bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 46
Ezekiel 46
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 45
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 47 →
1
Zimene Ambuye Chauta akunena ndi izi, akuti, “Chipata chakuvuma cha bwalo lam'kati chizikhala chotseka masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito. Azitsekula pa tsiku la Sabata lokha ndi tsiku limene mwezi wakhala.
2
Mfumu poloŵa izidzera m'khonde lam'kati la chipata kuchokera kunja, nkudzaima pafupi ndi nsanamira yapakhomo. Ansembe apereke nsembe yake yopsereza ndi nsembe yachiyanjano. Mfumuyo ipembedze pachiwundopo, kenaka nkutuluka. Koma chipatacho asachitseke mpaka madzulo.
3
Anthu nawonso azipembedza pamaso pa Chauta pa khomo la chipata chimenecho pa masiku a Sabata ndiponso pa tsiku limene mwezi wakhala.
4
Nsembe yopsereza imene mfumu iyenera kupereka kwa Chauta ikhale motere: pa tsiku la Sabata azipereka anaankhosa asanu ndi mmodzi opanda chilema ndiponso nkhosa yamphongo yopanda chilema.
5
Pamodzi ndi nkhosa yamphongo iliyonse, mfumu izipereka ufa wokwanira efa imodzi. Pamodzi ndi anaankhosa aja mfumu iziperekanso ufa monga ingathere. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pa efa iliyonse ya ufa.
6
Pa tsiku limene mwezi wakhala mfumu ipereke mwanawang'ombe wamphongo wopanda chilema, anaankhosa asanu ndi mmodzi, ndi nkhosa yamphongo, zonsezo zopanda chilema.
7
Ipereke efa imodzi ya ufa pa ng'ombe yamphongo iliyonse, ndiponso efa ina pa nkhosa yamphongo iliyonse. Pa anaankhosa iperekenso ufa monga m'mene ingathere. Pamodzi ndi efa iliyonse ya ufa, ipereke hini imodzi ya mafuta.
8
Mfumu poloŵa, izidzera m'khonde lam'kati la chipata chakuvuma, nkutulukiranso pomwepo.
9
“Pa masiku achikondwerero, anthu am'dzikomo akabwera kudzapembedza Chauta, munthu woloŵera pa chipata chakumpoto azidzatulukira pa chipata chakumwera. Munthu woloŵera pa chipata chakumwera, azidzatulukira pa chipata chakumpoto. Munthu aliyense asadzatulukire pomwe waloŵera, koma azipita chakutsogolo.
10
Tsono mfumu izidzakhala pakati pao. Izidzaloŵa nthaŵi imene iwowo akuloŵa, nkutuluka nthaŵi imene iwowo akutuluka.
11
“Pa masiku achikondwerero ndi pa masiku ena osankhidwa, zopereka za ufa zikhale zokwanira efa imodzi pamodzi ndi ng'ombe yamphongo iliyonse, efa imodzinso pamodzi ndi nkhosa yamphongo iliyonse, koma pa mwanawankhosa azipereka monga m'mene angathere. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pamodzi ndi efa iliyonse ya ufa.
12
Pamene mfumu ikufuna kupereka zaufulu kwa Chauta, monga nsembe yopsereza kapena nsembe zachiyanjano, aitsekulire chipata chakuvuma. Ipereke nsembe yake yopsereza ndi nsembe yake yachiyanjano, monga m'mene imachitira pa tsiku la Sabata. Itamaliza, ituluke. Itatuluka, chipata chitsekedwe.
13
“Tsiku lililonse, nthaŵi yam'maŵa, azipereka kwa Chauta mwanawankhosa wa chaka chimodzi wopanda chilema.
14
Pamodzi ndi nyamayo aziperekanso m'maŵa mulimonse ufa wokwanira chimodzi mwa zigawo zisanu ndi chimodzi za efa. Aziperekanso chimodzi mwa zigawo zitatu za hini ya mafuta okandira ufa wosalala. Nsembe imeneyi yopereka kwa Chautayi iziperekedwa nthaŵi zonse.
15
Motero azipereka mwanawankhosa, ufa ndi mafuta m'maŵa mulimonse, kuti zikhale zopsereza tsiku ndi tsiku.”
16
Zimene Ambuye Chauta akunena ndi izi, akuti, “Kalonga akapereka chigawo cha chuma chake kwa mmodzi mwa ana ake, mphatsoyo ndi ya ana akewodi, popeza kuti ndi chigawo cha choloŵa cha makolo.
17
Koma akapereka mphatso yotere kwa mmodzi mwa atumiki ake, idzakhala ya mtumikiyo mpaka pa chaka cha ufulu. Pamenepo mphatsoyo idzabwerera kwa kalonga uja, chifukwa chuma chake chonse ncha ana okha.
18
Tsono kalonga asalande anthu gawo la chuma chaochao pakuŵachotsa m'dera lao la dziko. Ana ake kalonga aŵapatse choloŵa chao pa dziko limene lili lakelake, kuti choncho asalande ndi mmodzi yemwe mwa ana anga choloŵa chake.”
19
Pambuyo pake munthu uja adandidzeretsa pa khomo la pambali pa chipata nandiloŵetsa ku zipinda zopatulika za ansembe zoyang'ana kumpoto. Ndipo adandilozera malo chakuzambwe kwa zipindazo, nandiwuza kuti,
20
“Aŵa ndi malo m'mene ansembe azidzaphikiramo nyama za nsembe zopepesera kupalamula ndiponso nsembe zopepesera machimo. Kumenekonso ndiko kumene azidzaotcherako chopereka cha chakudya. Sadzatuluka nazo zoyerazi m'bwalo lakunja kuwopa kuti angapatsireko kuyera anthu enawo.”
21
Atatero adandiloŵetsa m'bwalo lakunja napita nane ku ngodya zinai za bwalolo. Tsono m'kati mwa ngodya iliyonse munali bwalo lina.
22
Motero pa ngodya zinai za bwalo lalikululo panali mabwalo ena ang'onoang'ono. Mabwalo amenewo anali ofanana, m'litali mwake mamita makumi aŵiri, muufupi mwake mamita khumi ndi asanu.
23
Kuzungulira mabwalo anai ang'onoang'onowo panali mpanda wamiyala, ndiponso malo osonkhapo moto, omangidwa m'munsi mwa mpandawo.
24
Tsono adandiwuza kuti, “Zimenezi ndizo zipinda zophikiramo, kumene anthu otumikira m'Nyumba ya Mulungu aziphikiramo nyama za nsembe za anthu.”
← Chapter 45
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 47 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48