bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 34
Ezekiel 34
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 35 →
1
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, ulengeze mau oimba mlandu abusa a Israele. Ulengeze, uŵauze kuti ‘Zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi: Tsoka kwa inu abusa a ku Israele, amene mumangodzisamala inu nokha. Kodi suja abusa amayenera kusamala nkhosa?
3
Chambiko mumadya, zaubweya mumavala, ndipo nyama zonenepa mumapha, koma nkhosa osasamala konse.
4
Nkhosa zofooka simudazilimbikitse, zodwala simudazichiritse, zopweteka simudazimange mabala ake, zosokera simudazibweze, ndipo zotayika simudazifunefune. Koma munkaziŵeta mozunza ndi mwankhalwe.
5
Ndiye zinkangoti balalabalala, poti panalibe mbusa. Motero zidasanduka chakudya cha zilombo zonse zakuthengo.
6
Nkhosa zanga zidamwazikana nkumangoyendayenda ku mapiri ndi ku magomo ataliatali. Zidabalalikira m'dziko lonse popanda wina wozilondola kapena kuzifunafuna.’
7
“Tsono abusa inu, tamverani zimene Ine Chauta ndikukuuzani:
8
Pali ine ndemwe, nkhosa zanga zidajiwa ndi zilombo zakuthengo, zidasanduka chakudya cha zilombo chifukwa chosoŵa abusa. Abusa anga sadalondole nkhosa zanga, ankangosamala za iwo okha, osasamala nkhosa.
9
Nchifukwa chake abusa inu, imvani mau a Ine Chauta.
10
Ndikuti, Ndaipidwa nanu abusanu. Ndidzakulandani nkhosa zanga, simudzazidyetsanso. Ndidzakuchotsani pa ntchito yaubusa, kuti musadzasamalenso za inu nokha. Ndidzapulumutsa nkhosa zanga kukamwa kwanu, ndipo simudzazidyanso.
11
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi, Tsopano nkhosa zangazo ndidzazifunafuna ndekha mwiniwakene, ndipo ndidzazisamala.
12
Monga mbusa amanka nafunafuna nkhosa zake, pamene zina zabalalikira kutali, Inenso ndidzatero, kunka ndikufunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa konse kumene zidamwazikira pa nthaŵi yamdima ndi yankhungu.
13
Ndidzazitulutsa pakati pa mitundu yonse ya anthu, ndidzazisonkhanitsa kuchokera ku maiko ena, ndipo ndidzazibwezera ku dziko lakwao. Ndidzaziŵetera ku mapiri a ku Israele, pafupi ndi mitsinje yake, ndi ku malo onse abwino kumene anthu amakhalako.
14
Ndidzaziŵetera ku mabusa abwino, ndipo zizidzadya msipu wonenepetsa ku mapiri okwera a Israele. Kumeneko zidzapumula ku mabusa abwino amsipu. Zidzapezadi mabusa abwino ku mapiri a Israele.
15
Ineyo mwiniwake ndidzakhala mbusa wa nkhosa zanga. Ndipo Ine ndemwe ndizidzazipumulitsa. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
16
Zotayika ndidzazifunafuna, zosokera ndidzazibweza, zopweteka ndidzazimanga mabala ake. Zofooka ndidzazilimbikitsa, koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaŵeta nkhosa zanga mwachilungamo.”
17
“Tsono kunena za inu, nkhosa zanganu, Ine Ambuye Chauta ndikukuuzani kuti, Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ndi nkhosa, pakati pa nkhosa zamphongo ndi atonde.
18
Kodi inu simukhutira kudya pa busa labwino? Nanga mumaponderezeranji zimene simudya? Kodi simukhutira kumwa madzi abwino? Nanga madzi amene simumwa mumaŵadetsereranji ndi mapazi anu?
19
Kodi mukufuna kuti nkhosa zanga zizidya udzu umene mudaponderezawo, ndi kumamwa madzi amene mudadetserera?
20
“Tsono Ine Ambuye Chauta ndikukuuzani kuti, Ineyo mwiniwake ndidzaweruza ndekha pakati pa inu nkhosa zonenepanu ndi zinzanu zoondazo.
21
Zofooka mumaziwomba ndi kuzikankhira kumbali, ndipo mumazigunda ndi nyanga zanu nkuzimwazira kutali.
22
Koma ndidzazipulumutsa nkhosa zangazo, ndipo sindidzalolanso kuti zijiwe. Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ina ndi nkhosa inanso.
23
Ndidzaziikira mbusa mmodzi, mtumiki wanga Davide. Iyeyo ndiye azidzazisamala, ndipo adzakhala mbusa wake.
24
Pamenepo Ine Chauta ndidzakhala Mulungu wake, ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yake. Ndatero Ineyo Chauta.”
25
“Ndidzapangana nazo chipangano chamtendere. Zilombo zonse zolusa ndidzazichotsa m'dziko, kuti nkhosa zanga zizidzakhala mwamtendere, ngakhale m'chipululu kapena m'thengo.
26
Ndidzakhazika anthu anga kufupi ndi phiri langa, ndipo ndidzaŵagwetsera mvula pa nthaŵi yake, mvula yake ya madalitso.
27
Mitengo ya m'minda idzabereka zipatso, ndipo minda idzakhala ndi zokolola zake, tsono anthu adzakhala mwamtendere m'dziko lao. Adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, pamene ndidzathyole magoli ao ndi kuŵapulumutsa kwa amene adaŵagwira ukapolo.
28
Anthu a mitundu ina sadzaŵafunkhanso, ndipo zilombo zakuthengo sizidzaŵadya. Adzakhala mwamtendere popanda wina woŵaopsa.
29
Ndidzachulukitsa zolima zao, mwakuti sadzafanso ndi njala m'dzikomo, ndipo choncho anthu a mitundu ina sadzaŵanyozanso.
30
Motero adzadziŵa kuti Ine Chauta Mulungu wao ndili nawo, ndipo kuti iwowo, Aisraelewo, ndi anthu anga. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
31
‘Inu ndinu nkhosa zanga, nkhosa zimene ndimadyetsa, ndipo Ine ndine Mulungu wanu. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.’ ”
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 35 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48