bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 33
Ezekiel 33
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 34 →
1
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, uza anthu a mtundu wako zimene zimachitika ndikatumiza nkhondo m'dziko. Suja anthu am'dzikomo amasankha mmodzi pakati pao kuti akhale mlonda.
3
Iye akaona mdani akubwera, amaliza lipenga kuti achenjeze aliyense.
4
Wina akalimva lipengalo, koma osasamala, ndipo mdani akabwera nkumupha, wadziphetsa ndi mtima wake.
5
Wadziphetsa yekha chifukwa choti sadasamale chenjezo. Akadasamala, akadapulumuka.
6
Koma mlonda akaona mdani akubwera, iye osaliza lipenga kuti achenjeze anthu, tsono mdani nkubwera napha munthu wina, ngakhale kuti munthuyo wafera machimo ake, Ine ndidzamzenga mlandu mlonda uja chifukwa cha imfa ya mnzakeyo.
7
“Tsono iwe mwana wa munthu, ndakuika kuti ukhale mlonda wa Aisraele. Ukamva mau anga, uŵachenjeze.
8
Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Munthu woipa iwe, udzafa,’ iwe nupanda kumchenjeza kuti aleke makhalidwe oipa, kuti akhalebe ndi moyo, munthuyo adzafadi ali wochimwa, koma iweyo ndidzakuzenga mlandu chifukwa cha imfa yake.
9
Koma munthu woipa ukamchenjeza kuti asiye njira zake zoipa, iye nkupitiriza makhalidwe ake oipawo, adzafa ali wochimwa, koma iweyo udzapulumutsa moyo wako.
10
“Iwe mwana wa munthu, uŵakumbutse Aisraele mau ao akuti, ‘Talemedwa ndi machimo athu ndipo tikuwonda nazo zolakwa zimene tachita. Kodi tingakhale ndi moyo bwanji?’
11
Uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndithudi, pali Ine ndemwe, sindikondwa ndikaona munthu woipa alikufa. Ndikadakonda kuti aleke kuchimwako kuti akhale ndi moyo. Inu Aisraele, muferanji? Tembenukani, lekani zoipa zimene mukuchita.
12
“Tsono iwe mwana wa munthu, uza anthu ako kuti, Pamene munthu wochita chifuniro cha Mulungu achimwa, zabwino zimene adaachita sizidzampulumutsa. Woipa akaleka kuchimwa, sadzalangidwa. Ndipo munthu wochita chifuniro cha Mulungu akayamba kuchimwa, sadzatha kukhala ndi moyo chifukwa cha ntchito zake zabwino.
13
Ngakhale ndiwuze munthu wochita chifuniro cha Mulungu kuti adzakhala ndi moyo, ngati iye agonera pa zabwino zimene adaachita kale, nayamba kuchimwa, zabwino zake zonse zimene adaachitazo zidzaiŵalika. Adzafera zochimwa zakezo.
14
Chimodzimodzi ndikamchenjeza munthu wochimwa kuti adzafa, tsono iye nkuleka kuchimwako, namachita zolungama ndi zabwino,
15
monga kubweza chigwiriro chimene adatenga chifukwa cha ngongole, kubweza zimene adaba, kusiya zochimwa ndi kumasunga malamulo opatsa moyo, ndithu sadzafa, adzakhala ndi moyo.
16
Ndidzamkhululukira machimo ake amene adaachita. Chifukwa cha zabwino ndi zolungama zimene adachitazo, ndithu adzakhala ndi moyo.
17
“Komabe anthu a mtundu wako amati, ‘Zimene Chauta amachitazi nzopanda chilungamo.’ Iyai, koma makhalidwe ao ndiwo amene ali osalungama.
18
Munthu wabwino akaleka kuchita zabwino, nayamba kumachita zoipa, adzafa nazo.
19
Munthunso woipa, akaleka kuchimwa, namachita zolungama ndi zabwino, adzapulumutsa moyo wake.
20
Tsono inu am'banja la Israele, mumanena kuti, ‘Zimene Chauta amachitazi nzopanda chilungamo.’ Iyai, aliyense mwa inu Ine ndidzamuweruza potsata zochita zake.”
21
Pa tsiku lachisanu la mwezi wakhumi, chaka cha khumi ndi chiŵiri cha ukapolo wathu, munthu amene adapulumuka ku Yerusalemu, adabwera kudzandiwuza kuti mzinda wagwa.
22
Madzulo, iyeyo asanabwere, ndidaagwidwa ndi mphamvu za Chauta. Koma m'maŵa mwake, munthuyo atafika, Chauta adandibwezera mphamvu zolankhulira, ndipo sindinalinso bububu.
23
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
24
“Iwe mwana wa munthu, anthu amene akukhala m'mizinda yamabwinja ku dziko la Israele, akunena kuti, ‘Abrahamu anali munthu mmodzi yekha, ndipo adamupatsa dziko lonse. Koma ife tilipo ambiri, motero tsopano dzikolo ndi lathu.’
25
Tsono uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, ‘Mumadya nyama pamodzi ndi magazi omwe. Mumapembedza mafano, mumapha anthu. Kodi tsono dzikolo nkudzakhaladi lanu?’
26
Mumadalira malupanga anu. Mumachita zonyansa, ndipo aliyense amachita chigololo ndi mkazi wa mnzake. Kodi dzikolo nkudzakhaladi lanu?
27
Uŵauze kuti, Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pali ine ndemwe wamoyo, anthu amene adatsala m'mizinda yamabwinja, adzaphedwa ndi lupanga. Amene adatsala m'midzi, ndidzaŵapereka ku zilombo kuti ziŵadye. Amene adabisala m'mapiri ndi m'mapanga, adzafa ndi mliri.
28
Dzikolo ndidzalisandutsa tsala ndiponso chipululu. Mphamvu zimene ankanyada nazo zidzatheratu. Mapiri a ku Israele adzasanduka thengo, kotero kuti munthu sadzadutsako.
29
Ndikadzalanga anthu chifukwa cha zonyansa zimene adachita, ndi kusandutsa dzikolo kuti likhale tsala ndiponso chipululu, pamenepo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
30
“Koma kunena za iwe, mwana wa munthu, anthu a mtundu wako amalankhula za iwe, akamakumana pafupi ndi makoma a mzinda ndi pa makomo a nyumba zao. Amauzana kuti, ‘Tiyeni tsopano tikamve zimene Chauta wanena.’
31
Anthu anga amadzasonkhana kwa iwe nakhala pansi kuti amve zimene iweyo unene. Koma akazimva, sazitsata zimenezo. Zokamba zao zimaonetsa chikondi, m'menemo mitima yao imangokonda phindu chabe.
32
Kwa iwowo sindiwe kanthu konse, ndiwe munthu wamba chabe womangoimba nyimbo zachikondi ndi liwu lokoma poimba zeze. Kumva amamva mau ako onse, koma saŵagwiritsa ntchito.
33
Koma zimene wanena zikadzachitikadi—ndipo zidzachitika kumene—apo adzadziŵa kuti pakati pao panalidi mneneri.”
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 34 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48