bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 32
Ezekiel 32
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 33 →
1
Pa tsiku loyamba la mwezi wa khumi ndi chiŵiri, chaka cha khumi ndi chiŵiri cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, imbira Farao, mfumu ya ku Ejipito, nyimbo yamaliro. Umuuze uthenga uwu wakuti: “Iwe umadziyesa mkango pakati pa mitundu ya anthu, koma uli ngati ng'ona. Umakhuvula m'mitsinje yako. Umavonongera madzi ndi mapazi ako, ndi kudetserera mitsinje.
3
Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndikadzasonkhanitsa pamodzi anthu a mitundu yambiri, ndidzakuponyera khoka ndipo iwowo adzakugwira m'kombe mwanga.
4
Ndidzakuponya ku mtunda ndi kukutaya pansi. Ndidzabweretsa mbalame zamumlengalenga kuti zidzatere pa iwe, ndiponso zilombo za m'dziko lonse kuti zidzakudye.
5
Nyama yako ndidzaiyanika pa mapiri, ndipo zigwa zidzadzaza ndi zotsala zako.
6
Ndidzanyowetsa dziko ndi magazi ako, mpaka ku mapiri komwe, ndipo mitsinje idzadzaza ndi nyama yako.
7
Ndikadzakuwononga, ndidzaphimba thambo, ndipo ndidzadetsa nyenyezi. Ndidzaphimba dzuŵa ndi mtambo, ndipo mwezi sudzaŵala.
8
Ndidzazimitsa zoŵala zonse zamumlengalenga, ndipo dziko lako ndidzalichititsa mdima. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
9
“Ndidzavutitsa mitima ya anthu a mitundu yambiri, pamene ndidzakupititsa ku ukapolo pakati pa mitundu ina, ku maiko amene sudaŵadziŵe.
10
Ndidzadabwitsa anthu ambiri ndi zimene zidzakugwere. Mafumu ao adzanjenjemera pokumbukira iwe, nditaŵaonetsa lupanga langa. Pa tsiku la kugwa kwako, aliyense adzadera nkhaŵa moyo wake.
11
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni idzakufika.
12
Ndidzagwetsa gulu lako lonse lankhondo ndi malupanga a asilikali oopsa kwambiri kupambana a mitundu ina yonse. “Adzathetsa kunyada kwa Ejipito, ndipo gulu lake lonse lankhondo lidzaonongeka.
13
Ndidzaononga ziŵeto zao zonse zokhala pambali pa madzi am'dzikomo. Kumadziko sikudzaonekanso phazi la munthu, ndipo phazi la nyama silidzavonongeranso madzi.
14
Pambuyo pake ndidzayeretsa madzi akumeneko, ndipo mitsinje idzayenda mokometsera ngati mafuta. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
15
Ejipito nditamsandutsa bwinja, ndipo dziko lonse nditaliwononga, nditapha onse okhala kumeneko, adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
16
“Mau angaŵa adzakhala nyimbo yamaliro, ndipo akazi a mitundu yachilendo adzaiimba, kuimbira Ejipito ndi gulu lake lonse lankhondo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
17
Pa tsiku la khumi ndi chisanu la mwezi woyamba, chaka cha khumi ndi chiŵiri cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
18
“Iwe mwana wa munthu, lira kwambiri chifukwa cha anthu ochuluka a ku Ejipito, ndipo uŵaloŵetse, pamodzi ndi anthu a m'maiko ena amphamvu, ku dziko la anthu akufa.
19
Uŵafunse kuti, ‘Kani ndinu okongola kupambana ena? Tsikirani ku manda pamodzi ndi ena onse osaumbalidwa.’
20
Aejipito adzagwa pakati pa anthu amene adaphedwa pa nkhondo. Lupanga nlosololasolola, iwowo adzaphedwa pamodzi ndi anthu ao ochuluka.
21
M'kati mwa manda atsogoleri amphamvu pamodzi ndi ogwirizana nawo azidzakambirana kuti, ‘Kani anthu osaumbalidwa aja, ophedwa pa nkhondo, afika kunsi kuno. Si aŵa agona apaŵa!’
22
“Komweko kuli Asiriya ndipo ankhondo ake onse ali m'manda omzungulira. Onsewo adaphedwa pa nkhondo.
23
Manda ao ali m'malo ozama kwambiri m'dziko la anthu akufa, ndipo manda ao adazungulira manda ake. Iwowo kale ankaopsa m'dziko la anthu amoyo, koma tsopano onsewo adafa, adaphedwa pa nkhondo.
24
“Komweko kulinso Elamu ndipo ankhondo ake onse ali m'manda omzungulira. Onsewo adaphedwa pa nkhondo. Anthuwo adatsikira ku manda ali osaumbalidwa. Iwowo kale ankaopsa m'dziko la anthu amoyo. Tsopano akuchita manyazi, pamodzi ndi amene ali m'manda.
25
Elamuyo amupangira malo ogonapo pakati pa anthu ophedwa, pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo, loikidwa momzungulira. Onsewo ndi osaumbalidwa, ophedwa pa nkhondo. Zoonadi, anthu amene kale ankaopsa m'dziko la anthu amoyo, tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali m'dziko la anthu akufa. Aikidwa pakati pa anthu ophedwa.
26
“Komwekonso kuli Meseki ndi Tubala. Ankhondo ao onse ali m'manda oŵazungulira. Anthuwo ndi osaumbalidwa, ndipo adaphedwa pa nkhondo. Iwowo kale ankaopsa m'dziko la anthu amoyo.
27
Sadaikidwe mwaulemu ngati ankhondo amphamvu amakedzana, amene adatsikira ku dziko la anthu akufa ndi zida zao zomwe zankhondo. Malupanga ao adaŵaika ku mitu yao, ndipo zishango zao adaphimbira mafupa ao. Kale anthu amphamvu ameneŵa ankaopsa m'dziko la anthu amoyo.
28
“Iwenso Farao, udzatswanyika ndipo udzagona pamodzi ndi anthu akufa osaumbalidwa, pamodzi ndi amene adaphedwa pa nkhondo.
29
Komweko kuli Edomu pamodzi ndi mafumu ake ndi akalonga ake onse. Ngakhale anali amphamvu, komabe adaikidwa m'manda. Akugona pamodzi ndi anthu osaumbalidwa, pamodzi ndi onse amene adatsikira ku dziko la anthu akufa.
30
“Komweko kulinso akalonga onse akumpoto, pamodzi ndi anthu onse a ku Sidoni, amene adatsikira ku dziko la anthu akufa mwamanyazi, pamodzi ndi ophedwa, ngakhale anali oopsa ndi mphamvu zao. Akugona osaumbalidwa pamodzi ndi ophedwa pa nkhondo. Kumeneko akuchita manyazi pamodzi ndi onse amene adatsikira kale ku dziko la anthu akufa.
31
“Farao akadzaona onseŵa, iye ndi magulu ake ankhondo adzathuza mtima pokumbukira kuchuluka kwa anthu ake amene adaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
32
Ndithudi ankaopsa m'dziko la anthu amoyo, koma iyeyo ndi magulu ake onse ankhondo adzaikidwa pamodzi ndi osaumbalidwa, pamodzi ndi onse ophedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 33 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48