bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 11
Ezekiel 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 12 →
1
Mzimu wa Mulungu udandinyamula kupita nane ku chipata chakuvuma cha Nyumba ya Chauta. Poloŵerapo panali anthu 25, ndipo pakati pa anthuwo ndidaona atsogoleri aŵa a anthu: Yazaniya mwana wa Azuri, ndi Pelatiya mwana wa Benaya.
2
Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu aŵiri ameneŵa ndiwo amene amapangana zoipa nkumalangiza anthu zoipa mumzinda muno.
3
Iwo amati, ‘Nthaŵi sinafike yoti nkumanga nyumba. Mzindawu uli ngati mphika umene uli pa moto, ifeyo tili ngati nyama imene ili mumphikamo.’
4
Tsono iwe mwana wa munthu, ulose moŵadzudzula, ulose ndithu.”
5
Pamenepo Mzimu wa Chauta udandigwira, ndipo udandiwuza kuti, “Unene kuti zimene akunena Chauta ndi izi, akuti, ‘Inu a m'banja la Israele, ndikudziŵa zimene zili mumtima mwanu.
6
Mwakhala mulikupha anthu ambiri mumzinda muno, ndipo mwaunjika mitembo yao m'miseu.’
7
“Nchifukwa chake Ambuye Chauta akunena kuti, ‘Mitembo ya anthu ophedwa imene mwaika kumeneko, imeneyo ndiyo nyama. Mzindawu ndiwo mphika ndithu. Koma ndidzakutulutsanimo.
8
Mukuwopa lupanga, tsono ndidzakugwetserani lupangalo.
9
Ndidzakutulutsani mumzimdamo, ndidzakuperekani kwa anthu akudza kuti akulangeni.
10
Inunso mudzafa ndi lupanga, ndidzakulangani mpaka ku malire a Israele. Pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
11
Choncho mzindawo sudzakhalanso ngati mphika wokutetezani, ndipo simudzakhalanso ngati nyama yam'menemo ai. Ndidzakulangani mpaka ku malire a Israele.
12
Pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. Simudatsate malangizo anga, simudamvere malamulo anga. Koma mwakhala mukutsata malamulo a mitundu ya anthu okuzungulirani.’ ”
13
Pamene ndinkalosa, nthaŵi yomweyo Pelatiya mwana wa Benaya adafa. Tsono ndidadzigwetsa pansi chafufumimba nkufuula kuti, “Inu Ambuye Chauta, kodi mukufuna kuŵatheratu Aisraele onse otsala?”
14
Pambuyo pake Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
15
“Iwe mwana wa munthu, achibale ako, ndiye kuti abale ako, anzako a ku ukapolo, onse a m'banja la Israele, anthu okhala ku Yerusalemu akuŵanena kuti, ‘Onse aja amene adatengedwa ukapolo ali kutali ndi Chauta, dziko lino tsopano nlathu.’ ”
16
“Nchifukwa chake uza anzako a ku ukapolo kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndine amene ndidaŵatumiza kutali pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuŵabalalitsa ku maiko ambiri. Pakali pano ndikuŵasungabe kumaiko kumene adatengedwako.”
17
“Nchifukwa chake unene ndithu kuti Ine Chauta mau anga ndikuti, Ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera kwa anthu a mitundu inayo ndi kuŵasonkhanitsa pamodzi, kuchokera kumaiko kumene ndidaŵabalalitsa. Kenaka ndidzaŵapatsa dziko la Israele.
18
Akadzaloŵa m'dzikomo, azidzachotsamo mafano onse oipa ndi onyansa.
19
Ndidzaŵapatsa mtima watsopano, ndipo ndidzaika moyo watsopano mwa iwo. Ndidzachotsa mtima wouma ngati mwala mwa iwo, ndipo ndidzaŵapatsa mtima wofeŵa ngati mnofu.
20
Motero adzatsata malamulo anga, adzasunga ndi kumvera malangizo anga. Choncho adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao.
21
Koma amene mitima yao yazama m'zonyansa ndi zoipa zinazo, ndidzaŵalanga chifukwa cha zonse zimene adachita. Ndikutero Ine Chauta.”
22
Tsono akerubi aja adayamba kuuluka, mikombero ili m'mbali mwao, ndipo ulemerero woŵala wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pa iwo.
23
Ulemerero wa Chautawo udakwera ndi kusiya mzindawo, nukaima pa phiri chakuvuma kwake kwa mzindawo.
24
Pambuyo pake Mzimu wa Mulungu udandinyamula nukandifikitsa kwa akapolo ku dziko la Babiloni. Zonsezi zidachitika m'masomphenya, monga momwe Mzimu wa Mulungu udaandiwonetsera. Kenaka zinthu zimene ndinkaziwonazo zidayamba kuzimirira.
25
Ndipo ndidaŵasimbira akapolo zonse zimene Chauta adaandiwonetsa.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48