bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 21
Ezekiel 21
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 22 →
1
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyang'ane cha ku Yerusalemu, ndipo ulalike zodzudzula malo ake opatulika. Ulose zodzudzula dziko la Israele.
3
Uliwuze dziko la Israelelo kuti Chauta akuti, ‘Ndimati ndilimbane nawe. Choncho ndidzasolola lupanga langa m'chimake kuti ndiphe anthu ako, abwino ndi oipa omwe.
4
Ndithu ndidzasolola lupanga langa m'chimake kuti ndidzaphe anthu ako oipa ndi abwino omwe, ndiye kuti anthu onse kuyambira kumwera mpaka kumpoto.
5
Motero anthu onse adzadziŵa kuti Ine Chauta ndasolola lupanga langa, ndipo sindidzalilonganso m'chimake.’
6
“Tsono iwe mwana wa munthu, buula pamaso pao, buula kwambiri ndi mtima woŵaŵa zedi.
7
Akakufunsa chifukwa chake chimene ukubuulira, uŵayankhe kuti, ‘Ndikubuula chifukwa cha nkhani zimene ndamvazi. Zikadzachitika zimenezo, mitima idzangoti fumu, ndipo manja ao onse adzalefuka, mpweya wao wonse udzaŵathera, onse m'maondo mwao mudzangoti zii. Zikubwera, zidzachitikadi!’ Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
8
Chauta adandipatsiranso uthenga uwu wakuti,
9
“Iwe mwana wa munthu, ulose, ndipo unene kuti Ambuye akuti, “ ‘Lupanga, lupanga, alinola, ndipo alipukuta.
10
Alinola kuti likaphe, alipukuta kuti ling'anipe ngati mphezi. Kodi tingakondwere bwanji, pamene anthu anga anyoza ndodo yanga yolangira?
11
Lupanga laperekedwa kuti alipukute ndipo kuti alinyamule. Lupanga limeneli lanoledwa ndi kupukutidwa, kuti alipereke m'manja mwa munthu amene amapha.
12
Ulire ndipo ufuule, iwe mwana wa munthu, chifukwa zonsezi zidzagwera anthu anga. Zidzagweranso akalonga a Aisraele. Adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi anthu anga. Nchifukwa chake udzigunde pa chifuŵa mwachisoni.
13
Zingalephere bwanji kuwoneka, popeza kuti akunyoza ngakhale ndodo yanga yolangira?’ Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
14
“Koma iwe mwana wa munthu, losa, ndipo uwombe m'manja. Lupangalo lidzagwe kaŵiri ngakhale katatu, ndiye kuti lupanga lophera. Ndilodi lupanga loononga anthu koopsa, limene likuŵazungulira.
15
Anthu anga adzataya mtima, ndipo ambiri adzagwa. Ndaŵaikira lupanga laphuliphuli. Ha, lupanga lidapangidwadi kuti lizing'anipa ngati mphezi, ndipo azilisolola nkuphera anthu.
16
Lupanga iwe, uzikapha ku dzanja lamanja, uzikapha ku dzanja lamanzere, kulikonse kumene nsonga yako yaloza.
17
Inenso ndidzaomba m'manja, ndi kuziziritsa mkwiyo wanga. Ine Chauta ndatero.”
18
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
19
“Iwe mwana wa munthu, ulembe zizindikiro pa miseu iŵiri imene mfumu ya ku Babiloni ingathe kudzeramo, pobwera ndi lupanga. Iŵiri yonseyo idzakhala yochokera ku dziko limodzi. Uike chikwangwani pa mphambano ya miseu yopita ku mzinda.
20
Ulembe zizindikiro pa mseu umene lupanga lidzadzere popita ku Raba wa ku Amoni, ndiponso ku Yuda ndi ku Yerusalemu, mzinda wamalinga.
21
Mfumu ya ku Babiloni yaima ku njira pa mphambano ya miseu. Ikuwombeza maula ndi mivi kuti ipeze njira yoyenera kudzeramo. Ikupempha nzeru kwa milungu yake, ndipo ikuyang'ana chiŵindi cha nyama yopereka ku nsembe.
22
Tsono m'dzanja lake lamanja muli muvi wa ula wolembedwa Yerusalemu. Kumeneko mfumu iyenera kukalalika za kupha anthu ndiponso kufuula mfuu wankhondo. Iyenera kupanga makina othyolera zipata, kuunda mitumbira yankhondo ndi kumanga nsanja.
23
Koma kwa anthu a ku Yerusalemu zidzaoneka ngati zolosa zabodza, chifukwa cha malumbiro amene adaachita kwa mfumuyo. Koma adzaŵakumbutsa za machimo ao, kuti adzatengedwe ukapolo.
24
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta, ndikuti, Mwandikumbutsa zolakwa zanu, ndipo kundiwukira kwanu kwaonekera poyera. Mukuwonetsa machimo anu pa zochita zanu zonse. Nchifukwa chake mudzagwidwa ndi kutengedwa ukapolo.
25
“Tsono iwenso, wolamulira Israele, iwe wonyozeka ndi woipa, lafika tsiku lako, ndiye kuti nthaŵi ya chilango chako chomaliza.”
26
Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Vula nduŵirayo, chotsa chisoti chaufumucho. Zonse zasinthika! Otsika uŵakweze, okwera uŵatsitse.
27
Chipasupasu! Chipasupasu! Mzinda ndidzaupasula, ndipo sadzaumanganso mpaka atafika amene ali woyenera kuulandira. Pamenepo ndidzaupatsa kwa iyeyo.
28
“Tsono iwe mwana wa munthu, ulalike kuti, ponena za Aamoni ndi manyozo ao, Ine Chauta ndikuti, “ ‘Lupanga, lupanga alisolola kuti liwononge. Alipukuta kuti liwononge, kuti ling'anipe ngati mphezi.
29
Zimene akuti akuziwona m'masomphenya nzabodza ndiponso maula ao ndi onama. Mudzakhala pamodzi ndi anthu oipa, amene tsiku lao lafika, ndiye kuti nthaŵi ya kulangidwa kwao komaliza.
30
Mulibwezerenso lupanga m'chimake. Ndidzakuweruzani kumalo kumene mudabadwira, ku dziko la makolo anu.
31
Ndidzakukwiyirani ndipo ukali wanga udzakuyakirani. Ndidzakuperekani m'manja mwa anthu ankhanza, amene amadziŵa kuwononga.
32
Mudzakhala ngati nkhuni pa moto. Ena adzakhetsa magazi anu m'dziko mwanu momwe. Palibe amene adzakukumbukiraninso. Ndatero Ine Chauta.’ ”
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48