bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 29
Ezekiel 29
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 30 →
1
Pa tsiku lakhumi ndi chiŵiri la mwezi wakhumi, chaka chakhumi cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, umuimbe mlandu Farao, mfumu ya ku Ejipito, ndipo ulose modzudzula iyeyo pamodzi ndi dziko lake lonse.
3
Umuuze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, “ ‘Ndikukuimba mlandu iwe Farao mfumu ya ku Ejipito, iwe ching'ona chogona m'mitsinje mwako. Wanena kuti, mtsinje wa Nailo ndi wako, udaulenga ndiwe.
4
Koma ndidzakukola ndi mbedza m'kamwa mwako, nsomba za m'mitsinje mwako zidzakangamira ku mamba ako. Tsono ndidzakutulutsa mumtsinjemo pamodzi ndi nsomba zimene zakukangamira.
5
Ndidzakutaya ku chipululu, iweyo pamodzi ndi nsomba za m'mitsinje yako. Udzagwera ku thengo popanda wina wokutola kuti aike maliro ako. Ndidzakusandutsa chakudya cha zilombo ndi mbalame.’
6
“Motero onse okhala ku Ejipito adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. Iwe Ejipito unali ngati ndodo yabango kwa Aisraele.
7
Ndodoyo idaphwanyikira m'manja ataigwira, ndipo idaŵacheka pa mapewa. Ataitsamira, iyo idathyoka, ndipo m'chiwuno mwao monse mudagwedezeka.
8
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndikubweretsera nkhondo kuti idzaononge anthu pamodzi ndi nyama zomwe.
9
Dziko la Ejipito lidzasanduka chipululu, lopanda anthu. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. “Zoona, iwe udati, ‘Nailo ndi wanga, ndidamlenga ndine.’
10
Tsono Ine ndikudana ndi iweyo, pamodzi ndi mitsinje yakoyo. Ndipo Ejipito ndidzamsandutsa bwinja, kuyambira ku mzinda wa Migidoli mpaka ku mzinda wa Siyene, kukafika ku malire a Etiopiya.
11
Palibe phazi la munthu kapena la nyama limene lidzapondapo. Kudzakhala kopanda anthu pa zaka makumi anai.
12
Dziko la Ejipito ndidzalisandutsa bwinja kupambana mabwinja a maiko ena onse. Pa zaka makumi anai mizinda yakenso idzakhala yopasuka kupambana mizinda ina yopasuka. Aejipitowo ndidzaŵamwaza pakati pa mitundu ya anthu, ndi kuŵabalalitsa pakati pa maiko ena.
13
“Komabe Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pomatha zaka makumi anaizo, ndidzasonkhanitsa Aejipito kuchokera ku mitundu ya anthu kumene adamwazikira.
14
Ndidzaŵachotsa ku ukapolo, ndipo ndidzaŵabwezera ku Patirosi kumene adachokera. Kumeneko adzakhala ndi ufumu wotsika.
15
Ufumuwo udzasanduka wofooka kupambana maufumu ena onse, ndipo sudzadzikuzanso pakati pa mitundu ya anthu. Ndithudi Aejipito ndidzaŵachepetsa kwambiri, kotero kuti sadzatha kulamuliranso mitundu ina.
16
Aisraele sadzadaliranso Ejipito. Ndipo chilango chimenechi chidzaŵakumbutsa kuchimwa kwao kuja pamene ankapempha Aejipito kuti aŵathandize. Motero Aisraele adzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta.”
17
Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, chaka cha 27 cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
18
“Iwe mwana wa munthu, kale Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, idaagwiritsa ntchito ankhondo ake pokathira nkhondo mzinda wa Tiro, mpaka munthu aliyense adachita dazi chifukwa chosenza katundu, ndipo adanyuka pa phewa. Komabe ngakhale iyeyo, kapena gulu lake lankhondo, sadaphulepo kanthu pa ntchito yonse imene adaigwirayo polimbana ndi mzindawo.
19
Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloniyo, ndidzampatsa Ejipito. Adzatenga chuma chake nadzachifunkha nkupita nacho. Zimenezi zidzakhala malipiro a gulu lake lankhondo.
20
Ndampatsa dziko la Ejipito kuti akhale malipiro ake, chifukwa iye ndi ankhondo ake adandigwirira ntchito. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
21
“Pa nthaŵi imeneyo, Aisraele ndidzaŵapatsa mphamvu zatsopano, ndipo iwe Ezekiele ndidzakulimbitsa kuti udzathe kulankhula pakati pao. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 30 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48