bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 44
Ezekiel 44
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 43
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 45 →
1
Munthu uja adapita nane ku chipata cha kunja kwa malo opatulika choyang'ana kuvuma. Chinali chotseka.
2
Tsono adandiwuza kuti, “Chipata ichi chikhale chotseka, osachitsekula. Wina asaloŵerepo ai, poti Ambuye, Mulungu wa Israele, waloŵerapo. Nchifukwa chake chizikhala chotseka.
3
Kalonga yekha angathe kukhala pamenepo ndi kumadya chakudya pamaso pa Chauta. Adzaloŵa ndi kutuluka kudzera m'khonde lam'kati la chipata chimenecho.”
4
Pambuyo pake munthuyo adandidzeretsa pa chipata chakumpoto ndipo tidafika kumaso kwa Nyumba ya Mulungu. Kumeneko ndidaona ulemerero wa Chauta utadzaza Nyumba yakeyo. Pamenepo ndidadzigwetsa chafufumimba.
5
Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, samala bwino, uyang'anitsitse ndipo umvetse bwino zonse zimene ndikuuze za malamulo ndi malangizo okhudza za Nyumba yangayi. Uzindikire bwino amene angaloledwe kuloŵa m'Nyumba ino ndiponso amene sayenera kuloŵamo.
6
Anthu a mtundu waupandu wa Israele uŵauze mau anga akuti, Aisraele inu, lekani zonyansa zanu zonse.
7
Mudaloŵetsa m'malo anga opatulika alendo osaumbalidwa mu mtima ndi m'thupi momwe. Anthuwo adaipitsa Nyumba yanga pamene inu munkandipatsa chakudya, mafuta ndi magazi omwe. Pochita zoipa zoterezi mudaphwanya chipangano changa.
8
M'malo moti muzisamala ndinu zinthu zanga zopatulika, mwasankha alendoŵa kuti aziyang'anira malo anga opatulika.
9
“Tsono zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Mwa alendo amene ali osaumbalidwa mu mtima ndi m'thupi, pasapezeke ndi mmodzi yemwe woloŵa m'malo anga opatulika, ngakhalenso alendo amene amakhala pakati pa Aisraele.
10
“Tsono Alevi amene adaandisiya kutali pa nthaŵi imene Aisraele adaasokera potsata mafano, adzalangidwa chifukwa cha kulakwa kwao.
11
Adzangokhala atumiki chabe ku malo anga opatulika. Adzayang'anira zipata za Nyumba ya Mulungu ndi kugwira ntchito zina zake kumeneko. Adzapha nyama za nsembe zopsereza, ndi za nsembe zina za anthu. Motero adzidzaimirira anthuwo ndi kumaŵatumikira.
12
Iwowo ankatumikira anthu popembedza mafano, ndipo adasokeretsa Aisraele potero. Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikulumbira ndithu kuti ameneŵa ayenera kulangidwa chifukwa cha zolakwa zao.
13
Saloledwa kudzafika pafupi ndi Ine, kuti anditumikire ngati ansembe. Sadzayandikira zinthu zanga zopatulika ndi zopereka zoyera kwambiri. Adzachititsidwa manyazi chifukwa cha ntchito zao zonyansa.
14
Komabe ndidzaŵaika kuti aziyang'anira Nyumba yanga ndi kutumikira pa ntchito zonse zoyenera kuchitika kumeneko.
15
“Koma ansembe a fuko la Levi a m'banja la Zadoki, amene adakhalabe okhulupirika pa ntchito zosamala malo anga opatulika nthaŵi imene Aisraele adaasokera ndi kundisiya Ine, okhawo adzasendera kwa Ine kuti anditumikire. Adzabwera kwa Ine kudzapereka nsembe za mafuta ndi magazi. Ndatero Ine Ambuye Chauta.
16
Iwo okhawo ndiwo adzaloŵe ku malo anga opatulika ndi kudzayandikira tebulo langa kuti anditumikire. Ndiwo amene adzasamalire zinthu zanga.
17
Pamene aloŵa ku chipata cham'kati, azivala bafuta. Asavale chovala chilichonse cha ubweya wankhosa ponditumikira pa zipata za bwalo lam'kati ndiponso m'kati mwa Nyumba yanga.
18
Azivala nduŵira zabafuta kumutu, ndi akabudula abafuta. Asavale chilichonse choŵachititsa thukuta.
19
Potulukira ku anthu a ku bwalo lakunja, azivula zovala zimene anavala potumikira m'kati, ndi kuzisiya m'zipinda zopatulika. Ndipo avale zovala zina, kuwopa kuti angapatsireko kuyera anthu enawo ndi zovala zaozo.
20
“Ansembewo asamete mpala kapena kuŵeta tsitsi lalitali kwambiri, koma azingoliyepula.
21
Wansembe asamwe vinyo pamene ali pafupi kuloŵa m'bwalo lam'kati.
22
Asakwatire mkazi wamasiye wamba kapena mkazi wosudzulidwa. Azikwatira namwali wosadziŵa mwamuna, ŵa fuko la Israele, kapena mkazi wamasiye wa wansembe mnzake.
23
“Ansembe aziphunzitsa anthu anga kusiyanitsa pakati pa zinthu zoyera ndi zinthu wamba, ndiponso pakati pa zinthu zoyenera ndi zosayenera kuperekera nsembe.
24
Pakakhala milandu, ansembe adzakhala oweruza, ndipo adzayenera kugamula milanduyo potsata malamulo anga. Atsate malamulo anga ndi malangizo anga pa za masiku anga onse achikondwerero. Adzasamalenso kuti masiku anga a Sabata akhale oyera.
25
“Wansembe asadziipitse pokhudza munthu wakufa, kupatula ngati ndi bambo wake kapena mai wake, mwana wake wamwamuna kapena wamkazi, mbale wake kapena mlongo wake wosakwatiwa.
26
Ngati aipitsidwa kenaka nkuyeretsedwa, adikire masiku asanu ndi aŵiri, kuti akhale woyeretsedwa kotheratu.
27
Tsono pa tsiku loti aloŵe m'bwalo lam'kati kuti akatumikire m'malo opatulika, apereke nsembe yopepesera machimo. Ndatero Ine Ambuye Chauta.
28
“Ansembe asadzakhale ndi choloŵa chilichonse ai. Choloŵa chao ndine. Ndipo musadzaŵapatse chuma mu Israele. Chuma chao ndine.
29
Iwo azidzadyako za chopereka cha zakudya, za nsembe zopepesera machimo, ndi za nsembe zopepesera kupalamula. Ndipo zonse zoperekedwa kwa Mulungu mu Israele zidzakhala zao.
30
Zopambana pa zonse zoyambirira kucha ndi pa zopereka zina zonse, zidzakhale za ansembe. Muzidzaŵapatsa ufa wanu umene mwayambirira kusinja, kuti choncho m'nyumba mwanu mukhale madalitso.
31
Kaya ndi mbalame kaya ndi nyama, ansembe asadye yofa yokha kapena yochita kujiwa.
← Chapter 43
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 45 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48