bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 42
Ezekiel 42
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 41
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 43 →
1
Pambuyo pake munthu uja adapita nane ku bwalo lakunja chakumpoto, nandiloŵetsa m'nyumba ina yoyang'anana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi nyumba ina yakumpoto.
2
Nyumba yakumpotoyi m'litali mwake inali ya mamita makumi asanu, muufupi mwake inali ya mamita 25.
3
Kuyang'anana ndi bwalo lam'kati la mamita khumi, ndiponso kuyang'anana ndi chiwundo cha bwalo lakunja, panali makonde atatu osanjikana.
4
Kumaso kwa zipindazo kunali njira yam'kati, muufupi mwake mamita asanu, m'litali mwake mamita makumi asanu. Makomo ake adaaloza kumpoto.
5
Zipinda zam'mwamba zinali zazifupi m'mimbamu kupambana zam'munsi ndi zapakati, chifukwa njira zake zam'kati zidaalanda malo ambiri.
6
Zonse zinali zosanjikana patatu, ndipo zinalibe nsanamira monga za mabwalo. Motero zipinda zam'mwamba zinali zochepera kuyerekeza ndi zapakati ndi zapansi.
7
Khoma lakunja, kutalika kwake mamita 25, linkatsatana ndi zipinda kutsogolo kwake pambali pa bwalo lakunja.
8
Zipinda za m'mbali mwa bwalo lakunja m'litali mwake zinali za mamita 25. Koma zokhala m'mbali mwa Nyumba ya Mulungu ija m'litali mwake zinali za mamita makumi asanu.
9
Pansi pa zipinda zimenezi panali khoma lake chakuvuma, kuchokera ku bwalo lakunja kumene khoma la bwalo linkayambira.
10
Mbali yakumwera, kuyang'anana ndi bwalo ndi nyumbayo, kunali zipinda zina, ndipo kumaso kwake kunali njira.
11
Zipinda zimenezi m'litali mwake ndi muufupi mwake ndiponso maonekedwe ake onse zinali zolingana ndi zoyang'ana kumpoto zija. Makomo ake ndi zitseko zake zinalinso zolingana.
12
Ndipo kunsi kwa zipinda zakumwera, kunali khomo lake mbali ya kuvuma kumene ankaloŵerako. Kunalinso khoma logaŵa zipinda.
13
Tsono munthu uja adandiwuza kuti, “Zipinda zakumpoto ndi zakumwera zoyang'anana ndi khonde nzoyera. M'menemo ansembe okhala kufupi ndi Chauta amadyeramo zopereka zopatulika kwambiri. M'menemo adzaikamo zopereka zimenezi pamodzi ndi zopereka za chakudya, nsembe yopepesera machimo, ndi nsembe zopepesera kupalamula, poti malowo ndi oyera.
14
Ansembe ataloŵa m'malo oyerawo, sadzatulukamo kupita m'bwalo lakunja popanda kusiya m'menemo zovala zimene amavala potumikira zija. Zimenezi nzoyera. Ayenera kuvala zina asanafike pa anthu.”
15
Atamaliza kuyesa m'kati mwa Nyumba ya Mulungu, munthu uja adatuluka nane pa chipata chopenya kuvuma. Pamenepo adayesa bwalo lonse.
16
Adayesa mbali yakuvuma ndi bango loyesera lija, kutalika kwake kunali kwa mamita 250.
17
Kenaka adatembenuka nayesa mbali yakumpoto ndi bango lakelo, kutalika kwake kunali kwa mamita 250.
18
Adatembenuka nayesa mbali yakumwera ndi bango lake. Kutalika kwake kunali kwa mamita 250.
19
Adatembenukanso nayesa kuzambwe ndi bango lake. Kutalika kwake kunali kwa mamita 250.
20
Motero adayesa mbali zonse zinai. Panali khoma lozungulira bwalo lonselo, m'litali mwake linali la mamita 250, muufupi mwakenso mamita 250. Khomalo linali lolekanitsa zinthu zoyera ndi zinthu wamba.
← Chapter 41
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 43 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48