bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 24
Ezekiel 24
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 25 →
1
Pa tsiku lakhumi la mwezi wakhumi, chaka chachisanu ndi chinai cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, lemba dzina la tsiku lalero, lero lomwe lino. Lero ndilo tsiku limene mfumu ya ku Babiloni yazinga Yerusalemu ndi zithando zankhondo.
3
Uŵaphere mwambi anthu aupanduŵa. Uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, “ ‘Ikani mphika pa moto, ndipo muthiremo madzi.
4
Mumphikamo muikemo nthuli za nyama, nthuli zabwino kwambiri za mwendo wathako ndi mwendo wamwamba. Mudzazemo mafupa abwino.
5
Pa gulu la nkhosa musankhulepo nkhosa yabwino kwambiri, ndipo muike nkhuni pansi pa mphikawo. Madziwo aŵire, kenaka muphike nyama ija pamodzi ndi mafupa omwe’.
6
“Tsono zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Tsoka kwa mzinda wamagaziwe, tsoka kwa mphika wa dzimbiri lokangamira ndi losachoka. Mutulutsemo nthuli imodziimodzi, osasankhula.
7
Magazi amene adakhetsa mumzindamo akadali pakati pake, chifukwa adaŵataya pa thanthwe losalala osati pa dothi, kuti fumbi lingaŵafotsere.
8
Ndidaŵasiyadi magaziwo pa mwala wambee, kuti asafotsereke, chifukwa chofuna kuwonetsa mkwiyo wanga ndi kulipsira.
9
“Tsono Ine Ambuye Chauta ndikuti, Tsoka kwa mzinda wamagaziwo! Inenso ndidzayatsa chimulu chachikulu cha nkhuni.
10
Onjeza nkhuni, usonkhe moto, uphike nyama, uiphike bwino, utsanyule msuzi, ndipo upsereze mafupa.
11
Tsono uike pa makala mphika wopanda kanthuwo, kuti chitsulo chake chipse, kuchita kuti psuu. Zonyansa zake zonse zisungunuke, dzimbiri lichoke.
12
Koma nkuuyeretsa bwanji? Dzimbiri lake lidaloŵerera, silingathe kuchoka ngakhale ndi moto womwe.
13
Dzimbiri limeneli ndi zilakolako za dama lako, poti nditakutsuka sudayere. Tsono sudzayeranso mpaka mkwiyo wanga utakwaniratu pa iwe.
14
Ine Chauta ndalankhula zimenezi. Zilikudza ndipo ndidzazichitadi. Sindidzabwerera m'mbuyo, sindidzakulekerera kapena kukhululuka ai. Ndidzakulanga potsata makhalidwe ako ndi zimene udachita. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
15
Chauta adandipatsiranso uthenga uwu wakuti,
16
“Iwe mwana wa munthu, ndikulanda mwadzidzidzi mkazi wako amene amakukomera m'maso kwambiri. Koma usadandaule, usalire kapena kukhetsa misozi.
17
Udzume, koma m'chikatikati, usabume maliro. Nduŵira yako uvale ndithu, nsapatonso uvale. Usaphimbe kumaso kapena kudya chakudya cha olira.”
18
Choncho ndidalankhula ndi anthu m'maŵa, madzulo mkazi wanga nkumamwalira. M'maŵa mwake, ndidachita monga momwe adandilamulira.
19
Anthu adandifunsa kuti, “Bwanji osatifotokozera tanthauzo lake la zimene ukuchitazi? Kodi ukuchitiranji zotere?”
20
Ndidaŵayankha kuti, “Chauta adandipatsira uthenga uwu, adati,
21
‘Uza Aisraele mau anga akuti, Ndidzaipitsa Nyumba yanga imene mwakhala mukuinyadira kwambiri. Mumakondwa kwambiri poiwona, ndipo mumaikonda ndi mtima wonse. Ana anu aamuna ndi aakazi amene mudaŵasiya m'mbuyo, adzaphedwa ndi lupanga.’
22
Koma inu mudzachita monga ndachitira inemu. Simudzaphimba kumaso, kapena kudya chakudya cha anthu olira.
23
Nduŵira mudzavala ndithu ku mutu, nsapatonso mudzavala. Simudzalira maliro kapena kukhetsa misozi. Koma mudzavutika zedi chifukwa cha machimo anu, ndipo muzidzangodzumirana.
24
Tsono ine Ezekielene ndidzakhala chitsanzo kwa inu, mudzachita monga momwe ine ndachitira. Chauta akuti zimenezi zikadzachitika, mudzadziŵa kuti Iye ndi Ambuye Chauta.”
25
Pambuyo pake Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tsiku lina anthuŵa ndidzaŵachotsera linga lao limene ankakondwerera kukongola kwake, limene linkaŵakomera m'maso poliwona, limenenso ankaikapo mtima kwambiri. Ndidzaŵachotseranso ana ao aamuna ndi aakazi.
26
Pa tsiku limenelo wopulumuka adzabwera kudzakuuza zimenezo.
27
Pa tsiku lomwelo udzathanso kulankhula, choncho udzalankhula naye wopulumukayo, sudzakhalanso bububu. Motero udzakhala chizindikiro kwa iwo, ndipo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48