bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 5
Ezekiel 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 6 →
1
“Iwe mwana wa munthu, tenga lupanga lakuthwa ngati lumo la wometa, umete tsitsi ndi ndevu. Tsono utenge choyesera, ugaŵe tsitsilo patatu.
2
Kuzinga mzinda kuja kukatha, chimodzi cha zigawo zitatu za tsitsilo uchitenthe pakati pa mzinda. Chigawo chachiŵiri uchiduledule ndi lupanga, poyenda mozungulira mzinda wonsewo. Chigawo chachitatu uchimwazire ku mphepo, ndidzachitsata nditasolola lupanga.
3
Utengeko tsitsi pang'ono, ulimange mu mpendero wa mkanjo wako.
4
Pa tsitsi limeneli utapepo lina, uliponye pa moto, nkulitentha. Moto wa tsitsilo udzayaka mpaka kutentha Israele yense.”
5
“Zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi, akuti, ‘Uyu ndi Yerusalemu. Ndamuika pakati pa dziko lapansi, ndipo maiko onse akumzungulira.
6
Koma anthu a ku Yerusalemu adapandukira malamulo anga, kupambana anthu a mitundu ina. Adakhala osamvera kupambana anthu a m'maiko ozungulira. Adakanadi malamulo anga ndipo sadasunge malangizo anga.’
7
Nchifukwa chake zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Chipongwe chanu nchachikulu kupambana cha anthu a mitundu yokuzungulirani. Simudatsate malamulo anga, simudasunge malangizo anga, koma mudatsata malamulo a anthu a mitundu yokuzungulirani.
8
Nchifukwa chake Inenso ndakukanani. Ndidzakulangani anthu a mitundu ina akuwona.
9
Ndidzakulangani ndi chilango chimene sindidakulange nachoni nkale lonse, ndipo sindidzakulanga nachoninso nkutsogolo komwe, poti zolakwa zanu nzonyansa kwambiri.
10
Tsono mwa inu makolo adzadya ana ao ndipo ana adzadya makolo ao. Ndidzakulanganidi, ndipo onse otsala pakati pa inu, ndidzaŵamwazira ku mphepo zonse zinai.”
11
“Pali Ine ndemwe Mulungu wamoyo, ndidzakuwonongani mopanda chifundo, chifukwa choti mwaipitsa Nyumba yanga ndi mafano anu oipa ndi miyambo yanu yonyansa. Tsono Ine sindidzakulekererani, sindidzakuchitirani chisoni mpang'ono pomwe.
12
Chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu anu chidzafa ndi mliri, kapena chidzaonongeka ndi njala. Chigawo china chidzaphedwa ndi lupanga kunja kwa mzinda. Ndipo chigawo china ndidzachimwazira ku mphepo zonse zinai, pochita kuchipirikitsa ndi lupanga langa losolola.”
13
“Ndimo m'mene udzachitire mkwiyo wanga, ndipo ndidzaŵakalipira mpaka mtima wanga utakhala pansi. Choncho adzadziŵa kuti Ine Chauta ndidalankhula mwansanje pokulangani monga m'mene ndachitiramu.”
14
“Iwe Yerusalemu, ndidzakusandutsa bwinja. Udzakhala chinthu chonyozeka m'maso mwa anthu a mitundu yokuzungulira ndi kwa onse odutsapo.
15
Udzakhala chinthu chonyozeka, ndipo adzakunyodola. Udzakhala ngati chenjezo ndi chinthu choopsa kwa mitundu ya anthu okuzungulira, pamene ndidzakulanga mwamphamvu ndi kugamula mlandu wako mokwiya ndi mwaukali. Ndatero Ine Chauta.
16
Ndidzakulasa ndi njala yolasa ngati mivi yoopsa ndi yosakaza, kuti ndikuwononge. Ndidzagwetsa njalayo pa iwe pochepetsa chakudya chako cha tsiku ndi tsiku.
17
Ndidzatumiza njala ndi zilombo zakuthengo ndipo zidzakulanda ana ako. Ndidzakugwetsa ndi mliri ndipo padzakhala kuphana pakati pa anthu ako. Ndidzakudzetsera nkhondo yokuwononga. Ndatero Ine Chauta.”
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48