bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 20
Ezekiel 20
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 21 →
1
Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu, chaka chachisanu ndi chiŵiri cha ukapolo, akuluakulu ena a ku Israele adabwera kudzapempha nzeru kwa Chauta. Tsono adakhala pansi pamaso panga.
2
Pamenepo Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
3
“Iwe mwana wa munthu, akuluakulu a ku Israele uŵauze mau anga akuti, Kodi mwabwera kudzapempha nzeru kwa Ine? Pali Ine ndemwe, sindilola zotere. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
4
“Iwe mwana wa munthu, kodi ukuvomera kudzaŵaweruza? Kodi udzagamula mlandu wao? Tsonotu uŵafotokozere zonyansa zonse zimene adachita makolo ao.
5
Pambuyo pake uŵauze mau anga akuti, Pa tsiku limene ndidasankhula Israele, ndidalumbira kwa zidzukulu za Yakobe, ndipo ndidadziwulula kwa iwo ku Ejipito. Ndidalumbira ndi kuŵauza kuti, ‘Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.’
6
Tsiku limenelo ndidalumbira kwa iwo kuti ndidzaŵatulutsa m'dziko la Ejipito, kupita nawo ku dziko limene ndidaŵapatsa, dziko lamwanaalirenji, lokongola kwambiri kupambana maiko ena.
7
Ndidaŵauza onse kuti aliyense ataye zonyansa zonse zimene ankasangalala nazo, ndipo asadziipitse ndi mafano a ku Ejipito. Ine ndine Chauta Mulungu wanu.
8
Koma adandipandukira, adakana kundimvera. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adasiya zonyansa zake zimene ankasangalala nazo. Palibe amene adasiya mafano a ku Ejipito. Tsono ndidaganiza zoŵaonetsa ukali ndi mkwiyo wanga ku Ejipito komwe.
9
Koma sindidachite zimenezo, kuti choncho dzina langa lilemekezeke, lisanyozeke pakati pa anthu a mitundu ina amene Aisraele ankakhala nawo. Paja ndinali nditaonetsa mphamvu zanga pamaso pa mitunduyo pakutulutsa Aisraele m'dziko la Ejipito.
10
“Ndidaŵatulutsadi ku Ejipito ndi kuŵatsogolera m'chipululu.
11
Ndidaŵapatsa malangizo anga kumeneko, ndi kuŵaphunzitsa malamulo anga, amene amakhalitsa moyo anthu oŵamvera.
12
Ndidaŵapatsanso masiku a Sabata kuti akhale ngati chizindikiro pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziŵe kuti Ine Chauta ndimaŵayeretsa.
13
Koma Aisraele adandipandukira m'chipululumo. Sadatsate malangizo anga ndipo adakana malamulo anga, amene amakhalitsa moyo anthu oŵamvera. Anthuwo adaipitsa kotheratu masiku anga a Sabata. Motero Ine ndidaganiza zoŵalanga mwaukali m'chipululu momwemo ndi kuŵaononga kotheratu.
14
Koma zimenezo sindidazichite, kuti choncho dzina langa lilemekezeke, lisanyozeke pakati pa anthu a mitundu ina amene adandiwona ndikutulutsa Aisraelewo ku Ejipito.
15
Kuwonjezera pamenepo, ndidalumbira kwa iwo m'chipululu nditakweza dzanja, kuti sindidzaŵaloŵetsa m'dziko limene ndinali nditaŵapatsa, dziko lamwanaalirenji, lokoma kwambiri kupambana maiko ena onse.
16
Paja adakana malangizo anga, sadamvere malamulo anga, ndipo adaipitsa masiku anga a Sabata. Mtima wao udakonda kutsata mafano ao.
17
Komabe ndidaŵamvera chisoni ndipo sindidaŵaononge ndi kuŵatheratu m'chipululu.
18
“Ndidalamula ana ao m'chipululu kuti asatsate malangizo a makolo ao, asamvere malamulo ao, kapena kudziipitsa ndi mafano ao.
19
Ndidati, ‘Ine ndine Chauta Mulungu wanu. Muzitsata malamulo anga, ndi kumvera malangizo anga.
20
Muzilemekeza masiku anga a Sabata ngati opatulika, kuti adzakhale ngati chizindikiro pakati pa Ine ndi inu. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta Mulungu wanu.’
21
“Koma ana ao nawonso adandipandukira. Sadatsate malangizo anga, sadamvere malamulo anga, amene amakhalitsa moyo anthu oŵamvera. Ndiponso adaipitsa masiku anga a Sabata. Tsono ndidaganiza zoŵalanga mokwiya ndi kuŵalipsira m'chipululu momwemo.
22
Koma sindidachite zimenezo, kuti choncho dzina langa lilemekezeke, lisanyozeke pakati pa anthu a mitundu ina amene adandiwona ndikutulutsa Aisraelewo ku Ejipito.
23
Ndidachita kulumbira m'chipululu nditakweza dzanja, kuti ndidzaŵabalalitsa pakati pa mitundu ya anthu ndi kuŵamwazira ku maiko akutali,
24
chifukwa sadamvere malamulo anga, adakana malangizo anga, adaipitsa masiku anga a Sabata, ndipo adapembedza mafano a makolo ao.
25
Kuwonjezera pamenepo ndidaŵapatsa malamulo amene sankaŵakomera, ndiponso malangizo amene sakadatha kupeza nawo moyo wabwino.
