bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezekiel 6
Ezekiel 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 7 →
1
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, uyang'ane ku mapiri a ku Israele, ndipo uŵadzudzule ndi mau aŵa akuti,
3
Inu mapiri a ku Israele, imvani mau a Ambuye Chauta. Akuuza mapiri ndi magomo, mitsinje ndi zigwa kuti, ‘Ine weniweniyo ndidzakuthirani nkhondo, ndipo ndidzaononga akachisi anu opembedzerako mafano.
4
Maguwa anu ansembe adzaonongedwa, ndipo maguwa anu ofukizirapo lubani adzaphwanyidwa. Anthu anu odzapembedza pamenepo ndidzaŵaphera pafupi ndi mafano anu.
5
Tsono mitembo ya Aisraele ndidzaimwaza patsogolo pa mafano ao. Ndidzamwaza mafupa anu pozungulira maguwa anu onse.
6
Konse kumene mukakhale, mizinda yanu idzasanduka mabwinja. Akachisi onse adzaonongedwa, kotero kuti maguwa anu onse pamodzi ndi mafano anu omwe adzaphwanyidwa. Maguwa anu ofukizirapo lubani adzagwetsedwa, ndipo zonse zimene mudapanga zidzatheratu.
7
Anthu anu adzaphedwa pakati panu, motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.’ ”
8
“Komabe ena mwa inu ndidzaŵasiya amoyo. Adzapulumuka ku nkhondo, ndipo ndidzaŵamwazira ku maiko ena, pakati pa anthu a mitundu ina.
9
Tsono opulumuka mwa inu adzandikumbuka pakati pa anthu a mitundu inayo, kumene adatengedwa ukapolo. Ndidzaŵamvetsa chisoni ndi manyazi chifukwa cha kusakhulupirika kuja ndi kundipandukira kuja, ndiponso chifukwa cha kuika mtima kwao pa mafano. Tsono adzachita nyansi ndi iwo eniakewo poona zoipa zonse zimene adachita, pamodzi ndi zochita zao zonyansa.
10
Pamenepo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndipo sindinkaŵaopseza chabe pamene ndinkanena kuti ndidzaŵalanga.”
11
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Omba m'manja mwako, ndipo uponde phazi lako pansi kwamphamvu. Tsono unene kuti, ‘Tsokalo!’ chifukwa cha zonyansa zonse zimene banja la Israele lachita. Adzafa ndi nkhondo, njala ndi mliri.
12
Amene ali kutali adzafa ndi mliri. Amene ali pafupi adzafa ndi nkhondo. Aliyense wotsala adzafa ndi njala. Ndimo m'mene mkwiyo wanga udzagwere pa iwo.
13
Apo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, pamene mudzaona ophedwa ao ali vuu pakati pa mafano, kuzungulira maguwa ao, pamwamba pa magomo ndi mapiri onse, pansi pa mtengo uliwonse wogudira, ndi wa thundu uliwonse wa masamba ambiri, ku malo onse kumene ankapereka nsembe zonunkhira kwa mafano ao onse.
14
Motero ndidzaŵakantha ndi mkono wanga, ndipo dziko lao lonse ndidzalisandutsa chipululu ku malo ao onse kumene akukhala. Ndidzalisandutsa bwinja kuchokera ku chipululu mpaka ku mzinda wa Ribula. Pamenepo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48