bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 8
Ezekiel 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 9 →
1
Tsiku lachisanu la mwezi wachisanu ndi chimodzi, chaka chachisanu ndi chimodzi cha ukapolo, ndidaali khale m'nyumba mwanga pamodzi ndi akuluakulu a ku Yuda. Mwadzidzidzi mphamvu za Ambuye Chauta zidandifikira.
2
Ine ndiyang'ane, ndidaona chinthu chooneka ngati munthu. Munthuyo kuchokera m'chiwunomu kumapita m'munsi anali ngati moto. Kuchokera m'chiwuno kukwera m'mwamba anali ngwee ngati mkuŵa wonyezimira.
3
Adatambalitsa chinthu chonga dzanja nandigwira tsumba. Pomwepo mzimu wa Mulungu udandikweza mu mlengalenga. Ndipo ngati ndikuwona Mulungu kutulo, udapita nane ku Yerusalemu, nundiika pa khoma loloŵera ku chipata cham'kati choyang'ana kumpoto. Kumeneko kunali fano loputa mkwiyo wa Mulungu.
4
Ulemerero wa Mulungu wa Israele udaoneka kumeneko, monga momwe ndidaaonera kale m'masomphenya m'chigwa muja.
5
Pamenepo Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tayang'ana kumpoto.” Ine nkuyang'anadi kumpoto. Kumeneko, pafupi ndi guwa pa khomo la chipata, ndidaona fano loputa mkwiyo wa Mulungu lija.
6
Chauta adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuwona zimene Aisraele akuchitazi, zonyansa zazikulu zimene akuchita kuno, zondichotsa ku Nyumba yanga yoyera? Ndipotu udzaona zonyansa zina zazikulu kuposa zimenezi.”
7
Pambuyo pake adapita nane ku khomo loloŵera ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Ine poyang'ana, ndidaona dzenje pakhomapo.
8
Tsono adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, boola pakhomapo.” Ndidabooladi, ndipo ndidapeza ngati khomo.
9
Adandiwuza kuti, “Loŵa, uwone zonyansa zazikulu zimene anthu akuchita kuno.”
10
Motero ndidaloŵa, ndipo pamakomapo ndidaonapo zithunzi za zinthu zosiyanasiyana zokwaŵa pansi, za nyama zonyansa ndiponso za mafano ena onse amene Aisraele ankapembedza.
11
Atsogoleri a Aisraele makumi asanu ndi aŵiri anali ataima pamenepo. Yazaniya, mwana wa Safani, anali pakati pao. Aliyense mwa iwo anali ndi chofukizira lubani m'manja, ndipo utsi wa fungo lokoma la lubani unkatuluka m'menemo.
12
Tsono Chauta adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuwona zimene akulu a Israele akuchita mumdima muno? Aliyense akupembedza fano lakelake m'nyumbamu. Akunena kuti, ‘Chauta sakutiwona! Chauta walisiya dziko!’ ”
13
Chauta adandiwuzanso kuti, “Udzaŵaonanso akuchita zonyansa zina zazikulu kupambana zimenezi.”
14
Pambuyo pake adapita nane ku chipata cha ku Nyumba ya Chauta choyang'ana kumpoto. Kumeneko ndidaona akazi ena atakhala pansi, akulira mulungu wao wotchedwa Tamuzi.
15
Chauta adati, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziwona zimenezi? Komabe udzaona zonyansa zina zazikulu kupambana zimenezi.”
16
Kenaka adapita nane ku bwalo lam'kati la Nyumba ya Chauta. Kumeneko, ku khomo loloŵera ku Nyumba ya Chauta, pakati pa khonde ndi guwa, kunali anthu aamuna ngati 25. Adaafulatira Nyumba ya Chautayo, nkhope zao zitaloza chakuvuma, ndipo ankapembedza dzuŵa choyang'ana kuvuma.
17
Chauta adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziwona zimenezi? Ayuda sakukhutira nazo zonyansa akuchita panozi. Koma akufalitsanso zandeu m'dziko lonse. Motero akuutsa ukali wanga, akundipsetsa mtima ndi zochita zao.
18
Tsono Ine ndidzaŵalanga ndili wokwiya. Sindidzaŵayang'ana ndi maso achifundo, ndipo sindidzaŵalekerera. Ngakhale adzalire mofuula kwa Ine, sindidzaŵamvera ai.”
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48