26
Ndidaŵalekerera kuti adziipitse ndi zopereka zao, makamaka pakupereka ana ao achisamba ngati nsembe zootcha. Ndidatero kuti ndiŵadetse nkhaŵa, ndipo kuti adziŵe kuti Ine ndine Chauta.
27
“Iwe mwana wa munthu, lankhula nawo tsono Aisraele, uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Makolo anu adandinyozanso poleka kundikhulupirira,
28
pamene ndidaŵaloŵetsa m'dziko limene ndidaachita kulumbira kuti ndidzaŵapatsa. Kulikonse kumene adaona chitunda chachitali ndi mtengo wogudira, kumeneko ankapereka nsembe ndi zopereka zao zondikwiyitsa. Kumeneko ankapereka nsembe za fungo lokoma, ndiponso nsembe zazakumwa.
29
Ndidaŵafunsa kuti, Kodi chitunda kumene mukupitako nchotani? Choncho dzina lake lakhala ‘Chitunda chachipembedzo’ mpaka lero.”
30
“Tsono uŵauze Aisraele kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Kodi mudzadziipitsa monga momwe makolo anu adachitira ndi kusokera popembedza milungu yao yonyansa?
31
Pamene mubwera ndi mphatso zanu, ndi kumapereka ana anu kuti akhale nsembe zopsereza, mumadziipitsa potumikira mafano anu ambirimbiri mpaka lero lino. Kodi Aisraele inu, ndingathe kukulolani bwanji kuti mulandire malangizo kwa Ine? Pali Ine ndemwe Chauta wamoyo, sindidzalola zoterezi.
32
Inuyo mukufuna kukhala ngati anthu a mitundu ina, ngati anthu a m'maiko ena amene amapembedza mitengo ndi miyala. Koma zimenezo sizidzachitika konse.
33
“Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pali Ine ndemwe wamoyo, ndidzakulamulani ndi dzanja langa lamphamvu, nditasamula mkono wanga ndili wokwiya kwambiri.
34
Ndi dzanja langa lamphamvu ndi mkono wanga wosamula kuwonetsa mkwiyo, ndidzakuchotsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndi kukusonkhanitsani kuchokera kumaiko kumene mudabalalikirako.
35
Ndidzakuloŵetsani m'chipululu choyenera akunja. Kumeneko ndidzakuimbani mlandu choonana maso ndi maso.
36
Ndidzakulangani monga momwe ndidalangira makolo anu ku chipululu cha ku Ejipito. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
37
“Ndidzakuŵerengani ndi ndodo ya mbusa, ndi kukuloŵetsani m'chigwirizano cha chipangano changa.
38
Ndidzakuchotserani anthu amene amandipandukira ndi kundichimwira. Ndidzaŵatulutsa m'dziko limene akukhalamolo, koma sadzapondamo m'dziko la Israele. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
39
“Koma inu Aisraele, zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Pitani nonsenu mukatumikire mafano anu! Koma ndithu ndikuti pambuyo pake mudzandimveranso, ndipo simudzaipitsanso dzina langa loyera popereka mphatso kwa mafano anu!
40
Zoonadi Aisraele onse adzanditumikira m'dziko mwaomo ku phiri langa lalitali, phiri loyera la ku Israele. Kumeneko ndidzaŵalandira moŵakomera mtima. Kumeneko ndidzayembekeza kulandira mitulo yao ndi mphatso zao zopambana, pamodzi ndi zopereka zao zopatulika.
41
Inu nomwe ndidzakulandirani ngati nsembe za fungo lokoma, nditakutulutsani pakati pa anthu a mitundu ina, ndi kukusonkhanitsani kuchokera kumaiko kumene mudabalalikira. Pamenepo ndidzaonetsa ungwiro wanga pakati pa inu, ndipo mitundu yonse ya anthu idzaona.
42
Apo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzakubwezerani kwanu ku dziko la Israele, dziko limene ndidachita kulumbira kuti ndidzapatsa makolo anu.
43
Kumeneko mudzakumbukira makhalidwe anu oipa ndi zonyansa zanu zonse zimene mudadziipitsa nazo. Ndipo mudzamva nyansi ndi inu nomwe chifukwa cha zonse zimene mudachita.
44
Tsono inu a m'banja la Israele mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, pamene ndidzakuchitirani zabwino, osakumbukira makhalidwe anu oipa ndi ntchito zanu zopotoka, kuti choncho dzina langa lilemekezeke. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
45
Pambuyo pake Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
46
“Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyang'ane kumwera, ndipo ulalikire modzudzula anthu akumwera. Uliimbe mlandu dziko lankhalango lakumwera ku Negebu.
47
Uliwuze kuti, Chauta akuti mumvere mau ake, Iye akunena kuti, ‘Ndidzakuyatsa moto, ndipo motowo udzapsereza mitengo yako yonse youma ndi yaiŵisi yomwe. Malaŵi ake adzakhala osazimika, ndipo aliyense kuchokera kumwera mpaka kumpoto adzapsa nawo.
48
Anthu onse adzadziŵa kuti Ine Chauta ndine amene ndauyatsa motowo, ndipo sudzazimidwadi.’ ”
49
Tsono ndidati, “A! Inu Ambuye Chauta, anthu akundinena, akuti, ‘Suja amangonena nthano chabe ameneyu!’ ”
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48