bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 25
Ezekiel 25
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 26 →
1
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa anthu a ku Amoni, ulalike zoŵadzudzula.
3
Unene kuti, inu Aamoni, imvani mau a Ambuye Chauta akuti, ‘Paja mudatchula mau onyodola, mutaona malo anga opatulika akuipitsidwa, nthaka ya Israele itaguga, ndipo anthu a ku Yuda atatengedwa ukapolo.
4
Nchifukwa chake ndidzakuperekani m'manja mwa anthu akuvuma. Adzakhoma mahema ao ndi kumanga nyumba zao m'dziko mwanu. Adzakudyerani zipatso zanu, adzakumwerani mkaka wanu.
5
Ndidzasandutsa Raba kuti akhale busa la ngamira, ndipo ndidzasandutsa mizinda ya Aamoni kuti ikhale makola a nkhosa. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
6
Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Mudaomba m'manja ndi kulumphalumpha mokondwa, ndipo mudanyodola dziko la Israele ndi kulinyoza ndi mtima wonse.
7
Nchifukwa chake Ine ndidzakukanthani ndi dzanja langa ndipo ndidzakuperekani kuti mukhale chofunkha cha mitundu ina ya anthu. Ndidzakuchotsani pakati pa mitundu ina ya anthu, ndipo ndidzakufafanizani pa dziko lapansi. Ndidzakuwonongeranitu, ndipo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.’
8
“Mau a Ine Ambuye Chauta ndi aŵa: Chifukwa choti Mowabu adanena kuti a ku Yuda ali ngati anthu ena onse,
9
ndidzagumula mbali ina ya Mowabu, ndidzaononga mizinda yake yakumalire, ndiye kuti mizinda ija yokongola kwambiriyi ya Beteyesimoti, Baala-Meyoni ndi Kiriyataimu.
10
Ndidzapereka Amowabu pamodzi ndi Aamoni m'manja mwa mitundu yakuvuma, kotero kuti Aamoni adzaiŵalikiratu pakati pa mitundu ya anthu.
11
Amowabunso ndidzaŵalangadi. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
12
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Chifukwa choti Edomu adalipsira Yuda mwankhanza, adapalamula kwambiri pakutero.
13
Choncho Edomuyo ndidzamkantha ndi dzanja langa, ndipo ndidzaononga anthu pamodzi ndi nyama zomwe kumeneko. Dzikolo ndidzalisandutsa chipululu kuyambira ku Temani mpaka ku Dedani. Anthu ambiri adzaphedwa pa nkhondo.
14
Ndidzalanga Edomu ndi dzanja la anthu anga Aisraele. Adzamchita monga m'mene mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzafunire. Choncho adzaona kulipsira kwanga. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
15
“Mau a Ine Ambuye Chauta ndi aŵa: Afilisti adalanga anthu anga mwankhanza ndi kuŵalipsira ndi mtima wonyoza ndi wofuna kuŵaononga malinga ndi chidani chao chachikhalire.
16
Nchifukwa chake Afilistiwo ndidzaŵakantha ndi dzanja langa. Ndidzafafaniza Akereti ndi kuwononga ena onse okhala m'mbali mwa nyanja.
17
Ndidzaŵalipsira koopsa ndi kuŵalanga mwaukali kwambiri. Ndikadzaŵalanga choncho, adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 26 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48