bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 1
Jeremiah 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 2 →
1
Aŵa ndi mau a Yeremiya, mwana wa Hilikiya, mmodzi mwa ansembe a ku Anatoti, m'dziko la Benjamini.
2
Chauta adalankhula naye pa nthaŵi ya Yosiya, mfumu ya ku Yuda, mwana wa Amoni, pa chaka cha khumi ndi chitatu cha ufumu wake.
3
Chauta adalankhula nayenso pa nthaŵi ya Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, mpaka mwezi wachisanu wa chaka cha khumi ndi chimodzi cha Zedekiya, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, pamene anthu a ku Yerusalemu adatengedwa ukapolo.
4
Chauta adandiwuza kuti,
5
“Ndisanakulenge m'mimba mwa mai wako, ndinali nditakudziŵa kale. Usanabadwe nkomwe, ndinali ntakupatula kale, ndidakuika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.”
6
Ine ndidati, “Ha, Ambuye Chauta! Ine ndine mwana, kulankhula sindidziŵa.”
7
Koma Iye adandiyankha kuti, “Usati, ‘Ndine mwana.’ Udzapita ndithu kwa anthu onse kumene ndidzakutuma, ndipo chilichonse chimene ndidzakulamula udzachilankhula.
8
Usaŵaope, Ine ndili nawe, ndidzakupulumutsa,” akuterotu Chauta.
9
Tsono Chauta adatambalitsa dzanja lake nakhudza pakamwa panga. Ndipo adandiwuza kuti, “Tamvera, ndikuika mau anga m'kamwa mwako.
10
Ndikukuika lero kuti ukhale ndi ulamuliro pa maiko a anthu ndi maufumu ao, kuti uzule ndi kugwetsa, kuti uwononge ndi kugumula, kuti umange ndi kubzala.”
11
Chauta adandifunsa kuti, “Yeremiya, kodi ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona nthambi ya mtowo.”
12
Chauta adati, “Waona bwino. Ineyo ndikuwonetsetsa kuti zichitikedi zimene ndidanena.”
13
Chauta adandifunsa kachiŵiri kuti, “Kodi ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona mbiya yogaduka, yafulatira kumpoto.”
14
Apo Iye adandiwuza kuti, “Ndiye kuti tsoka la anthu a m'dziko lino lidzachokera kumpoto.
15
Ndikuitana anthu a mafuko onse a maufumu akumpoto,” akuterotu Chauta. “Mafumu ao adzabwera, aliyense adzaika mpando wake waufumu pa zipata za Yerusalemu, ndiponso pozungulira malinga ake. Iwo adzazinganso mizinda yonse ya Yuda.
16
Ndidzatulutsa mlandu wanga wotsutsa anthu anga, chifukwa cha zoipa zimene adachita pakundisiya Ine. Adafukiza lubani kwa milungu ina, namapembedza zimene adapanga ndi manja ao.
17
Koma iwe Yeremiya, ukonzeke. Nyamuka, ukaŵauze zonse zimene ndikukulamula. Iwowo asakuwopse, kuwopa kuti Ineyo ndingakuwopse iwo akuwona.
18
Lero ine ndikukulimbitsa ngati mzinda wamalinga, mzati wachitsulo, ndiponso ngati makoma amkuŵa, kuti usachite mantha ndi wina aliyense m'dziko lonse, kaya ndi mafumu a ku Yuda, nduna zakumeneko, ansembe kapena anthu wamba.
19
Iwo adzalimbana nawe, koma sadzakupambana, pakuti ine ndili nawe ndipo ndidzakupulumutsa,” akuterotu Chauta.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52