bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 3
Ezekiel 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 4 →
1
Pamenepo Mulungu adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, idya chimene ndikukupatsachi. Idya mpukutuwu ndipo pita ukalankhule ndi Aisraele.”
2
Motero ine ndidayasama, ndipo adandipatsa mpukutu kuti ndidye.
3
Tsono adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, idya mpukutu ndikukupatsawu, ukhute.” Choncho ndidadya, ndipo unkatsekemera ngati uchi.
4
Kenaka adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, pita kwa Aisraele, ukaŵauze mau anga.
5
Sindikukutuma kwa anthu olankhula chilankhulo chachilendo ndi chovuta ai, ndikukutuma kwa Aisraele.
6
Sindikukutuma kwa mitundu yambiri ya anthu amene chilankhulo chao nchachilendo ndi chovuta, amenenso sungathe kumvetsa zimene akulankhula. Ndithudi, ndikadakutuma kwa anthu achilendo otero, bwenzi iwo atakumvera.
7
Koma Aisraele sadzakumvera, chifukwa safuna kundimvera Ine. Onsewo ngaliwuma ndi a mtima wosamvera.
8
Tsono Ine ndidzakusandutsa waliwuma ndi wolimba mtima monga iwo omwewo.
9
Ndidzakulimbitsa kupambana thanthwe lina lililonse, kuti ukhale wolimba ngati mwala wa daimondi. Usachite nawo mantha anthu aupanduwo.”
10
Mulungu adapitiriza nati, “Iwe mwana wa munthu, umvetsetsetu zonse zimene ndikukuuza, ndipo uzikumbukire.
11
Tsopano upite kwa Aisraele anzako amene ali ku ukapolo, ukalankhule nawo. Kaya akamvera kaya akakana, uzikaŵauza kuti, ‘Zimene akunena Ambuye Chauta nzakutizakuti,’ ”
12
Pamenepo Mzimu wa Mulungu udandinyamula, ndipo kumbuyo kwanga ndidamva liwu lamphamvu ngati chivomezi chachikulu, lonena kuti, “Utamandike ulemerero wa Chauta kumene Iye amakhala!”
13
Phokoso ndidaalimvalo linali la mapiko a zilengolengo zija akukhudzana mu mlengalenga, ndiponso phokoso la mikombero ya pambali pake ija, lomveka ngati chivomezi chachikulu.
14
Mzimu wa Mulungu udandikweza ndi kundinyamula, ndipo ndidachokapo ndili ndi mtima woŵaŵa ndi wonyuka. Mphamvu za Chauta zidandiloŵa dzolimba.
15
Motero ndidafika kwa amene anali ku ukapolo ku Telabibu, pafupi ndi mtsinje wa Kebara. Ndidakhala pansi pakati pao masiku asanu ndi aŵiri, ndili wothedwa nzeru kwabasi.
16
Masiku asanu ndi aŵiriwo atatha, Chauta adandipatsira uthenga. Adati,
17
“Iwe mwana wa munthu, ndakuika kuti ukhale mlonda woyang'anira Aisraele. Uzikati ukamva mau anga, uzikaŵachenjeza.
18
Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Munthu woipa iwe, udzafa,’ iwe nupanda kumchenjeza kuti aleke makhalidwe oipawo, kuti akhalebe ndi moyo, munthuyo adzafadi ali wochimwa, koma iweyo ndidzakuzenga mlandu chifukwa cha imfa yake.
19
Koma munthu woipa ukamchenjeza kuti asiye njira zake zoipa, iye nkumapitirizabe makhalidwe ake oipawo, adzafa ali ochimwa, Koma iweyo udzapulumutsa moyo wako.
20
“Ngati munthu wokhulupirira ayamba kuchita uchimo, Ine nkumuika m'zoopsa, ameneyo adzafa. Ngati iweyo sudamchenjeze, inde adzafa chifukwa cha kuchimwa kwakeko, ndipo kukhulupirika kwake sindidzakukumbukira, koma tsono mlandu wa imfa yake udzakhala pa iwe.
21
Koma ukamchenjeza kuti asachimwe, iye nkulekadi kuchimwa, mosapeneka konse adzapulumutsa moyo wake, chifukwa chotsata chenjezo lako. Ndipo iwenso udzapulumutsa moyo wako.”
22
Nthaŵi ina ndidamva kuti mphamvu za Chauta zandiloŵa kwambiri, ndipo Iye adandiwuza kuti “Nyamuka, upite ku chigwa. Ndidzalankhula nawe kumeneko.”
23
Choncho ndidanyamuka kupita ku chigwa. Kumeneko ndidaona ulemerero wa Chauta, monga momwe ndidaauwonera ku mtsinje wa Kebara. Pomwepo ndidadzigwetsa pansi chafufumimba.
24
Koma Mzimu wa Mulungu udaloŵa mwa ine, ndipo udandiimiritsa. Apo Chauta adandilankhula nandiwuza kuti, “Pita kwanu, ukadzitsekere m'nyumba mwako.
25
Ndipo kumeneko, iwe mwana wa munthu, adzakumanga ndi zingwe, kotero kuti sudzatha kuyendanso pakati pa anthu.
26
Ndidzakangamiza lilime lako kukhosi, kotero kuti sudzathanso kulankhula ndi kuŵachenjeza, chifukwa ndi anthu aupandu.
27
Koma pamene ndidzayambe kulankhula nawe, ndidzakupatsa mphamvu zolankhulira. Ndipo udzaŵauze kuti, ‘Zimene akunena Ambuye Chauta nzakutizakuti.’ Wofuna kumva, amve. Wosafuna kumva, akhale, popeza kuti anthuwo ngaupandu.”
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48