bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 31
Ezekiel 31
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 32 →
1
Pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu, chaka cha khumi ndi chimodzi cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, unene mau aŵa kwa Farao mfumu ya ku Ejipito pamodzi ndi gulu lake la nkhondo: “ ‘Kodi pa ukulu wanu nkukuyerekezani ndi yani?
3
Ndithu ndidzakufanizirani ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni, wa nthambi zabwino zochititsa mthunzi m'nkhalango, nthambi zosomphoka, zofika mpaka ku mitambo.
4
Madzi ndiwo amene ankaukulitsa, ndipo akasupe ankautalikitsa. Mitsinje inkayenda mozungulira kumene unaliri, mifuleni yake inkafika ku mtengo uliwonse m'dzikomo.
5
Koma mtengo uwu udatalika kwambiri kupambana mtengo wina uliwonse. Nthambi zake zidachuluka ndi kutalika kwambiri, popeza kuti mizu yake inkalandira madzi ambiri.
6
Mbalame zamumlengalenga zinkamanga zisa zake m'nthambi za mtengowo. Nyama zonse zakuthengo zinkaswanirana m'munsi mwa nthambizo. Mitundu yonse yotchuka ya anthu inkakhala mumthunzi mwake.
7
Unali mtengo wokongola kwambiri wa nthambi zitalizitali, chifukwa choti mizu yake inkazama ndi kulandira madzi ambiri.
8
M'munda wa Mulungu munalibe mkungudza wofanafana ndi umenewo. Munalibe mtengo wa paini wa nthambi zofanafana ndi zake. Munalibenso mkuyu umene unali ndi nthambi zotere. M'munda wa Mulungu munalibe mtengo wina wofanafana ndi umenewu kukongola kwake.
9
Ndi Ineyo Mulungu amene ndidaukongoletsa, pochulukitsa nthambi zake, kotero kuti mitengo yonse ya mu Edeni, munda wa Mulungu inkachita nawo nsanje.’
10
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Chifukwa choti mtengowo udatalika kwambiri nkufika mpaka ku mitambo, ndipo unkanyada pokula choncho,
11
Ine ndidaupereka m'manja mwa mfumu yolamulira anthu a mitundu ina, kuti mfumuyo iwulange potsata zolakwa zake.
12
Alendo ankhalwe kwambiri pakati pa mitundu ya anthu adzaudula, ndipo adzangoutaya. Nthambi zake zidzagwera pa mapiri, ndiponso m'zigwa zonse. Nthambi zakezo zidzathyokera m'mitsinje yam'dzikomo. Motero anthu a mitundu yonse ya dziko lapansi amene ankasangalala mumthunzi mwake adzausiya nachoka.
13
Mbalame zonse zamumlengalenga zidzakhala pa thunthu la mtengo wakugwawo. Nyama zonse zakuthengo zidzakhala pa nthambi zake.
14
Zonsezi zidzatero kuti pasakhale mtengo ndi umodzi womwe wa m'mbali mwa mtsinje umene udzatalike kwambiri, kapena umene nsonga zake zidzafike ku mitambo. Ndiponso pasadzakhale mitengo ina yolandira bwino madzi, imene msinkhu wake ungafike ku mitambo. Pakuti yonseyo kutha kwake ndi kufa, kupita kunsi kwa dziko lapansi, kukakhala pamodzi ndi anthu akufa, amene adaloŵa kale m'manda.
15
“Zimene Ine Ambuye Chauta ndikunena ndi izi: Mkungudzawo utatsikira ku manda, ndidauza nyanja kuti iwulire maliro pa kuuphimba. Ndidaumitsa mitsinje yake, ndipo madzi ambiri adaphwa. Ndidachititsa mdima pa Lebanoni chifukwa cha mtengowo, ndipo mitengo yonse yam'dzikomo idauma.
16
Mitundu ya anthu idagwedezeka pakumva mkokomo wa kugwa kwake, pamene ndidautsitsira ku manda pamodzi ndi amene adafa. Pamenepo ku dziko la akufa mitengo yonse ya ku Edeni, ndi yonse yokongola ya ku Lebanoni yothiriridwa bwino, idasangalatsidwa chifukwa cha zimenezi.
17
Mitundu imene inkakhala mumthunzi mwake chifukwa cha kumvana nawo, nayonso idapezana nawo kumandako, pamodzi ndi amene adaphedwa ku nkhondo.
18
“Pakati pa mitengo ya ku Edeni, kodi unalipo ndi umodzi womwe wolingana nawe pa ulemerero ndi pa ukulu? Komabe iwenso udzatsikira ku dziko la akufa, pamodzi ndi mitengo ina yonse ya ku Edeni. Udzagona pamodzi ndi amene adaphedwa ku nkhondo, m'gulu la anthu osaumbalidwa! Mtengowo ndi mfumu ya ku Ejipito pamodzi ndi anthu ake. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 32 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48