bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 7
Ezekiel 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 8 →
1
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Chauta ndikuuza dziko la Israele kuti chimalizo chili pafupi. Chimalizo chafika ku mbali zonse zinai za dziko.
3
Tsopano chimalizo chili pa iwe Israele. Mkwiyo wanga ndidzauthira pa iwe. Ndidzagamula mlandu wako potsata mayendedwe ako, ndipo ndidzakulanga chifukwa cha zonyansa zako.
4
Sindidzakumvera chifundo kapena kukuleka. Ndidzakulanga chifukwa cha machitidwe ako ndiponso chifukwa cha zonyansa zimene zili pakati pako. Pamenepo udzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
5
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Chiwonongeko chikubwera, chiwonongeko chotsatana nchinzake.
6
Chimalizo chafika, chimalizo chija chafika! Chakugwera, ndithu chabwera.
7
Inu anthu okhala m'dziko, chiwonongeko chanu chafika. Nthaŵi yafika, tsiku lili pafupi, tsiku lachisokonezo, osati lachimwemwe, ku mapiri.
8
Posachedwapa ndidzakukwiyirani, ndipo ukali wanga udzathera pa inu. Ndidzagamula mlandu wanu potsata makhalidwe anu, ndipo ndidzakulangani chifukwa cha zonyansa zanu zochuluka.
9
Sindidzakumverani chifundo kapena kukulekani ai. Ndidzakulangani potsata makhalidwe anu ndiponso chifukwa cha zonyansa zimene mumachita. Pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, amene ndakulangani.”
10
“Onanitu tsiku latsoka! Onanitu chikubwera! Chilango chanu chafika. Kunyada kwanu kwakakata, kudzitama kwanu kwaonekera poyera.
11
Ndeu zasanduka chilango cha kuipa kwao. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene adzatsale. Zinthu zao zidzatha, chuma chao chidzathanso, ndipo ulemerero wao womwe udzatha.”
12
“Nthaŵi yafika, tsiku layandikira. Wogula asakondwe, ndipo wogulitsa asamve chisoni, pakuti ukali wanga waŵagwera onse chimodzimodzi.
13
Wogulitsa sadzazipezanso pa moyo wake wonse zimene adagulitsa kwa wina, pakuti chilango chidzagwera onsewo, sichingasinthike. Chifukwa cha machimo ake, palibe aliyense amene adzapulumutsa moyo wake.
14
Lipenga lalira, ndipo onse akonzeka. Koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akupita ku nkhondo, pakuti mkwiyo wanga wagwera onse pamodzi.
15
“M'miseu akumenyana, m'nyumba muli mliri ndi njala. Anthu okhala ku midzi adzafa ndi nkhondo. Okhala m'mizinda adzafa ndi mliri ndi njala.
16
Ngati otsala adzapulumukepo, azikakhala ku mapiri, nkumalira ngati nkhunda. Aliyense azidzabuula chifukwa cha tchimo lake.
17
Manja onse adzalefuka, maondo adzangoti zii, kulobodoka ngati madzi.
18
Adzavala ziguduli, ndipo adzagwidwa ndi mantha. Adzakhala ndi nkhope zamanyazi, kumutu adzameta mpala.
19
Adzataya siliva wao m'miseu, ndipo golide wao adzamuwona ngati wonyansa. Siliva wao ndi golide wao sadzatha kuŵapulumutsa pa tsiku limene Chauta adzaonetse ukali wake. Chuma chaochi sichingaŵathandize kuthetsa njala, kapena kukhala okhuta, pakuti ndicho chidaŵagwetsa m'machimo.”
20
“Kale ankanyada chifukwa cha zodzikongoletsera zao zamakaka. Koma ankazigwiritsa ntchito popanga mafano onyansa. Nchifukwa chake zodzikongoletsera zaozo ndidzazisandutsa zoŵanyansa.
21
Ndidzazipereka kwa anthu akudza kuti azifunkhe. Anthu oipa kwambiri a pa dziko lapansi adzazilanda ndi kuziipitsa.
22
Ine ndidzaŵalekerera anthuwo, kuti adzaipitse malo anga okondedwa. Adzaloŵamo ngati mbala nkuipitsamo.
23
“Konzani maunyolo, popeza kuti anthu opha anzao achuluka m'dziko, mzinda wadzaza ndi ndeu.
24
Ndidzatuma mitundu ya anthu yoipa kwambiri kuti ilande nyumba zao. Amphamvu pakati panu kunyada kwao kudzaŵathera, pamene ndidzalole mitundu yachilendoyo kuti iwononge malo amene amapembedzerapo.
25
Pamene nkhaŵa idzaŵafikira, adzafunafuna mtendere, koma osaupeza.
26
Tsoka lidzatsatana ndi tsoka linzake, padzakhala mphekesera zosatha. Anthu adzafunafuna mneneri kuti aŵalosere zakutsogolo, adzasoŵa ansembe oŵaphunzitsa malamulo, ndipo akuluakulu sadzakhalanso ndi uphungu.
27
Mfumu idzalira, akalonga ake adzachita mantha. Manja a anthu am'dzikomo adzauma ndi mantha. Ndidzaŵalanga moyenerera machimo ao, ndidzaŵaweruza monga momwe iwowo adaŵeruzira anzao. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48