bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 12
Ezekiel 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 13 →
1
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu aupandu. Iwowo maso openyera ali nawo, komabe saona. Makutu omvera ali nawo, komabe saamva, chifukwa choti ngaupandu.
3
Tsono iwe mwana wa munthu, longedza katundu wako wopita naye ku ukapolo. Ndipo unyamuke ulendo wako masana ndithu, iwo akuwona, ukachite ngati wopita ku ukapolo kuchoka kwanu kupita ku chilendo, iwowo akuwona. Mwina mwake iwo nkumvetsa ngakhale ali aupandu.
4
Katundu wako wopita naye ku ukapolo umtulutse masana, iwo akuwona. Ndipo madzulo, iwo akuwona ndithu, uchoke kumudzi kwanu, monga ngati ukupita ku ukapolo.
5
Uboole dzenje pa khoma, iwo akuwona, ndipo utulukire pamenepo.
6
Usenze katundu wako pa phewa, iwo akuwona, ndipo upite kunja ku mdima. Uphimbe kumaso kotero kuti sungathe kuwona pansi, chifukwa ndakusandutsa chizindikiro chochenjeza anthu a m'banja la Israele.”
7
Ndidachita monga momwe adandiwuzira. Ndidatulutsa katundu wanga masana, nditammanga ngati wopita naye ku ukapolo. Madzulo ndidaboola khoma ndi manja. Pamene chisisira chinkayamba, ndidasenza katundu wanga pa phewa kutuluka naye, iwo akuwona.
8
M'maŵa mwake Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
9
“Iwe mwana wa munthu, kodi Aisraele, anthu aupandu aja, suja adakufunsa kuti, ‘Ukuchita chiyani?’
10
Uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Uthengawu ukunena za kalonga wa ku Yerusalemu ndiponso za banja lonse la Aisraele onse okhala kumeneko.
11
Uŵauze kuti iwe ndiwe chizindikiro choŵachenjeza. Zimene zakuchitikira iwe, zidzaŵachitikiranso iwowo. Adzatengedwa kupita ku ukapolo.
12
Kalonga wao adzasenza katundu wake nchisisira ndi kunyamuka. Adzatulukira pa dzenje limene anthu adaboola pa khoma, ataphimba kumaso kwake kuti asaone kumene akupita.
13
Koma ndidzayala ukonde pa iye ndi kumkola mu msampha wanga. Ndidzapita naye ku Babiloni, ku dziko la Akaldeya, komabe iye sadzalipenya, ndipo adzafera kumeneko.
14
Onse okhala naye pafupi, athandizi ake ndiponso ankhondo ake omwe, ndidzaŵabalalitsa ku mbali zonse zinai za dziko lapansi. Ndidzaŵalondola ndi lupanga losolola.
15
Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzaŵamwaza pakati pa mitundu yachilendo ndi kuŵabalalitsa ku maiko ambiri.
16
Koma ndidzasiyako oŵerengeka amene adzapulumuke ku nkhondo, njala, ndi mliri, kuti akafotokoze nkhani yonse ya zochita zao zonyansa pakati pa mitundu ya anthu kumene akupitako. Apo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
17
Pambuyo pake Chauta adandipatsiranso uthenga uwu wakuti,
18
“Iwe mwana wa munthu, ukamadya, uzinjenjemera. Ukamamwa, uzinthunthumira ndi mantha.
19
Anthu am'dzikomo uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta za anthu okhala ku Yerusalemu ndiponso m'dziko la Israele ndi izi: Anthuwo adzadya buledi mwamantha ndi kumwa madzi mwankhaŵa. Dziko lidzafunkhidwa kwathunthu chifukwa cha nkhondo za anthu onse okhala m'menemo.
20
Mizinda imene ili ndi anthu idzasakazika, ndipo dziko lidzasanduka chipululu. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
21
Mau a Chauta adandifika akuti,
22
“Iwe mwana wa munthu, kodi mwambi umene ukumveka m'dziko la Israelewu ukutanthauza chiyani? Mwambiwo ukuti, ‘Masiku akuchuluka, komabe zolosa sizikuchitika.’
23
Tsono uŵauze anthu kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndiwuthetsa mwambi umenewu, sudzamvekanso ku Israele. Koma nthaŵi ili pafupi yoti zonse zimene ndidakuululirani m'masomphenya zidzachitikedi.
24
Nthaŵi imeneyo sikudzakhalanso zinthu zina zonama zoziwona ngati kutulo. Sikudzakhalanso kuwombeza koshashalika pakati pa Aisraele.
25
Ine Chauta ndidzanena zimene ndidzafune, ndipo zidzachitikadi. Sipakhalanso zochedwa ai, koma masiku anu omwe ano, Ine ndidzalankhula kwa inu anthu aupandunu, ndipo ndidzazichitadi,” ndikutero Ine Ambuye Chauta.
26
Chauta adandipatsiranso uthenga uwu wakuti,
27
“Iwe mwana wa munthu, Aisraele akunena kuti zinthu zimene ukuziwona tsopano m'masomphenyazi sizidzachitika konse pa zaka zambiri. Akuti ukulosa zinthu za kutsogolo kwambiri.
28
Tsono uŵauze kuti, Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Zonena zanga sizidzachedwanso ai. Ndidzachitadi chilichonse chimene ndanena. Ndikutero Ine Chauta!”
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48