bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 43
Ezekiel 43
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 42
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 44 →
1
Pambuyo pake munthu uja adapita nane ku chipata choyang'ana kuvuma.
2
Kumeneko ndidaona ulemerero wa Mulungu wa Israele ukuchokera kuvuma. Liwu lake linali ngati mkokomo wa madzi, ndipo dziko lapansi lidaŵala ndi ulemerero wakewo.
3
Zimene ndidaziwona m'masomphenya zinali ngati zomwe ndidaaziwona zija pamene Chauta adaabwera kudzaononga mzinda. Zinalinso ngati zimene ndidaaziwona ku mtsinje wa Kebara. Tsono ndidadzigwetsa pansi chafufumimba.
4
Ulemerero wa Chauta udakaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, kuloŵera chipata choyang'ana kuvuma.
5
Mzimu wa Mulungu udandinyamula numandiloŵetsa m'bwalo lam'kati. Ndipo ulemerero wa Chauta udadzaza Nyumba yakeyo.
6
Munthu uja ataima pambali panga, ndidamva wina akundilankhula kuchokera m'Nyumba ya Mulungu.
7
Adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, malo ano ndi malo a mpando wanga waufumu, malo amene ndimapondapo mapazi anga. Kuno ndiye kumene ndidzakhale pakati pa anthu anga Aisraele mpaka muyaya. Iwowo ngakhalenso mafumu ao, sadzaipitsanso dzina langa loyera pokhala osakhulupirika kapena poika mitembo ya mafumu ao ku zitunda zachipembedzo.
8
Ankamanga chiwundo chao pafupi ndi changa ndiponso mphuthu zao pafupi ndi zanga, nkungokhala khoma chabe pakati pa iwowo ndi Ine. Motero ankaipitsa dzina langa loyera ndi zonyansa zao zimene ankachita. Tsono ndidaŵaononga ndili wokwiya.
9
Tsopano aleke zonyansa zao, aleke kupembedza milungu ina, ndipo achotse mitembo ya mafumu ao, isakhalenso pafupi ndi Ine. Apo Ine ndidzakhala pakati pao mpaka muyaya.
10
“Iwe mwana wa munthu, uŵauze Aisraele za Nyumba ya Mulunguyi, maonekedwe ake ndi mamangidwe ake, kuti achite manyazi ndi machimo ao.
11
Akachita manyazi ndi zoipa zonse zimene adachita, uŵasimbire za Nyumba ya Mulungu ndi maonekedwe ake, za makomo ake otulukira ndi oloŵera, za kaonekedwe kake konse ndi za makonzedwe ake onse. Uŵafotokozere malamulo ndi malangizo ake, ndipo uŵalembe iwo akuwona, kuti aziŵakumbukira ndi kumaŵatsatadi.
12
Limeneli ndilo lamulo la Nyumba ya Mulungu imene idzamangidwa pamwamba pa phiri. Pozungulira pake ponse padzakhala poyera kwambiri. Limeneli ndilo lamulo la Nyumba ya Mulungu.
13
“Nayi miyeso ya guwa lansembe potsata miyeso yomwe ija imene adaayesera Nyumba ya Mulungu. Patsinde pake padzakhala ngalande ya masentimita makumi asanu kuzama kwake, ndiponso muufupi mwake. M'milomo mwake mwa ngalandeyo mudzakhala mwa mjintchi wa masentimita 25.
14
Guwalo msinkhu wake udzakhala wotere: kuchokera pa tsinde pansi mpaka pa phaka lapansi mita limodzi, muufupi mwake theka la mita. Kuchokera ku phaka laling'ono mpaka ku phaka lalikulu, msinkhu wake udzakhala mamita aŵiri, muufupi mwake mudzakhala masentimita makumi asanu.
15
Malo osonkhapo moto pa guwa msinkhu wake udzakhala mamita aŵiri. Pamwamba pake padzatuluka nyanga zinai, kutalika kwake theka la mita.
16
Malo osonkhapo motowo kutalika kwake kudzakhala mamita asanu ndi limodzi, muufupi mwakenso mamita asanu ndi limodzi, motero adzakhala olingana mbali zonse.
17
Phaka lapakati lidzakhala la mamita asanu ndi aŵiri kutalika kwake, ndiponso asanu ndi aŵiri muufupi mwake, pa mbali zake zonse zinai. Ndipo mkombero wake udzakhala wa masentimita 25 mjintchi wake. Ngalande ya patsinde pa guwalo idzakhala ya masentimita makumi asanu, ndipo makwerero a paguwapo adzayang'ana kuvuma.”
18
Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, ndikukuuza kuti guwa litamangidwa, malamulo ake popereka nsembe yopsereza ndiponso powaza magazi paguwapo, ndi aŵa:
19
Ansembe a fuko la Levi, am'banja la Zadoki, ndiwo azibwera pafupi nane kudzanditumikira. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Udzaŵapatse mwanawang'ombe wamphongo kuti aperekere nsembe yopepesera machimo.
20
Utaipha, udzatengeko magazi, ndi kuŵapaka pa nyanga zinai za guwa pa ngodya zinai za phaka, ndiponso kuzungulira mkombero. Motero udzaliyeretsa guwalo ndi kulidalitsa.
21
Kenaka udzatenge ng'ombe yamphongo imene yaperekedwa ngati nsembe yopepesera machimo. Udzaitenthe pa malo ake enieni, m'bwalo la Nyumba ya Mulungu, kunja kwa malo opatulika.
22
M'maŵa mwake udzapereke tonde wopanda chilema, kuti nayenso akhale nsembe yopepesera machimo. Ndi tondeyo udzayeretse guwalo monga momwe udachitira ndi ng'ombe yamphongo ija.
23
Utaliyeretsa kwathunthu guwalo, udzapereke ng'ombe yamphongo yopanda chilema ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema.
24
Udzazipereke pamaso pa Chauta, ndipo ansembe adzazithire mchere ndi kuzipereka kuti zikhale nsembe zopsereza kwa Chauta.
25
Tsiku lililonse pa masiku asanu ndi aŵiri uzidzapereka tonde, ng'ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo, kuperekera nsembe yopepesera machimo. Zonsezo zidzakhale zopanda chilema.
26
Masiku asanu ndi aŵiriwo adzachite mwambo wopepesera milandu ndi kuyeretsa guwa, kuti alipatulire Chauta.
27
Masiku amenewo atatha, kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu mpaka m'tsogolo mwake, ansembe azidzapereka pa guwalo nsembe zanu zopsereza ndiponso nsembe zanu zachiyanjano. Apo ndidzakulandirani. Ndatero Ine Ambuye Chauta.”
← Chapter 42
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 44 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48