bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 4
Ezekiel 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 5 →
1
Mulungu adati, “Iwe mwana wa munthu, tenga phale, uliike pamaso pako, ndipo ulembepo chithunzi cha mzinda wa Yerusalemu.
2
Mzindawo uuzinge ndi ngalande, uunde mitumbira yankhondo, uuzinge ndi zithando zankhondo ndipo uzike makina ogumulira, kuzungulira mzindawo.
3
Utenge chitsulo, uchiimike ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mzindawo. Uyang'anitsitse mzindawo, ndipo uumangire zithando zankhondo ndi kuuzinga kotheratu. Chimenechi chidzakhala chizindikiro kwa Aisraele.”
4
“Tsono ugonere kumanzere kwako, ndipo machimo a anthu a ku Israele ndidzaŵaika pa iwe. Udzasenza machimo aowo masiku onse amene udzagonere mbali imeneyo.
5
Ndachitatu kukuikira masiku, okwanira 390, kulinganiza ndi zaka za machimo ao. Umu ndimo m'mene udzasenzere machimo a Aisraele.
6
Utatha zimenezi, udzatembenuke nkugonera ku dzanja lamanja. Tsono udzasenze machimo a anthu a ku Yuda pa masiku makumi anai, tsiku lililonse kulinganiza ndi chaka chathunthu cha chilango chao.
7
Uyang'anitsitse zithando zankhondo zozinga Yerusalemu. Ukwinye dzanja la mkanjo wako, ukweze mkono wako ndipo ulose modzudzula Yerusalemu.
8
Ndithudi, ndidzakumanga ndi zingwe, kotero kuti sudzatha kutembenukira uku ndi uku, mpaka kuzingidwa kwa Yerusalemu kutatha.
9
“Tsopano tenga tirigu ndi barele, nyemba ndi mphodza, mapira ndi mcheŵere, zonsezo uziike m'mbale imodzi, kenaka upange buledi. Uzidzadya pa masiku 390 amene udzakhale ukugonera mbali imodzi.
10
Udzayeseko theka la kilogramu la bulediyo, kuti akhale chakudya chako. Uzidzadya kamodzi kokha pa tsiku.
11
Uyesekonso makapu aŵiri a madzi, kuti akhale chakumwa chako cha tsiku ndi tsiku.
12
Udzadya buledi wako wophika ngati makeke abarele. Ndoŵe youma ya anthu ndiyo idzakhale nkhuni zako zophikira, ndipo uzidzaphikira kumene anthu angathe kukuwona.”
13
Tsono Chauta adati, “Buledi ameneyu ndiye chifaniziro cha chakudya chodetsedwa chimene Aisraele azidzadya ku maiko achilendo kumene ndidzaŵapirikitsire.”
14
Koma ine ndidati “Inu Ambuye Chauta, inetu sindidadziipitsepo motero pa chipembedzo. Kuyambira ubwana wanga mpaka lero lino, sindidadyepo nyama yofa yokha kapena yojiwa ndi zilombo, ndipo sindidadyepo nyama yonyansa pa zachipembedzo.”
15
Apo Iye adati, “Chabwino, ndidzakulola kuphikira ndoŵe ya ng'ombe m'malo mwa ndoŵe ya anthu, pophika buledi.”
16
Kenaka adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Yerusalemu ndidzaŵachepetsera buledi wa tsiku ndi tsiku. Anthuwo buledi wao azidzachita woyesa, ndipo azidzadya mwankhaŵa. Madzi aonso azidzachita oyesa, nkumamwa mwamantha.
17
Motero chakudya ndi madzi zidzaŵathera pang'onopang'ono. Azidzada nkhaŵa akamapenyana, ndipo adzatheratu nkuwonda chifukwa cha machimo ao.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48