bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 28
Ezekiel 28
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 29 →
1
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, uza mfumu ya ku Tiro mau angaŵa akuti, Iwe ndi mtima wako wodzikuza umanena kuti, ‘Ine ndine mulungu. Ndimakhala ngati mfumu pa mpando wa milungu pakati pa nyanja yozama.’ Koma chonsecho ndiwe munthu chabe, osati mulungu, ngakhale umadziyesa wanzeru ngati mulungu.
3
Ai, iwe ndiwe wanzerudi kupambana Daniele, palibe chinsinsi chobisika kwa iwe.
4
Nzeru zako ndi kumvetsa kwako zidakulemeretsa pokupatsa chuma cha golide ndi siliva.
5
Udachulukitsa chuma chako chifukwa cha nzeru zako zoyendetsera malonda, ndipo ukunyada chifukwa cha chuma chakocho.
6
Tsono Ine Ambuye Chauta ndikuti, Poti umadziganizira kuti ndiwe wanzeru ngati mulungu,
7
Ine ndidzabwera ndi anthu achilendo kuti adzalimbane nawe. Iwowo ndi mtundu wa anthu ankhanza kwambiri. Adzakuthira nkhondo kuti aononge zokoma zonse zimene udazipata ndi nzeru zako, ndiponso kuti athyole kunyada kwako.
8
Adzakuponya ku malo a anthu akufa, udzafa imfa yoopsa m'nyanja yozama.
9
Kodi pamenepo udzanenabe kuti ndiwe mulungu pamaso pa anthu amene akukuphawo? Iyai, udzaoneka ngati munthu ndithu osati mulungu, pamene udzakhala m'manja mwa okuphawo.
10
Udzafa imfa ya anthu osaumbalidwa m'manja mwa anthu achilendo. Ine ndalankhula zimenezi. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
11
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
12
“Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo ya maliro, kulira mfumu ya ku Tiro. Uiwuze mau angaŵa akuti, Udaali chitsanzo cha ungwiro weniweni. Udaali wanzeru ndiponso wokongola kwabasi.
13
Unkakhala ngati ku Edeni, ku munda wa Mulungu, ndipo unkadzikongoletsa ndi miyala yamtengowapatali ya mitundu yonse: karineliyoni, topazi, jasipere, kirisoliti, berili, onikisi, safiro, rubi ndi emeradi. Zoikamo miyalayo zinali zagolide. Adakupangira zonsezi pa tsiku limene udalengedwa.
14
Ndidakuikira mngelo woopsa kuti azikulonda. Unkakhala pa phiri langa lopatulika, ndipo unkayenda pakati pa miyala yamoto.
15
Makhalidwe ako anali angwiro kuyambira tsiku limene udalengedwa mpaka nthaŵi imene udayamba kuchita zoipa.
16
Potanganidwa ndi zamalonda, udaachulukitsa zandeu ndi kumangochimwa. Nchifukwa chake ndidakuchotsa ku phiri langa lopatulika. Mngelo amene ankakulonda adakupirikitsa kuchokera ku miyala yamotoyo.
17
Unkanyada chifukwa cha kukongola kwako, udaipitsa nzeru zako chifukwa chofuna kukhala wotchuka. Motero ndidakugwetsa pansi kuti ukhale chenjezo kwa mafumu ena.
18
Udachita zoipa zambiri pa kugula ndi kugulitsa zinthu, ndipo choncho malo ako achipembedzo udaŵaipitsa. Motero ndidabutsa moto pakati pako ndi kukupserezeratu. Onse okupenya tsopano amaona kuti ndiwe phulusa pa dziko lapansi.
19
Anthu a mitundu yonse amene ankakudziŵa akuwopsedwa ndi zimene zidakuchitikira. Imfa yako inalidi yoopsa, ndipo sudzakhalanso mpaka muyaya.”
20
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
21
“Iwe mwana wa munthu, utembenukire ku mzinda wa Sidoni ndipo ulose momdzudzula kuti,
22
“Ine Ambuye Chauta ndikuti, ‘Ndine mdani wako, iwe Sidoni, ndipo anthu akadzaona zimene ndidzakuchite iwe, adzandilemekeza. Adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzakulanga ndipo ndikadzaonetsa pakati pako kuti Ine ndine woyera.
23
Ndidzakugwetsera mliri, ndipo m'miseu yako mudzayenderera mitsinje ya magazi. Anthu adzatha phu nkuphedwa, nkhondo idzakuzinga mbali zonse. Tsono anthu adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.’ ”
24
“Nthaŵi imeneyo pafupi ndi Aisraele sipadzakhalanso anthu onyoza omaŵalasa ngati mitungwi, kapena omaŵapweteka ngati minga. Apo anthu adzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta.
25
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Nditasonkhanitsa Aisraele kuchokera ku mitundu ya anthu kumene adamwazikira, ndidzaonetsa kuyera kwanga mwa iwo, anthu a mitundu yonse akuwona. Aisraelewo adzakhalanso m'dziko lao limene ndidaapatsa mtumiki wanga Yakobe.
26
Adzakhala kumeneko mwamtendere, ndipo adzamanga nyumba ndi kulima minda yamphesa. Adzakhala kumeneko mwamtendere, pamene ndidzalange anthu oyandikana nawo, amene ankaŵanyoza. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, Mulungu wao.”
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 29 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48