bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 18
Ezekiel 18
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 19 →
1
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Chifukwa chiyani anthu a ku Israelenu mumakonda kubwerezabwereza mwambi uja wakuti, ‘Nkhuyu zodya akulu zidapota ndi ana omwe?’
3
Ndithu, pali ine ndemwe wamoyo, mwambi umenewu simudzaunenanso ku Israele.
4
Moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa mwana ndi wanga, wa bambo ndi wanganso. Munthu amene wachimwa, ndiye amene adzafe.
5
“Tiyese kuti pali munthu wabwino amene amatsata malamulo ndi kuchita zabwino.
6
Iyeyo sadyera nao ku zitunda zachipembedzo. Sapembedza mafano a ku Israele. Saipitsa mkazi wa munthu wina. Sakhudza mkazi pamene ali wosamba.
7
Sazunza munthu wina aliyense, koma amabwezera wangongole chigwiriro chake. Saaba, amadyetsa anjala, ndipo amaveka ausiwa.
8
Sakongoza ndalama kuti apezepo phindu kapena kulandira chiwongoladzanja. Amadziletsa kuchita zoipa, ndipo sachita mokondera pogamula milandu ya anthu.
9
Amatsata malangizo anga, ndipo amamvera malamulo anga mokhulupirika. Munthu wotereyu ndi wolungama, adzakhala ndi moyo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
10
“Mwina munthu wotero nkubala mwana amene ntchito yake nkuba ndiponso kupha anthu.
11
Iye amachita zambiri zimene bambo wake sadachitepo. Amadyera nao ku zitunda zachipembedzo, amaipitsa mkazi wa munthu wina,
12
amazunza osoŵa ndi osauka. Amaba, sabwezera chigwiriro cha munthu wangongole. Amatembenukira ku mafano, namachita zonyansa.
13
Amakongoza kuti apezepo phindu, ndipo kuti alandire chiwongoladzanja. Kodi munthu wotereyu nkukhala ndi moyo? Ai ndithu, sadzakhala ndi moyo. Chifukwa adachita zoipa zonsezi, adzaphedwa, ndicho chilango chomuyenerera.
14
“Mwina mwake munthu woipa uja nkubala mwana amene aona machimo a bambo wake. Amaona, koma satsanzirako. Sadyera nao ku zitunda zachipembedzo.
15
Sapembedza mafano a ku Israele, saipitsa mkazi wa munthu wina,
16
sazunza munthu wina aliyense, satenga chigwiriro ndipo saaba. Koma amadyetsa anjala ndi kuveka ausiŵa.
17
Amakana kuchita zoipa, sakongoza kuti apezepo phindu kapena kuti alandire chiwongoladzanja. Amatsata malangizo anga ndi kumvera malamulo anga. Munthu woteroyo sadzafera zolakwa za bambo wake. Adzakhala ndi moyo.
18
Koma bambo wake, popeza kuti adachimwa pozunza anthu ena ndi kubera mbale wake ndiponso kuŵachita zoipa anansi ake, adzafera zoipa zakezo.
19
“Mwina mungathe kufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mwana salangidwa chifukwa cha zolakwa za bambo wake?’ Mwanayo adzakhala ndi moyo chifukwa choti nthaŵi zonse ankachita zolungama ndi zokhulupirika, ndipo ankamvera malamulo anga onse mosamala.
20
Munthu wochimwa ndiye amene adzafe, osati wina. Mwana sadzafera machimo a bambo wake, ndipo bambo sadzafera machimo a mwana wake. Munthu wabwino adzakolola zipatso za ubwino wake. Munthu woipa adzakolola zipatso za kuipa kwake.
21
“Munthu wochimwa akaleka machimo ake amene ankachita, namamvera malamulo anga onse, ndi kumachita zolungama ndi zokhulupirika, ndithudi ameneyo adzakhala ndi moyo, sadzafa.
22
Zoipa zake zonse zidzakhululukidwa. Adzakhala ndi moyo chifukwa cha ntchito zake zolungama.
23
Ine Ambuye Chauta ndikuti, Kodi imfa ya munthu woipa Ine ndimakondwera nayo? Iyai, koma ndikadakonda kuti woipa aleke njira zake zoipa ndi kukhala ndi moyo.
24
“Koma munthu wabwino akasanduka woipa, namachita zonyansa za mitundu yonse zimene anthu amachita, kodi munthu woteroyo nkukhala ndi moyo? Iyai, ntchito zake zonse zabwino sizidzakumbukika. Wapalamula, wachimwa, adzafa basi.
25
Koma inu mumati, ‘A! Zimene Ambuye amachitazi nzopanda chilungamo.’ Tamvani tsono Aisraele inu: Kani zochita zanga ndiye zosalungama? Kodi si zochita zanu zimene zili zosalungama?
26
Ngati munthu wabwino aleka kuchita zoyenera, namachita zoipa, adzafa chifukwa cha zoipa zakezo.
27
Komanso munthu woipa akaleka zoipa zake, namachita zoyenera, adzapulumutsa moyo wake.
28
Poti adazindikira kuipa kwa zolakwa zake, nazileka, ndiye kuti adzakhala ndi moyo, sadzafa.
29
Komabe Aisraele akunena kuti zochita za Ambuye nzosalungama. Pepani, Aisraele inu, ndinu amene mumachita zosalungama, osati Ine.
30
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Aisraele inu, aliyense mwa inu ndidzamuweruza molingana ndi ntchito zake. Lapani, tembenukani mtima, kuti machimo anu asakuwonongeni.
31
Tayani zoipa zanu zonse zakale zimene mudachimwira Ine. Mukhale ndi mtima watsopano ndi nzeru zatsopano. Nanga muferenji, inu anthu a ku Israele?
32
Sindikondwera nayo imfa ya munthu wina aliyense. Nchifukwa chake lapani, kuti mukhale ndi moyo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48