatulika ndi za kadziko ka mzinda, chikhale cha mfumu. Chidzayenda motere: kuyambira m'malire a chigawo chopatulika kukalekeza m'malire akuvuma, mbali ina kuyambiranso m'malire a chigawo chopatulika kukalekeza m'malire akuzambwe, kumapaza kufupi ndi zigawo za mafuko, dera lonselo likhale la mfumu. Chigawo chopatulika ndi malo oyera a Nyumba ya Mulungu zikhale pakatimpakati.
22
Chigawo cha Alevi ndi chigawo cha mzinda zikhale pakati pa dera la mfumulo. Dera limenelo lidzakhale pakatimpakati pa dziko la Yuda ndi la Benjamini.”
23
“Za mafuko ena otsala zidzayenda motere: kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe padzakhala chigawo chimodzi, chimenechi ncha Benjamini.
24
Kuchitana malire ndi Benjamini, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Simeoni.
25
Kuchitana malire ndi Simeoni, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Isakara.
26
Kuchitana malire ndi Isakara, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Zebuloni.
27
Kuchitana malire ndi Zebuloni, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Gadi.
28
Malire a Gadi mbali yakumwera ku Negebu achokere kumwera kuyambira ku Tamara mpaka ku Dziŵe la Meriboti-Kadesi, kenaka kuchokera ku Mtsinje wa ku Ejipito, kukafika ku Nyanja Yaikulu.
29
Dziko lonselo ndilo mupatse mafuko a Israele kuti likhale choloŵa chao. Zigawo zimenezi zidzakhala zao. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
30
“Aŵa ndiwo akhale makomo otulukira mu mzinda, ndipo atchulidwe maina a mafuko a Aisraele. Kumpoto, kumene kutalika kwake ndi kwa mamita 2,250,
31
kukhale zipata zitatu: chipata cha Rubeni, cha Yuda, ndi cha Levi.
32
Kuvuma, kumene kutalika kwake ndi kwa mamita 2,250, kukhale zipata zitatu: chipata cha Yosefe, cha Benjamini ndi cha Dani.
33
Kumwera, kumene kutalika kwake ndi kwa mamita 2,250, kukhale ndi zipata zitatu: chipata cha Simeoni, cha Isakara ndi cha Zebuloni.
34
Kuzambwe, kumene kutalika kwake ndi kwa mamita 2,250, kukhale zipata zitatu: chipata cha Gadi, cha Asere ndi cha Nafutali.
35
Choncho kutalika kwa mzindawo kuzungulira ponse kukhale mamita 9,000, ndipo dzina la mzindawo mpaka muyaya likhale ‘Chauta-ali-pano.’ ”
← Chapter 47
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48