bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 27
Ezekiel 27
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 28 →
1
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, uimbe nyimbo yodandaulira Tiro.
3
Uuze Tiro, mzinda wokhala pa dooko la nyanja, umene umachita malonda ndi anthu a mitundu yambiri ya ku maiko ambiri a m'mbali mwa nyanja, kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: “ ‘Iwe Tiro, wakhala ukunena kuti, “Ndine wokongola kwabasi.”
4
Malire ako ali m'kati mwenimweni mwa nyanja. Amisiri amene adakumanga, adakumanga ngati chombo chochititsa kaso zedi.
5
Adakupanga ndi matabwa a mitengo ya paini ya ku phiri la Seniri. Adatenga mkungudza ku Lebanoni kuti adzapangire mlongoti wako.
6
Adapanga nkhafi zako ndi mtengo wa thundu wa ku Basani. Adapanga thandala lako ndi matabwa a mitengo ya paini ya ku zilumba za Kitimu, pakati pa matabwawo panali zosema za minyanga ya njovu.
7
Thanga lako linali la nsalu yabafuta. Nsalu yake inali yopeta bwino, yochokera ku Ejipito, ndipo ndiyo inali ngati mbendera yako. Nsalu zophimba mahema ako zinali zobiriŵira ndi zofiirira, zochokera ku zilumba za Elisa.
8
Anthu a ku Sidoni ndi a ku Arivadi ndiwo amene ankakupalasa. Akatswiri ako, iwe Tiro, anali mwa iwe, ndiwo amene ankakuyendetsa.
9
Mwa iwe munalinso akuluakulu ndi akatswiri a ku Gebala, amene ankakonza ziboo zako. Amalinyero ambiri m'zombo zao ankadzakuyendera kuchokera ku maiko onse kudzachita nawe malonda.’
10
“Anthu a ku Persiya, a ku Ludi ndi a ku Puti adaloŵa m'gulu la ankhondo ako. Ankapachika zishango zao ndi zisoti m'kati mwako, ndipo potero ankakupatsa ulemerero.
11
Ankhondo a ku Arivadi ndi a ku Heleki ankalonda malinga ako ponse pozungulira. Anthu a ku Gamadi ankakwera pa nsanja zako, ndi kukapachika zishango zao pa malinga ako ponse pozungulira. Amenewo ndiwo amene ankakukongoletsa kwabasi.
12
“Dziko la Tarisisi linkachita nawe malonda chifukwa cha katundu wako wamtundumtundu, ndipo unkagulako siliva, chitsulo, chitini ndi mtovu, mosinthana ndi katundu wako.
13
Yavani, Tuba ndi Meseki ankachita nawe malonda. Ankakugulitsa akapolo ndi ziŵiya zamkuŵa mosinthana ndi katundu wako.
14
Anthu a ku Betetogarima ankapereka akavalo antchito, akavalo ankhondo ndi abulu mosinthana ndi katundu wako.
15
Anthu a ku Dedani ankachita nawe malonda, anthunso a m'mbali mwa nyanja ankakupatsa minyanga ya njovu ndi phingo mosinthana ndi katundu wako.
16
Anthu a ku Aramu ankagula zinthu zambiri zamalonda mosinthana ndi katundu wako wochuluka. Iwo ankapereka miyala ya emeradi, nsalu zofiirira, nsalu zopetapeta, nsalu zabafuta, korale ndi miyala ya rubi, mosinthana ndi katundu wako.
17
Yuda ndi Israele ankagula malonda ako. Iwo ankapereka tirigu, zipatso za olivi, nkhuyu zoyamba, ndiponso uchi, mafuta aolivi ndi zonunkhira zokometsera chakudya, mosinthana ndi katundu wako.
18
Anthu a ku Damasiko ankagula kwa iwe chifukwa cha kuchuluka kwa zamalonda zako ndi katundu wako wosiyanasiyana. Ankakugulitsa vinyo wa ku Heliboni ndi ubweya wa nkhosa wambee.
19
Ankaperekanso vinyo wa ku Uzala, ndiponso zitsulo zosalala, kasiya ndi bango lonunkhira, kusinthitsa ndi malonda ako.
20
Anthu a ku Dedani ankakugulitsa nsalu zoika pa zishalo za akavalo.
21
Arabiya ndi mafumu onse a ku Kedara ankachita nawe malonda mosinthana ndi ana a nkhosa, nkhosa zamphongo ndi mbuzi.
22
Amalonda a ku Sheba ndi a ku Rama ankagulanso kwa iwe. Ankapereka zonunkhira zabwino kwambiri, miyala ya mtengo wapatali ndi golide yemwe, mosinthana ndi katundu wako.
23
Mizinda iyi ya Harani, Kane, Edeni, Asuri ndi Kilimade inkachita nawe malonda.
24
Anthu akumeneko ankasinthitsana nawe zovala zabwino kwambiri, nsalu zofiirira, nsalu zopetapeta, makalipeti amaŵangamaŵanga, zonsezo atazimanga bwino ndi zingwe zolimba.
25
Zombo za ku Tarisisi zinkanyamula malonda ako. “Motero iweyo unali ngati chombo chapanyanja chodzaza ndi katundu wolemera.
26
Opalasa ako adakupititsa ku nyanja yozama, kumene mphepo yakuvuma idakukankhira nikumiza m'kati mwa nyanja.
27
Chuma chako, katundu wako ndi malonda ako, amalinyero ako ndi oongolera omwe, amisiri a matabwa a zombo zako ndiponso oyendetsa malonda ako, asilikali ako onse amene anali m'katimo, ndi gulu lonse lankhondo pakati pako, onsewo adamira m'nyanja tsiku limene udaonongeka.
28
Chifukwa cha kufuula kwa amalinyerowo, kumtunda kudagwedezeka.
29
Onse amene amapalasa chombo, atuluka m'zombo zao. Amalinyero onse ndi oongolera omwe aimirira ku mtunda.
30
Onsewo akukulira iweyo, kulira kwake kwambiri. Akudzithira fumbi kumutu, nkumamvimvinizika pa phulusa.
31
Akudzimeta mpala chifukwa cha iwe, ndipo akuvala ziguduli. Akulira ndi mitima yoŵaŵa.
32
Akukuimbira nyimbo yodandaula, akuti, ‘Ndani adaonongedwapo ngati Tiro, pakati pa nyanja?’
33
Pamene malonda ako ankaoloka nyanja, unkakondweretsa mitundu yambiri ya anthu pa zosoŵa zao. Mafumu a dziko lapansi adalemera nacho chuma chako.
34
Koma tsopano wathyokera m'nyanja, pansi penipeni pa nyanja. Kungoti iweyo, katundu wako ndi antchito ako onse, nonse mwathera pamodzi m'nyanja.
35
Aliyense amene amakhala m'mbali mwa nyanja waopsedwa nazo zimene zakuchitikira. Mafumu ao akuchita mantha, nkhope zao zasinthika ndi mantha.
36
Anthu amalonda a ku maiko ena akukunyodola tsopano. Watha mochititsa mantha, sudzakhalaponso mpaka muyaya.”
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 28 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48