bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 47
Ezekiel 47
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 46
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 48 →
1
Tsono munthu uja adabwerera nane ku chipata cha ku Nyumba ya Mulungu. Ndidaona kasupe akutuluka kunsi kwa chiwundo choloŵera ku Nyumba ya Mulungu chakuvuma, poti Nyumbayo inali yoyang'ana kuvuma. Kunkayenda madzi kunsi kwa chipupa chakumwera cha Nyumba ya Mulungu, chakumwera kwa guwa.
2
Adanditulutsira pa chipata chakumpoto, nazungulira nane panja pake mpaka ku chipata chakunja choyang'ana kuvuma. Ndipo ndidaona madzi akutuluka chakumwera kwa chipata.
3
Munthuyo adapita chakuvuma ali ndi choyesera m'manja mwake, nayesa mamita mazana asanu. Kenaka adandiwuza kuti ndiloŵe m'madzimo. Madziwo adandilekeza m'kakolo.
4
Adayesanso mamita mazana asanu, nandiloŵetsanso m'madzi muja, ndipo madziwo adandilekeza m'chiwuno.
5
Adayesanso mamita mazana asanu, ndipo madzi adasanduka mtsinje ndithu, ine osatha kuwoloka, poti madziwo adaakwera, anali ozama kwambiri olira kusambira poŵaoloka.
6
Apo adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, waziwonatu zimenezi ati?” Atatero adandibwezera ku gombe la mtsinjewo.
7
Titafika kugombeko, ndidaona mitengo yambiri pa mbali iliyonse ya gombelo.
8
Tsono munthuyo adandiwuza kuti, “Madzi ameneŵa akupita ku chigawo chakuvuma cha dziko kutsikira ku chigwa cha Araba. Potsiriza pake, akakathira m'Nyanja Yakufa imene madzi ake ali oipa, madziwo adzakoma.
9
Kumene mtsinjewo ukuyenda, cholengedwa chilichonse chidzakhala ndi moyo, nsombanso zidzachuluka. Pakuti madzi ameneŵa amapita kumeneko kuti akometse madzi anzake. Ndipo kulikonse kumene mtsinjewo ukuyenda, zonse zidzakhala ndi moyo.
10
Asodzi a nsomba adzakhala pa madooko ao, chifukwa kuyambira ku Engedi mpaka ku Enegilaimu kudzakhala malo abwino oponyako akombe. Mumtsinjewo mudzakhala nsomba zamitundumitundu, monga za m'Nyanja Yaikulu.
11
Koma mataŵale ake ndi maiŵe ake sadzakhala ndi madzi abwino, adzakhalabe amchere.
12
Pambali pa mtsinjewo, pa gombe lililonse, padzakhala mitengo yobereka zipatso za mtundu uliwonse. Masamba ake sadzafota, ndipo zipatso zake zidzakhala zosalekeza. Izidzabereka mwezi uliwonse, chifukwa madzi ake ndi ochokera ku Nyumba ya Mulungu. Zipatso zake anthu azidzadya, ndipo masamba ake azidzachita mankhwala.”
13
Zimene Ambuye Chauta akunena ndi izi, akuti, “Naŵa malire amene mudzatsate poŵagaŵira dziko la Israele mafuko khumi ndi aŵiri aja: Yosefe alandire zigawo ziŵiri.
14
Dzikoli mudzagaŵana mofanana, chifukwa ndidalumbira kuti ndidzalipereka kwa makolo anu ndipo lidzakhala lanulanu. Motero lidzapatsidwa kwa inu mwamaere, kuti likhale choloŵa chanu.
15
Malire ake adzayende motere: chakumpoto kwake achokere ku Nyanja Yaikulu, kutsata mseu wa ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamati, kupitirira ku Zedati,
16
Berata ndi Sibraimu, mizinda imene ili pakati pa malire a Damasiko ndi Hamati, mpaka ku Hazere-Hatikoni pafupi ndi malire a Haurani.
17
Motero malire akumpoto adzachokera ku nyanja mpaka ku mzinda wa Hazarenoni umene wachitana malire ndi Damasiko chakumpoto, ndiponso mpaka m'malire a Hamati chakumpoto. Imeneyi ndiyo idzakhala mbali yakumpoto.”
18
“Malire akuvuma ayende chakumwera kuchokera ku Hazarenoni pakati pa Haurani ndi Damasiko, kutsata mtsinje wa Yordani pakati pa Giliyadi ndi dziko la Israele, kuloza ku nyanja yakuvuma mpaka ku Tamara. Imeneyi idzakhala mbali yakuvuma.”
19
“Malire akumwera ayende kuchokera ku Tamara mpaka ku dziŵe la Meriboti-Kadesi. Kuchokera kumeneko atsate malire a ku Ejipito mpaka ku Nyanja Yaikulu. Imeneyi ndiyo mbali yakumwera.”
20
“Malire akuzambwe akhale Nyanja Yaikulu mpaka ku malo oyang'anana ndi chipata cha Hamati. Imeneyi ndiyo mbali yakuzambwe.”
21
“Motero mugaŵane dziko limeneli pakati panu potsata mafuko a Israele.
22
Muligaŵe kuti likhale choloŵa chanu. Likhalenso la alendo amene amakhala pakati panu, nabereka ana pakati panu. Alendowo adzakhala nanu ngati mbadwa za mu Israele. Adzapatsidwa choloŵa chao pamodzi ndi inuyo.
23
Mlendo aliyense umpatse choloŵa chake ku fuko limene akukhalakolo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
← Chapter 46
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 48 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48