bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 39
Ezekiel 39
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 38
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 40 →
1
“Iwe mwana wa munthu, ulalike zodzudzula Gogi. Umuuze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndikudana nawe iwe Gogi, kalonga wamkulu wa ku Meseki ndi ku Tubala.
2
Ndidzakuzunguza ndi kukupirikitsira m'tsogolo. Ndidzakutenga kuchokera ku maiko akutali kumpoto, ndipo ndidzakutuma kuti ukalimbane ndi anthu okhala m'mapiri a ku Israele.
3
Pambuyo pake ndidzathyola uta wa ku dzanja lako lamanzere, ndipo ndidzagwetsa mivi ya ku dzanja lako lamanja.
4
Udzagwa ku mapiri a ku Israeleko, iweyo pamodzi ndi magulu ako onse ankhondo ndi onse amene amakuthandiza. Ndidzakusandutsa chakudya cha miimba ndi cha zilombo zakuthengo.
5
Udzafera kuthengo, poti ndagamula choncho Ineyo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
6
Ndidzagwetsa moto pa dziko la Magogi ndi pa onse amene amakhala mwamtendere m'mbali mwa nyanja. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
7
Ndidzamveketsa dzina langa loyera pakati pa anthu anga Aisraele. Ndipo sindidzalola kuti dzina langa liipitsidwenso. Anthu a m'maiko onse adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndine Woyera uja wa ku Israele.
8
“Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndithu zilikudza, zidzachitikadi. Ndiye tsiku limene ndidanena lija.
9
Okhala m'mizinda ya Aisraele adzatuluka ndipo adzasonkhanitsa zida zankhondo zosiyidwa kuti azitenthe ngati nkhuni: ndiye kuti zishango ndi lihawo, mauta ndi mivi, zibonga ndi mikondo. Adzazisonkhere moto pa zaka zisanu ndi ziŵiri.
10
Sadzatolera nkhuni ku thengo kapena kusalika zina ku nkhalango. Moto wao azidzasonkha ndi zidazo. Motero adzafunkha oŵafunkha, ndipo adzabera oŵabera. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
11
“Pa tsiku limenelo Gogi ndidzampatsa malo a manda oti amuikemo ku dziko la Israele, m'chigwa cha anthu apaulendo, kuvuma kwa Nyanja Yakufa. Chigwacho chidzatsekera njira anthu odzera kumeneko, chifukwa Gogi ndi gulu lake lankhondo adzaikidwa kumeneko, ndipo chigwacho chidzatchedwa chigwa cha gulu lankhondo la Gogi.
12
Aisraele adzakhala akukwirira mitembo pa miyezi isanu ndi iŵiri, kuti ayeretse dziko.
13
Anthu onse am'dzikomo adzakwirira nao, ndipo ntchito imeneyo adzatchuka nayo pa tsiku limene ndidzaonetse ulemerero wanga. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
14
Miyezi isanu ndi iŵiri itapita, adzasankha anthu odzayendera m'dziko lonselo, kuti azifunafuna mitembo imene idatsalira ndi kumaikwirira, motero adzaliyeretseratu dzikolo.
15
Popita m'dzikomo, azidzati wina akaona fupa la munthu, azidzaika chizindikiro pambali pake, mpaka fupalo litakwiriridwa m'chigwa cha gulu lankhondo la Gogi.
16
Komwekonso kudzakhala mzinda wotchedwa Gulu lankhondo. Motero dzikolo lidzakhala loyeretsedwa.”
17
“Ndiye iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Chauta mau anga ndi aŵa: Uitane mbalame ndi nyama zonse zakuthengo, uziwuze kuti, ‘Sonkhanani mubwere kuno. Musonkhane kuchokera kumbali zonse. Mubwere ku phwando limene ndikukukonzerani ku mapiri a Israele. Phwando lake ndi lansembe. Kumeneko mudzadya nyama ndi kumwa magazi.
18
Mudzadya nyama ya ankhondo amphamvu, ndipo mudzamwa magazi a akalonga a dziko lapansi. Onsewo adaphedwa ngati nkhosa zamphongo, anaankhosa, mbuzi ndiponso ngati ng'ombe zamphongo zonenepa za ku Basani.
19
Ku phwando lansembe limene ndikukukonzeranilo, mudzadya zonona mpaka kukhuta, mudzamwa magazi mpaka kuledzera.
20
Zoonadi ku tebulo langa mudzakhuta podya akavalo ndi okwerapo ake, ankhondo amphamvu ndi asilikali amitundumitundu. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
21
“ ‘Ndidzaonetsa ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu yonse. Ndipo adzaona m'mene ndidzaŵalangire ndi dzanja langa, limene ndidzaŵasanjike.
22
Kuyambira tsiku limenelo mpaka m'tsogolo mwake, Aisraele adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta Mulungu wao.
23
Anthu a m'maiko onse adzadziŵa kuti Aisraele adaatengedwa ukapolo chifukwa cha machimo ao, chifukwa anali osakhulupirika kwa Ine. Choncho ndidaŵafulatira, ndipo ndidaŵapereka m'manja mwa adani ao. Motero onsewo adafa pa nkhondo.
24
Ndidaŵachita zimenezi chifukwa cha kunyansa kwao ndi machimo ao, ndipo ndidaŵafulatiradi.
25
“ ‘Tsono zimene Ine Ambuye Chauta ndikunena ndi izi: Tsopano a m'fuko la Yakobe ndidzaŵakhazikanso pabwino. Aisraelenso onse ndidzaŵachitira chifundo. Dzina langa loyera ndidzaliteteza.
26
Anthuwo akadzakhazikika mwamtendere m'dziko lao, popanda wina woŵavuta, pamenepo adzaiŵala zamanyazi zao zimene zidaŵagwera chifukwa chosandikhulupirira Ine.
27
Ndidzaŵabwezera kwao kuŵachotsa pakati pa mitundu ina ya anthu, ndi kuŵasonkhanitsa kuchokera ku maiko a adani aowo. Motero ndidzaonetsa pamaso pa mitundu yambiri ya anthu kuti ndinedi Woyera.
28
Choncho adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta Mulungu wao. Paja ndidaaŵatumiza ku ukapolo pakati pa mitundu ina ya anthu, kenaka ndidaŵabwezanso onse ku dziko lao, osasiyako ndi mmodzi yemwe.
29
Sindidzaŵafulatiranso, popeza kuti ndidzatumiza mzimu wanga kwa Aisraele. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.’ ”
← Chapter 38
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 40 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48